1 Sam. 29 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Afilisti akana Davide.

1Afilisti adasonkhanitsa magulu ao ankhondo ku Afeki. Nawonso Aisraele adamanga zithando zankhondo pa chitsime cha ku Yezireele.

2Pamene atsogoleri ankhondo a Afilisti ankatsogoza magulu ao a ankhondo mazana angapo ndiponso zikwi zingapo, Davide ndi ankhondo ake ankayenda pambuyo ndi Akisi.

3Pamenepo atsogoleri aja a Afilisti adafunsa kuti, “Kodi Ahebriŵa akuchita chiyani kuno?” Akisi adayankha kuti, “Uyutu ndi Davide, mtumiki wa Saulo mfumu ya Aisraele. Iye wakhala nane tsopano masiku ambiri kapena nditi zaka, chibwerere chake kuno sindidampeze cholakwa chilichonse mpaka lero lino.”

4Koma iwo adamkalipira Akisiyo namuuza kuti, “Mumbweze munthuyo kuti abwerere ku malo amene mudampatsa. Sadzapita nafe ku nkhondo, kuwopa kuti kunkhondoko angakasanduke mdani wathu. Nanga munthu ameneyu angathe kudziyanjanitsa bwanji ndi mbuyake? Iyeyu angathe kuchita zimenezi pakupha anthu athu ali panoŵa.

51Sam. 18.7; 21.11Ameneyutu ndi Davide, yemwe uja ankamuvinira ndi kumuimbira kuti,

“ ‘Saulo wapha zikwi inde,

koma Davide wapha zikwi khumikhumi?’ ”

6Apo Akisi adaitana Davide namuuza kuti, “Pali Chauta wamoyo, iwe wakhala wokhulupirika kwa ine, ndipo kutumikira kwako m'magulu anga ankhondo kwandikomera kwambiri. Sindidakupeze cholakwa kuyambira tsiku limene udabwera kuno mpaka lero lino. Komabe atsogoleri enaŵa sakukufuna.

7Choncho ubwerere tsopano. Upite mwamtendere, kuwopa kuti atsogoleri a Afilisti angaipidwe nawe.”

8Davide adamufunsa kuti, “Kodi ndachita chiyani? Kodi mwapeza chiyani pa ine mtumiki wanu, kuyambira nthaŵi imene ndidayamba kukugwirirani ntchito mpaka tsopano lino? Nanga ndilekerenji kukamenyana nkhondo ndi adani anu, mbuyanga mfumu?”

9Akisi adayankha kuti, “Ndikudziŵa kuti ndiwe wosalakwa ndithu, monga mngelo wa Mulungu. Komabe atsogoleri ankhondo a Afilisti akunena kuti, ‘Davide asapite nafe ku nkhondo.’

10Tsono udzuke m'mamaŵa, pamodzi ndi anthu ako amene udabwera nawo, munyamuke kukangocha.”

11Choncho Davide ndi anthu omwe anali naye adanyamuka m'mamaŵa nabwerera ku dziko la Afilisti. Koma Afilisti adakafika mpaka ku Yezireele.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help