1 2Maf. 15.7; 2Mbi. 26.23 Chaka chimene mfumu Uziya adamwalira, ndidaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu wautali ndi wokwezedwa. Mkanjo wao unali wautali kwambiri, kotero kuti udadzaza Nyumba yao yonse.
2Pamwamba pao padaaimirira Aserafi. Aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi: aŵiri ophimbira kumaso, aŵiri ophimbira mapazi, aŵiri oulukira.
3 Chiv. 4.8 Aserafiwo ankafuulirana kuti,
“Ngwoyera, ngwoyera, ngwoyera Chauta Wamphamvuzonse,
ulemerero wake wadzaza dziko lonse lapansi.”
4 Chiv. 15.8 Chifukwa cha kufuulako maziko a zitseko ndi ziwundo adagwedezeka ndipo m'Nyumba ya Chautamo mudangoti utsi pha.
5Apo ine ndidati: “Tsoka langa ine! Ndatayika. Pakuti ndine munthu wa pakamwa poipa, ndipo ndimakhala pakati pa anthu a pakamwa poipa. Komabe maso anga aona Mfumu, Chauta Wamphamvuzonse.”
6Pomwepo mmodzi mwa Aserafi aja adaulukira kwa ine, ali ndi khala lamoto m'manja mwake. Khalalo adaalichotsa pa guwa la nsembe ndi mbaniro.
7Ndipo adandikhudza pakamwa ndi khala lamotolo nati, “Taona, ndakukhudza milomo ndi khalali. Kulakwa kwako kwachotsedwa, machimo ako akhululukidwa.”
8Kenaka ndidamva mau a Ambuye akuti,
“Kodi ndidzatuma yani, ndani adzatipitire?”
Apo ndidati “Ndilipo ineyo, tumeni.”
9 Mt. 13.14, 15; Mk. 4.12; Lk. 8.10; Yoh. 12.40; Ntc. 28.26, 27 Ndipo Ambuyewo adati,
“Pita, kaŵauze anthu ameneŵa kuti,
‘Kumva muzimva, koma osamvetsa.
Kupenya muzipenya, koma osazindikira.’
10Tsono anthu ameneŵa uŵaphe mtima,
uŵagonthetse makutu,
ndipo uŵatseke m'maso,
kuti angaone ndi maso ao,
angamve ndi makutu ao,
angamvetse ndi mitima yao,
kenaka nkutembenuka mtima ndi kuchiritsidwa.”
11Pamenepo ndidafunsa kuti,
“Zimenezo ndi mpaka liti, Inu Ambuye?”
Iwo adati:
“Mpaka mizinda itasanduka mabwinja,
mpaka nyumba zitasoŵa anthu okhalamo,
mpaka dziko litasanduka chipululu ndithu.
12Ine anthuŵa ndidzaŵasamutsira kutali,
ndipo dziko lidzakhala thengo.
13Tsono ngakhale chigawo chachikhumi cha anthu
chitsaleko m'dzikomo,
nachonso chidzayatsidwa moto.
Koma monga mitengo ya muŵanga ndi ya thundu
imasiya chitsa akaidula,
chonchonso mbeu yoyera ija idzatsalira
ngati chitsa chotsala m'dziko.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.