1Mlesi ali ngati mwala wonyansa,
aliyense amamseka chifukwa cha kuipa kwake.
2Mlesi ali ngati ndoŵe yonyansa,
amene waitola, amasamba m'manja.
Za ana oleredwa moipa3Kukhala bambo wa mwana wamwamuna wopanda mwambo,
ndi chinthu chochititsa manyazi,
ndipo kubadwa kwa mwana wamkazi ndi tsoka.
4Mtsikana wanzeru amapeza banja,
koma mtsikana wopanda manyazi amavutitsa bambo wake.
5Mkazi wachipongwe amachititsa manyazi bambo wake
ndi mwamuna wake.
Ndipo onsewo amamnyoza.
6Kulangiza pa nthaŵi yosayenera
kuli ngati nyimbo pa maliro,
koma kulanga kapena kukwapula
nkofunika nthaŵi zonse.
Za nzeru ndi uchitsiru7Kuphunzitsa chitsiru kuli ngati kumata mbiya
yophwanyika ndi phula,
kulinso ngati kudzutsa munthu amene wagona tulo tofa nato.
8Kulankhula ndi chitsiru kuli ngati kulankhula
ndi munthu woodzera.
Ukangotsiriza kulankhula chimafunsa kuti, “Mukuti chiyani?”
9Ana oleredwa ndi mwambo aiŵalitsa anthu
kuti makolo anali anthu osauka.
10Koma ana osokonezeka, onyada ndi opanda mwambo
amapeputsa ulemu wa makolo ao.
11Munthu wakufa umulire,
chifukwa wasiya kuŵala kwa dzuŵa.
Chitsiru uchilire,
chifukwa chasiya nzeru zake.
Munthu wakufayo usamulire kwambiri
pakuti wapeza chiwuso.
Koma chitsiru moyo wake umaipiratu kupambana imfa.
12 Gen. 50.10; Yud. 16.24 Maliro olira anthu akufa amakhala a masiku asanu ndi aŵiri.
Maliro olira anthu opusa ndi osasamala za Mulungu,
amakhala a masiku onse a moyo wao.
13Usamalankhule kwambiri ndi chitsiru,
kapena kukacheza kwa munthu wopusa.
Chenjera naye kuti ungagwe m'mavuto
ndipo kuti angakudetse pokhudzana naye.
Ngati ufuna mtendere umlewe,
ndipo uchitsiru wake sudzakutopetsa.
14Kodi pali chinthu cholemera kuposa mtovu?
Inde chilipo, dzina lake nchitsiru.
15Mchenga, mchere, ndi kamphumphu ka chitsulo
nkwapafupi kuzisenza kupambana kupirira munthu wopusa.
16Mtanda wa nyumba womangidwa bwino sugwedezeka ndi chivomezi.
Chimodzimodzi mtima woganiza mwanzeru sugwedezeka pa mavuto.
17Mtima woganiza mwanzeru
uli ngati makaka a utoto pa khoma losalala.
18Monga momwe mpanda wa pa phiri sungathe kulimba
ndi mphepo,
chonchonso mtima wa chitsiru wonjenjemera ndi
maganizo ake omwe sungalimbike konse ukapeza choopsa.
Za chibwenzi19Ukathopsola mnzako m'maso,
amadza misozi.
Ukabaya mnzako mu mtima,
amatulutsa zakukhosi.
20Ukaponya mwala kuti ulase mbalame,
zonse zimathaŵa.
Ukanyoza bwenzi lako,
chibwenzi chanu chidzatha.
21Ukasololera lupanga bwenzi lako,
usataye mtima, pali mwai woti nkuyanjananso.
22Ngati wayambana ndi bwenzi lako,
usavutike, mungathe kuyanjananso.
Koma kunyoza, chipongwe, kuulula zachinsinsi,
ndi kumjeda,
zonsezi zimathetsa chibwenzi chilichonse.
23Mnzako azikukhulupirira pamene ali mmphaŵi.
Akadzapeza bwino, udzasangalala naye.
Umthandize pa mavuto,
mwina nkudzalandirako kanthu iye atapeza chuma.
24Moto usanayake m'ng'anjo,
mumayamba mwatuluka nthunzi ndi utsi,
chimodzimodzi kumenyana kusanayambe,
kumayamba nkunyozana.
25Sindidzachita manyazi kutchinjiriza bwenzi langa,
sindidzamfulatira konse.
26Koma ngati choipa chindigwera chifukwa cha iye,
aliyense amene adzazimve, adzayamba kuchenjera naye.
Za kukhala maso27Ndani adzandithandiza kulonda pakamwa panga,
ndani adzandithandiza kusokerera kwamphamvu milomo yanga,
kuti ndisati ndilakwe,
ndisaonongeke ndi zokamba zanga?
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.