1Inu Chauta, kumbukirani zimene zatigwera.
Muyang'ane, muwone m'mene anthu akutinyozera.
2Choloŵa chathu chaperekedwa kwa alendo,
nyumba zathu zili m'manja mwa anthu akudza.
3Ife tili ngati ana amasiye, opanda bambo wao.
Amai athu ali ngati akazi amasiye.
4Madzi amene timamwaŵa tiyenera kuchita chogula.
Nkhuni zosonkhera moto nzoyeneranso kuchita chogula.
5Amatikankha mwankhanza,
goli lili m'khosi mwathu.
Ngakhale titope, satilola kupumula.
6Tidachita chibwenzi ndi Aejipito ndiponso ndi Aasiriya,
kuti mwina iwo nkutipatsako chakudya.
7Makolo athu adachimwa, ndipo adatha.
Ndiye ife tatengana nacho chilango
chifukwa cha machimo ao.
8Amene akutilamulira ndi akapolo,
palibe ndi mmodzi yemwe wotipulumutsa m'manja mwao.
9Pofunafuna chakudya, timagwa m'zoopsa
chifukwa cha anthu opha anzao ku chipululu.
10Khungu lathu likutentha ngati lili m'ng'anjo
chifukwa cha ululu wa njala.
11Ku Ziyoni akazi akuŵachita zadama mwakhakhamizo.
M'mizinda ina ya ku Yuda
anamwali akuŵachita chimodzimodzi.
12Akalonga akuŵapachika pomangirira manja ao,
akuluakulu sakuŵalemekeza konse.
13Achinyamata akuŵakakamiza kupera tirigu,
anyamata akudzandira nayo mitolo ya nkhuni.
14Akuluakulu adachokapo pa bwalo la mzinda,
achinyamata nyimbo zao zija zati zi!
15Chimwemwe chachoka m'mitima mwathu.
Kuvina kwathu kwasanduka kulira.
16Chisoti chathu chaufumu chachoka kumutu,
kugwa pansi.
Tsoka kwa ife, chifukwa tachimwa.
17Nchifukwa chake mitima yathu yalefuka,
chifukwa cha zimenezi m'masomu mwachita chidima.
18Phiri la Ziyoni lasanduka bwinja,
nkhandwe zikungoyendayendapo.
19Koma Inu Chauta, ndinu mfumu mpaka muyaya,
mpando wanu waufumu udzakhalapo pa mibadwo yonse.
20Chifukwa chiyani mwakhala mukutiiŵala nthaŵi yonse?
Chifukwa chiyani mwatisiya nthaŵi yaitali chotere?
21Inu Chauta mutitembenuzire kwa Inu,
kuti tibwerere mwakale.
Mutipatsenso masiku onga amakedzana aja.
22Kaya, monga nkuti mwatitayiratu?
Monga nkuti mwatikwiyira kopitirira?
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.