1 Chiv. 5.5; 22.16 Nthambi idzaphuka patsinde pa Yese,
ndipo mphukira idzatuluka ku mizu yake.
2Mzimu wa Chauta udzakhala pa Iye,
mzimu wopatsa nzeru ndi kumvetsa,
mzimu wopatsa uphungu ndi mphamvu,
mzimu wopatsa kudziŵa zinthu ndi kuwopa Chauta.
3Ndipo kuwopa Chauta
ndiye chidzakhale chinthu chomkondweretsa.
Sadzaweruza potsata zooneka pamaso,
kapena kugamula mlandu potsata zakumva.
4 2Ate. 2.8 Koma amphaŵi adzaŵaweruza mwachilungamo,
ndipo anthu otsika a pa dziko lapansi
adzaŵagamulira mlandu wao mosakondera.
Mau ochokera m'kamwa mwake
adzakhala ngati ndodo yokanthira ochimwa,
atalamula iyeyo anthu oipa adzaphedwa.
5 Aef. 6.14 Chilungamo chidzakhala ngati lamba wake,
ndipo kukhulupirika, ngati chomangira m'chiwuno mwake.
6 Yes. 65.25 Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa,
kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwanawambuzi,
mwanawang'ombe ndi mwanawamkango adzadyera limodzi,
mwana wamng'ono nkumaziŵeta zonsezo.
7Ng'ombe yaikazi ndi chimbalangondo
zidzadya pamodzi,
ndipo ana ao adzagona pamodzi.
Mkango udzadya udzu ngati ng'ombe.
8Mwana woyamwa adzaseŵera pa dzenje la mamba,
ndipo mwana woleka kuyamwa adzapisa
dzanja lake ku funkha la mphiri, osalumidwa.
9 Hab. 2.14 Sipadzakhala chilichonse chopweteka
kapena choononga pa phiri lopatulika la Mulungu.
Ndipo anthu a pa dziko lonse lapansi
adzakhala odzaza ndi nzeru ya kudziŵa Chauta,
monga nyanja imadzazira ndi madzi.
Otengedwa ku ukapolo adzabwerako.10 Aro. 15.12 Tsiku limenelo mfumu yatsopano yochokera ku banja la Davide idzakhala chizindikiro kwa anthu a mitundu yonse. Onse adzasonkhana kwa iye, ndipo malo ake okhalapo adzakhala aulemerero.
11Tsiku limenelo Ambuye adzatambalitsa dzanja lake kachiŵiri kuti aombole anthu ake otsalira ku Asiriya, ku Ejipito, ku Patirosi, ku Etiopiya, ku Elamu, ku Sinara, ku Hamati ndi pa zilumba za m'nyanja yamchere.
12Adzakwezera mitundu ya anthu mbendera,
adzasonkhanitsa otayika a ku Israele
ndi obalalika a ku Yuda kuchokera ku
mbali zonse zinai za dziko lapansi.
13Nsanje ya Efuremu idzatha,
ndipo osautsa Yuda adzaonongeka.
Efuremu sadzadukidwa ndi Yuda,
ndipo Yuda sadzavuta Efuremu.
14Koma Yuda ndi Efuremu adzathira
nkhondo pa Afilisti kuzambwe,
ndipo onsewo pamodzi adzalanda
zinthu za anthu akuvuma.
Adzalimbana ndi Aedomu ndi Amowabu,
ndipo Aamoni adzaŵagonjera.
15 Chiv. 16.12 Ndipo Chauta adzaphwetsa kotheratu
mwendo wa nyanja yofiira ya ku Ejipito.
Adzatambalitsa dzanja lake
ndipo adzaombetsa mphepo yotentha
pa mtsinje wa Yufurate.
Mtsinjewo udzagaŵikana m'timitsinje
tisanu ndi tiŵiri,
kuti anthu aoloke pouma.
16Padzakhala mseu waukulu woti
ayendepo otsalira ku Asiriya aja,
monga m'mene panaliri mseu waukulu
woyendapo Aisraele pochoka ku Ejipito.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.