Mas. 55 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lopempha chithandizoKwa Woimbitsa Nyimbo. Ndakatulo ya Davide, yoimbira zipangizo zazingwe.

1Inu Mulungu, tcherani khutu kuti mumve pemphero langa,

musabisale pamene ndikukupembani.

2Mundimvere, ndipo mundiyankhe.

Mtima wanga suli m'malo chifukwa cha mavuto anga.

3Ndikuda nkhaŵa chifukwa adani anga akundifuulira,

anthu oipa akundipsinja.

Akundivutitsa kwambiri,

akundikwiyira kosalekeza.

4Mtima wanga ukumva ululu woopsa,

zoopsa za imfa zandigwera.

5Mantha andifikira, ndipo ndikunjenjemera,

mantha aakulu andigwira.

6Ndipo ndimati,

“Ndikadakhala ndi mapiko onga a njiŵa,

bwenzi nditauluka kupita kutali kukapuma.

7Inde, ndikadathaŵira kutali

ndi kukakhala ku chipululu.

8“Ndikadafulumira

kupeza pobisalira mphepo yaukali yamkunthoyi.”

9Inu Ambuye, onongani zolinga za adani anga,

musokoneze upo wao.

Pakuti ndikuwona anthu

akuchita chiwawa ndi nkhondo mumzindamo.

10Usana ndi usiku iwo akuuzungulira pa makoma ake,

mumzindamo muli chiwawa ndi nkhondo.

11M'menemo muli chiwonongeko chokhachokha.

M'misika yake muli zopanikizana ndi zonyenga.

12Akadakhala mdani wanga wondinyozayo,

ndikadatha kupirira.

Akadakhala mdani wanga wondichita chipongweyo,

ndikadangobisala basi.

13Koma iweyo mnzanga, mnzanga woyenda naye,

bwenzi langa wozoloŵerana naye,

ndi amene ukuchita zimenezi.

14Tinkakambirana nkhani zokoma tili aŵiri,

tinkapembedza limodzi m'Nyumba ya Mulungu.

15Inu Mulungu, mulole

kuti imfa iŵagwere adani anga,

atsikire ku manda akadali moyo,

pakuti zoipa zili tho m'mitima ndi m'nyumba zao.

16Koma ine ndikupempha Chauta,

ndipo Iye adzandithandiza.

17Madzulo, m'maŵa ndi masana

ndikudandaula ndi kulira,

ndipo Iye adzamva mau anga.

18Adzapulumutsa moyo wanga pa nkhondo

imene ndikumenya,

pakuti anthu ambiri akukangana nane.

19Mulungu, amene akukhala pa mpando waufumu

kuyambira kalekale,

adzandimenyera nkhondo,

adzaŵatsitsa adani anga

chifukwa safuna kusintha khalidwe lao loipa,

ndipo saopa Iye.

20Mnzanga adatambasula dzanja lake

kuti amenye abwenzi ake,

adaphwanya chipangano chake.

21Mau ake anali osalala kupambana batala,

komabe mumtima mwake munali zankhondo.

Mau ake anali ofeŵa kupambana mafuta,

komabe anali ndi malupanga osololasolola.

22Tula kwa Chauta nkhaŵa zako,

ndipo Iye adzakuchirikiza.

Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.

23Koma Inu Mulungu mudzaŵaponya adani anga

m'dzenje lozama lachiwonongeko.

Anthu okhetsa magazi ndi onyenga

sadzafika ngakhale theka la masiku ao.

Koma ine ndidzadalira Inu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help