Lun. 19 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ku Nyanja Yofiira

1Koma anthu osamvera Mulungu adavutika nawo

mpaka kutha kwake ukali wanu wopanda chisoni.

Chifukwa Mulungu adaadziŵiratu zochita zao zakutsogolo.

2Adaadziŵa kuti ngakhale iwowo

adaaloleza anthu anu kupita,

naŵafulumizitsa kunyamuka,

pambuyo pake adzasintha maganizo nadzaŵalondola.

3Ndipo ndithudi ngakhale ankatanganidwabe ndi maliro ao,

ndi kulira ku manda a anthu ao akufa,

adavomera maganizo ena amsala.

Adalondola ngati anthu othaŵa

anthu aja amene iwo omwe adaapempha kuti achoke.

4Tsoka loŵayenera lidaŵaganizitsa cholinga chimenechi

ndi kuŵaiŵalitsa zoipa zimene zidaaŵagwera,

kuti choncho chikwanire kwenikweni chilango

chimene chinali chitapereŵera pa mazunzo ao.

5Pamenepo mudafunanso kuti

anthu anu apitirire ulendo wao wodabwitsa,

adaniwo apeze imfa yozizwitsa.

6Kakhalidwe ka zolengedwa zonse

kadasanduka katsopano potsata lamulo lanu,

kuti ana anu asapeze choŵaŵa chilichonse.

7Padaoneka mtambo wophimba zithando zao,

pamene panali madzi okhaokha padatuluka mtunda wouma.

Padapezeka njira yosavuta pakati pa Nyanja Yofiira,

ndiponso chigwa cha msipu pamalo pa mafunde aukali.

8Tsono amene dzanja lanu linkaŵateteza aja,

onse ngati fuko limodzi,

adadzera pamenepo ali kuyang'anitsitsa zozizwitsa zanu.

9Ankayenda mokondwa ngati akavalo pa busa lao,

ankalumphalumpha ngati anaankhosa,

nkumakutamandani Inu Ambuye mpulumutsi wao.

10Ankakumbukira zamakedzana

zimene zidaaŵaonekera ku dziko laukapolo,

kuti pamalo pa zifuyo, dziko lidaabereka udzudzu,

pamalo pa nsomba, mtsinje udaatulutsa achule ochuluka.

11Pambuyo pake adaonanso mbalame

za mtundu watsopano,

pamene nkhuli yao idaŵakankha

kupempha chakudya chokoma kwambiri.

12Pamenepo zinziri zidatuluka ku nyanja,

kuti azidye nkukhuta.

Chilango cha Aejipito

13Koma chilango chidaŵagwera anthu ochimwa,

ataŵachenjeza ndi zing'aning'ani.

Adalangidwa moyenerana ndi kuipa kwao,

chifukwa adaonetsa alendo chidani choopsa.

14Paja anthu ena ankakana kulandira alendo

akangofika kwa iwo,

koma iwowo adasandutsa akapolo

alendo amene ankaŵachitira zabwino.

15Si pokhapo ai,

koma oyambawo chilango chamtundu chidzaŵagwera

chifukwa cholandira alendo moipa.

16Koma anthu enaŵa

amene poyamba adalandira anthu anu ndi chimwemwe,

nagaŵana nawo zabwino zao,

pambuyo pake adaŵasautsa ndi ntchito zoŵaŵa.

17Ochimwawo adaŵalanganso pakuŵapatsa khungu,

monga oyamba aja,

amene ankazinga pakhomo pa wolungama.

Pamene paja mdima wandiweyani utaŵaphimba,

aliyense ankafunafuna njira ya kukhomo kwake.

Mau otsiriza

18Zolengedwa zidasinthana kakhalidwe,

monga poliza limba,

chingwe chilichonse chili ndi liwu lakelake,

koma kaimbidwe nkosiyana.

Zimenezi zimaoneka bwino

poyang'ana zimene zidaachitika.

19Nyama zapamtunda zidaasanduka zam'madzi,

zosambira m'madzi zidaatulukira ku mtunda.

20Moto udaasunga mphamvu yake ndi m'madzi momwe,

ndipo madzi adaaiŵala mphamvu zake zozimitsa moto.

21Mwina malaŵi a moto sadapsereze

minofu ya tizilombo todutsa pakati pake,

sadasungunule chakudya chofeŵa chakumwamba

chosakhalira kusungunuka chija.

22Inu Ambuye,

mudakuza ndi kuupatsa ulemerero

mtundu wa anthu anu pa zonse.

Simudaleke kuuthandiza nthaŵi zonse

ndi pamalo ponse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help