1 1Sam. 20.15-17 Tsiku lina Davide adafunsa kuti, “Kodi alipo wina aliyense wa banja la Saulo amene adatsalako? Ndikufuna kuti ndimchitire chifundo chifukwa cha Yonatani.”
2Panali mtumiki wina wa banja la Saulo, dzina lake Ziba. Ameneyo adamuitana kuti apite kwa Davide. Tsono mfumu idamufunsa kuti, “Kodi iwe ndiwe Ziba?” Iye adayankha kuti, “Ndine amene, mtumiki wanu.”
32Sam. 4.4 Apo mfumu idamufunsa kuti, “Kodi palibe wina aliyense wa pa banja la Saulo amene adatsalako? Ndikufuna kuti ndimchitire chifundo monga momwe ndidalonjezera kwa Mulungu?” Ziba adayankha kuti, “Padakali mwana wamwamuna wa Yonatani. Iyeyo ngwopunduka miyendo.”
4Mfumu idamufunsa kuti, “Ali kuti?” Ziba adayankha kuti, “Ali ku nyumba ya Makiri, mwana wa Amiyele, ku Lodebara.”
5Pamenepo mfumu Davide adatuma anthu kuti akamtenge, ndipo iwo adakamtengadi ku nyumba ya Makiri mwana wa Amiyele, ku Lodebara.
6Pamene Mefiboseti, mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, adafika kwa Davide, adaŵerama pamaso pake, napereka ulemu. Tsono Davide adati, “Mefiboseti!” Iyeyo adayankha kuti, “Ndabwera ine mtumiki wanu.”
7Davide adamuuza kuti, “Usaope. Ndifuna kukuchitira chifundo chifukwa cha Yonatani bambo wako, ndipo ndidzakubwezera dera lonse la Saulo mbuyako. Udzadya nane pamodzi masiku onse.”
8Iyeyo adamuŵeramira, nati, “Kodi ine mtumiki wanu ndine yani, kuti musamale galu wakufa ngati ine?”
9Tsono mfumu idaitana Ziba mtumiki wa Saulo, nimuuza kuti, “Zinthu zonse zimene zidaali za Saulo ndi zonse za pa banja pake ndazipereka kwa mwana wa mbuyako Saulo.
10Tsono iwe, ana ako ndi atumiki ako, muzidzamlimira iyeyo, ndi kumabwera ndi zinthu zokolola zakumunda, kuti banja la mbuyako likhale ndi chakudya. Koma Mefiboseti adzadya ndi ine masiku onse.” Ziba anali ndi ana aamuna 15 ndi atumiki 20.
11Tsono adauza mfumu kuti, “Mtumiki wanune ndidzachita zonse potsata zimene inu mbuyanga mfumu mwalamula.” Choncho Mefiboseti ankadya ndi Davide ngati mmodzi mwa ana a mfumu.
12Mefiboseti anali ndi mwana wamng'ono, dzina lake Mika. Ndipo anthu onse amene ankakhala m'nyumba ya Ziba, adasanduka atumiki a Mefiboseti.
13Choncho Mefibosetiyo adakhala ku Yerusalemu, poti iyeyo ankadya ku nyumba ya mfumu masiku onse. Koma tsono anali wolumala mapazi onse aŵiri.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.