1Pamene iwo ankayandikira ku Yerusalemu, nkufika ku Betefage, ku Phiri la Olivi, Yesu adatuma ophunzira aŵiri,
2naŵauza kuti, “Pitani m'mudzi mukuwonawo. Mukakangoloŵamo, mukapeza bulu ali chimangire, ndi mwana wake ali naye pamodzi. Mukaŵamasule nkubwera nawo kuno.
3Wina akakakufunsani kanthu, inu mukati, ‘Ambuye ali nawo ntchito, akangothana nawo aŵatumiza nthaŵi yomweyo.’ ”
4Zimenezi zidaatero kuti zipherezere zimene mneneri adaanena kuti,
5
13Yes. 56.7; Yer. 7.11Adaŵauza kuti, “Malembo akuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo.’ Koma inu mukuisandutsa phanga la achifwamba.”
14Anthu akhungu ndi opunduka adadza kwa Yesu m'Nyumba ya Mulungumo, ndipo Iye adaŵachiritsa.
15Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adaona zodabwitsa zimene Iye ankachita. Adamvanso ana akufuula m'Nyumba ya Mulungu kuti, “Ulemu kwa Mwana wa Davide.” Ndiye iwowo adapsa nazo mtima,
16Mas. 8.2 nafunsa Yesu kuti, “Kodi mukumva zimene akunenazi?” Yesu adaŵayankha kuti, “Inde. Kani simudaŵerenge konse mau a Mulungu aja akuti, ‘Mudaphunzitsa ana ndi makanda omwe kukutamandani kotheratu?’ ”
17Pamenepo Yesu adaŵasiya, natuluka mumzindamo kupita ku Betaniya, nakagona kumeneko.
Yesu atemberera mkuyu(Mk. 11.12-14, 20-24)18M'maŵa mwake, m'mamaŵa ndithu, pamene Yesu ankabwerera ku Yerusalemu, adaamva njala.
19Ataona mkuyu pambali pa mseu, nkupitapo, sadapezepo chilichonse koma masamba okhaokha. Pamenepo adauza mtengowo kuti, “Mtengo iwe, kuyambira tsopano mpaka muyaya usadzabalenso konse zipatso.” Nthaŵi yomweyo mkuyu uja udachita kuti gwa, kuuma.
20Pamene ophunzira aja adaona zimenezi, adadabwa nafunsa Yesu kuti, “Mkuyuwu wauma bwanji nthaŵi yomweyi?”
21Mt. 17.20; 1Ako. 13.2Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati mukhala ndi chikhulupiriro, osakayika, mudzachita zimene ndauchita mkuyuzi. Koma si pokhapo ai, ngakhale mutauza phiri ili kuti, ‘Choka apa, kadziponye m'nyanja,’ zidzachitikadi.
22Ngati mukhala ndi chikhulupiriro, zonse zimene mungapemphe kwa Mulungu mudzalandira.”
Afunsa Yesu za ulamuliro wake(Mk. 11.27-33; Lk. 20.1-8)23Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, ndipo pamene ankaphunzitsa, akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda adadzamufunsa kuti, “Kodi mphamvu zoti muzichita zimenezi mudazitenga kuti? Ndani adakupatsani mphamvu zimenezi?”
24Yesu adati, “Nanenso ntakufunsani funso limodzi. Mukandiyankha, ndiye ndikuuzeni kumene ndidazitenga mphamvu zoti ndizichita zimenezi.
25Kodi Yohane kuti azibatiza, mphamvu zake adaazitenga kwa yani, kwa Mulungu kapena kwa anthu?” Iwo aja adayamba kukambirana nkumati, “Tikati adaazitenga kwa Mulungu, Iyeyu anena kuti, ‘Nanga bwanji tsono simudamkhulupirire?’
26Komanso tikati adaazitenga kwa anthu, anthuŵa satileka, chifukwatu onse amati Yohane anali mneneri.”
27Ndiye adangomuyankha Yesuyo kuti, “Kaya, ife sitikudziŵa.” Apo Iye adati, “Nanenso tsono sindikuuzani kumene ndidazitenga mphamvu zoti ndizichita zimenezi.”
Fanizo la ana aŵiri28“Kodi inu, mukuganiza bwanji? Munthu wina anali ndi ana aamuna aŵiri. Adapita kwa woyamba, nakamuuza kuti, ‘Mwana wanga, pita ukagwire ntchito m'munda wamphesa lero.’
29Iyeyo adati, ‘Toto ine.’ Koma pambuyo pake adasintha maganizo, napitadi.
30Bambo uja adapita kwa mwana wina uja, nakamuuza mau omwe aja. Iyeyo adati, ‘Chabwino atate,’ koma sadapite.
31Kodi mwa aŵiriwo, yemwe adachita zimene bambo wake ankafuna ndi uti?” Iwo adati, “Woyamba uja.” Yesu adaŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti okhometsa msonkho ndi akazi adama akuloŵa mu Ufumu wa Mulungu inu nkumakusiyani m'mbuyo.
32Lk. 3.12; 7.29, 30Paja Yohane Mbatizi adaabwera nadzakuwonetsani njira ya chilungamo, inu osamkhulupirira, m'menemo okhometsa msonkho ndi akazi adama adamkhulupirira. Inuyo ngakhale mudaziwona zimenezo, simudasinthe maganizo pambuyo pake kuti muzimkhulupirira.”
Fanizo la antchito olima m'munda wamphesa(Mk. 12.1-12; Lk. 20.9-19)33 Yes. 5.1, 2 Yesu adati, “Imvani fanizo lina. Munthu wina anali ndi munda wake. M'mundamo adaabzalamo mipesa, namanga mpanda kuzinga mundawo. Adakumba nkhuti yoponderamo mphesa, namanga nsanja yolondera mundawo. Pambuyo pake munda uja adaubwereka alimi, iye nkunyamuka ulendo wa ku dziko lina.
34Nyengo yothyola zipatso itayandikira, munthu uja adatuma antchito ake kwa alimi aja, kuti akatengeko zipatso za m'munda muja.
35Koma alimiwo adaŵagwira antchito aja, wina kummenya, wina kumupha, wina kumponya miyala.
36Munthu uja adatumanso antchito ena, ochuluka koposa oyamba aja, ndipo alimi aja adaŵachita chimodzimodzi.
37Potsiriza pake adaŵatumira mwana wake, nanena kuti, ‘Mwana wanga yekhayu akamchitira ulemu.’
38Koma pamene alimiwo adaona mwana wakeyo, adayamba kuuzana kuti, ‘Ameneyu ndiye amene ati adzamsiyire chumachi. Tiyeni timuphe kuti chidzakhale chathu.’
39Tsono adamugwiradi, namuponya kunja kwa mundawo, nkumupha.
40“Kodi mwini munda wamphesa uja akadzafika, adzaŵatani alimi aja?”
41Iwo adati, “Adzaŵapha moŵazunza alimi oipawo, munda uja nkuubwereka alimi ena amene adzampatsa zipatso zake pa nyengo yake.”
42Mas. 118.22, 23Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi monga simudaŵerenge Malembo aja akuti,
“ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba adaaukana,
womwewo wasanduka mwala wapangodya,
wofunika koposa.
Ambuye ndiwo adachita zimenezi,
ndipo nzotidabwitsa kwambiri.’
43“Nchifukwa chake ndikunenetsa kuti Mulungu adzakulandani Ufumu wake ndi kuupereka kwa anthu ena amene adzabala zipatso zoyenera.”
[
44“Aliyense wogwera pa mwala umenewu, adzasanduka zidutswa zokhazokha. Ndipo aliyense amene mwalawu udzamugwere, udzangomutswanyiratu.”]
45Pamene akulu a ansembe ndi Afarisi adamva mafanizo ameneŵa a Yesu, adazindikira kuti ankanena iwowo,
46motero adafuna kumugwira. Koma ankaopa anthu, popeza kuti ochuluka ankakhulupirira kuti Yesu ndi mneneri.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.