1Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2Yes. 6.9, 10; Yer. 5.21; Mk. 8.18 “Iwe mwana wa munthu, ukukhala pakati pa anthu aupandu. Iwowo maso openyera ali nawo, komabe saona. Makutu omvera ali nawo, komabe saamva, chifukwa choti ngaupandu.
3Tsono iwe mwana wa munthu, longedza katundu wako wopita naye ku ukapolo. Ndipo unyamuke ulendo wako masana ndithu, iwo akuwona, ukachite ngati wopita ku ukapolo kuchoka kwanu kupita ku chilendo, iwowo akuwona. Mwina mwake iwo nkumvetsa ngakhale ali aupandu.
4Katundu wako wopita naye ku ukapolo umtulutse masana, iwo akuwona. Ndipo madzulo, iwo akuwona ndithu, uchoke kumudzi kwanu, monga ngati ukupita ku ukapolo.
5Uboole dzenje pa khoma, iwo akuwona, ndipo utulukire pamenepo.
6Usenze katundu wako pa phewa, iwo akuwona, ndipo upite kunja ku mdima. Uphimbe kumaso kotero kuti sungathe kuwona pansi, chifukwa ndakusandutsa chizindikiro chochenjeza anthu a m'banja la Israele.”
7Ndidachita monga momwe adandiwuzira. Ndidatulutsa katundu wanga masana, nditammanga ngati wopita naye ku ukapolo. Madzulo ndidaboola khoma ndi manja. Pamene chisisira chinkayamba, ndidasenza katundu wanga pa phewa kutuluka naye, iwo akuwona.
8M'maŵa mwake Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
9“Iwe mwana wa munthu, kodi Aisraele, anthu aupandu aja, suja adakufunsa kuti, ‘Ukuchita chiyani?’
10Uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Uthengawu ukunena za kalonga wa ku Yerusalemu ndiponso za banja lonse la Aisraele onse okhala kumeneko.
11Uŵauze kuti iwe ndiwe chizindikiro choŵachenjeza. Zimene zakuchitikira iwe, zidzaŵachitikiranso iwowo. Adzatengedwa kupita ku ukapolo.
12Kalonga wao adzasenza katundu wake nchisisira ndi kunyamuka. Adzatulukira pa dzenje limene anthu adaboola pa khoma, ataphimba kumaso kwake kuti asaone kumene akupita.
132Maf. 25.7; Yer. 52.11 Koma ndidzayala ukonde pa iye ndi kumkola mu msampha wanga. Ndidzapita naye ku Babiloni, ku dziko la Akaldeya, komabe iye sadzalipenya, ndipo adzafera kumeneko.
14Onse okhala naye pafupi, athandizi ake ndiponso ankhondo ake omwe, ndidzaŵabalalitsa ku mbali zonse zinai za dziko lapansi. Ndidzaŵalondola ndi lupanga losolola.
15Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzaŵamwaza pakati pa mitundu yachilendo ndi kuŵabalalitsa ku maiko ambiri.
16Koma ndidzasiyako oŵerengeka amene adzapulumuke ku nkhondo, njala, ndi mliri, kuti akafotokoze nkhani yonse ya zochita zao zonyansa pakati pa mitundu ya anthu kumene akupitako. Apo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
Chizindikiro cha mneneri wonjenjemera17Pambuyo pake Chauta adandipatsiranso uthenga uwu wakuti,
18“Iwe mwana wa munthu, ukamadya, uzinjenjemera. Ukamamwa, uzinthunthumira ndi mantha.
19Anthu am'dzikomo uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta za anthu okhala ku Yerusalemu ndiponso m'dziko la Israele ndi izi: Anthuwo adzadya buledi mwamantha ndi kumwa madzi mwankhaŵa. Dziko lidzafunkhidwa kwathunthu chifukwa cha nkhondo za anthu onse okhala m'menemo.
20Mizinda imene ili ndi anthu idzasakazika, ndipo dziko lidzasanduka chipululu. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
Mwambi ndi tanthauzo lake21Mau a Chauta adandifika akuti,
22“Iwe mwana wa munthu, kodi mwambi umene ukumveka m'dziko la Israelewu ukutanthauza chiyani? Mwambiwo ukuti, ‘Masiku akuchuluka, komabe zolosa sizikuchitika.’
23Tsono uŵauze anthu kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndiwuthetsa mwambi umenewu, sudzamvekanso ku Israele. Koma nthaŵi ili pafupi yoti zonse zimene ndidakuululirani m'masomphenya zidzachitikedi.
24Nthaŵi imeneyo sikudzakhalanso zinthu zina zonama zoziwona ngati kutulo. Sikudzakhalanso kuwombeza koshashalika pakati pa Aisraele.
25Ine Chauta ndidzanena zimene ndidzafune, ndipo zidzachitikadi. Sipakhalanso zochedwa ai, koma masiku anu omwe ano, Ine ndidzalankhula kwa inu anthu aupandunu, ndipo ndidzazichitadi,” ndikutero Ine Ambuye Chauta.
26Chauta adandipatsiranso uthenga uwu wakuti,
27“Iwe mwana wa munthu, Aisraele akunena kuti zinthu zimene ukuziwona tsopano m'masomphenyazi sizidzachitika konse pa zaka zambiri. Akuti ukulosa zinthu za kutsogolo kwambiri.
28Tsono uŵauze kuti, Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Zonena zanga sizidzachedwanso ai. Ndidzachitadi chilichonse chimene ndanena. Ndikutero Ine Chauta!”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.