1Aleksandro, mwana wa Filipo wa ku Masedoniya, wofumira ku dziko la Kitimu, adapambana Dariusi, mfumu ya ku Persiya ndi Mediya pa nkhondo, nakhala mfumu m'malo mwake. Nthaŵiyo nkuti atayamba kale kulamulira dziko la Grisi.
2Adamenya nkhondo zambiri, nalanda mizinda yambiri yamalinga, ndipo adapha mafumu ambiri m'maikomo.
3Adakafika mpaka ku malire a dziko la pansi pano nalanda chuma chambiri cha mitundu ya anthu. Tsono dziko lapansi litakhala phee kugonjera ulamuliro wake, iyeyo adayamba kunyada ndi kutukumuka mtima.
4Adasonkhanitsa gulu lankhondo lamphamvu kwambiri, ndipo adagonjetsa maiko, mafuko ndi mafumu ochuluka namaŵakakamiza kukhoma msonkho kwa iye.
5Pambuyo pake adadwala, nkuzindikira kuti ali pafupi kufa.
6Adaitana nduna zake zolemekezeka, ndiye kuti abwenzi ake amene adaakulira nawo pamodzi, ndipo adaŵagaŵira ufumu wake iye akali moyo.
7Adakhala mfumu zaka khumi ndi ziŵiri, naafa.
8Tsono iye atafa, nduna zake zidaloŵa ufumu, iliyonse m'dera lake.
9Nduna zonsezo zidavala zisoti zaufumu, ndipo pa zaka zambiri ana ao adaloŵa ufumu m'malo mwao. Iwoŵa adabweretsa zoipa zambiri pa dziko lapansi.
Antioko Epifane aloŵetsa zachilendo ku Israele10 2Am. 4.7 Mwa mafumuwo mudafumira wina woipa zedi, dzina lake Antioko Epifane, mwana wa mfumu Antioko. Poyamba adaali m'kaidi ku Roma ngati chigwiriro, pambuyo pake nkukhala mfumu, chaka cha 137 cha ufumu wa Agriki.
11Pa masiku amenewo, pakati pa Aisraele padapezeka ena onyoza Malamulo, ndipo adayamba kukopa anzao ambiri. Ankati, “Tiyeni tikachite nawo chipangano anthu a mitundu ina amene tayandikana nawoŵa, chifukwa kuyambira nthaŵi imene tidapatukana nawo, takhala tikupeza mavuto ambiri.”
12Zimene ankanenazo anthuwo zidaŵakomera.
13Ena mwa iwo, amene ankafunitsitsa zimenezo, adapita kwa mfumu kukafotokoza. Mfumuyo idaŵalola kutsata miyambo ya anthu a mitundu inayo.
14Tsono ku Yerusalemu adamanga bwalo lamaseŵera, potsata mwambo wa mitundu inayo.
151Ako. 7.18Anthu aja adabisa chizindikiro cha kuumbalidwa kwao, nasiya chipangano choyera chija. Motero adagwirizana ndi akunja aja nkudzipereka ku zoipa.
16Ataona kuti ufumu wake walimba, Antioko adaganiza zokhala mfumu ya ku Ejipito, kuti azilamulira kumeneko monga ankachitira ku Siriya.
17Choncho adasonkhanitsa gulu lankhondo lamphamvu, lokhala ndi magaleta, njovu, okwera pa akavalo ndiponso mabwato ambiri, nkukathira nkhondo dziko la Ejipito.
18Atayamba kumenyana nkhondo ndi Ptolemeyo, mfumu ya ku Ejipito, Ptolemeyoyo adabwerera m'mbuyo nathaŵa, ndipo anthu ambirimbiri adaphedwa.
19Asiriya adagonjetsa mizinda yamalinga ya ku Ejipitoko nalanda chuma chonse cha m'dzikolo.
Antioko avuta Ayuda20Atagonjetsa dziko la Ejipito chaka cha 143, Antioko pobwerera kwao, adapita ndi gulu lalikulu la asilikali kukathira nkhondo Aisraele ku Yerusalemu.
21Adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu modzikuza, natenga guwa lansembe lagolide, choikaponyale ndi ziŵiya zake zonse.
22Adalandanso tebulo la Buledi woperekedwa pamaso pa Mulungu, zikho zopatulika ndi mbale zina zagolide, zofukizira zagolide, nsalu zochingira ndiponso zisoti zaulemu. Adachotsanso makaka onse agolide amene anali kumaso kwa Nyumba ya Mulungu.
23Adalanda siliva, golide ndi ziŵiya zamtengowapatali, ndiponso chuma chonse chobisika chimene adachipeza.
24Zonsezo adapita nazo ku dziko lakwao. Adapha anthu ambiri, nkumanena mau achipongwe kwambiri ndi onyada.
25Kunali maliro aakulu ku Israele konse,
26Mafumu ndi akuluakulu adabuula ndi chisoni.
Anyamata ndi atsikana adafooka
ndipo akazi kukongola kwao kudatha.
27Mkwati wamwamuna aliyense adavala zachisoni.
Mkwati wamkazi adabindikira ndi chisoni
m'chipinda mwake.
28Dziko lonse lidanjenjemera modera nkhaŵa
anthu ake,
ndipo banja lonse la Yakobe lidachita manyazi
aakulu.
29Patapita zaka ziŵiri, mfumu idatumiza kapitao wa msonkho ku mizinda ya Yuda, ndipo adakafika ku Yerusalemu ndi gulu lankhondo.
30Kumeneko adaanena mau ake amtendere, koma achinyengo. Ataŵapusitsa choncho anthuwo, adauthira nkhondo mzindawo. Adaukantha moopsa, napha anthu ambiri.
31Tsono adafunkha mzindawo nautentha. Adagwetsa nyumba ndi malinga mbali zonse.
32Akazi ndi ana adaŵatenga kunka nawo ku ukapolo, ndipo adalanda ziŵeto zonse.
33Pambuyo pake adamanganso mzinda wa Davide nauzinga ndi chikhoma chachikulu ndi nsanja zolimba, nukhala boma lankhondo.
34Adakhazikamo anthu ochita zoipa, Ayuda osiya chipembedzo chao.
35Adadzitchinjiriza m'bomamo nasonkhanitsamo zida zankhondo, ndi chakudya. Zonse zimene adaazifunkha ku Yerusalemu adaziika kumeneko. Potero adachita ngati kutcha msampha woopsa.
36Adasanduka olalira Nyumba ya Mulungu
adani oipa mtima
olimbana ndi Aisraele nthaŵi zonse.
37Adapha anthu osalakwa
ponse pozungulira
Nyumba ya Mulungu.
Adaipitsa ndi malo oyera omwe.
38Anthu a ku Yerusalemu adathaŵa,
kuwopa iwowo,
motero mzindawo udasanduka malo a anthu
achilendo.
Udasanduka wachilendo kwa zidzukulu zake,
ndi ana ake omwe adauthaŵa.
39Nyumba yake ya Mulungu idasanduka ngati
chipululu.
Masiku ake achikondwerero adasanduka amaliro.
Masiku ake a Sabata adasanduka onyozeka,
ndipo ulemerero wake udasanduka manyazi.
40Manyazi ake anali aakulu monga momwe
udaaliri ulemerero wake,
chimwemwe chake nkusanduka chisoni.
Kukhazikitsa zipembedzo zachikunja41Pambuyo pake mfumu idakhazikitsa lamulo m'dziko lake lonse, lakuti anthu ake onse akhale amodzi,
42onse asiye miyambo imene inali yaoyao.
43Tsono anthu a mitundu ina adalivomera lamulo la mfumulo. Ndipo ngakhale anthu ambiri a ku Israele nawonso adayamba kutsata chipembedzo chachilendo, namapereka nsembe ku mafano, nkuipitsa tsiku la Sabata lomwe.
44Kenaka mfumu idatuma amithenga ku Yerusalemu ndi ku midzi ya ku Yudeya kukapereka makalata. Idaŵalamula kuti azitsata miyambo ina, yokhala yachilendo kwa anthu am'dzikomo.
45Idaŵaletsa kuti asamaperekenso nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi nsembe zazakumwa ku Nyumba ya Mulungu.
46Idaŵaletsanso kulemekeza masiku a Sabata ndi masiku achikondwerero, nkuŵalamula kuti aipitse Nyumba ya Mulungu ndi atumiki ake.
47Idaŵalamula kumanga maguwa, akachisi ndi nyumba zopembedzeramo mafano, kupereka nsembe za nkhumba ndi nyama zina zonyansa pa chipembedzo.
48Idaŵalamulanso kuti ana ao asamaumbalidwe, ndipo kuti iwo iwowo azidziipitsa mwa njira iliyonse,
49kuti choncho aiŵale Malamulo ndi kusintha miyambo yao yonse.
50Ndipo idanena kuti aliyense wosamvera lamulo la mfumulo adzaphedwa.
51Mfumu idalemba malamulo onsewo kulembera anthu onse a m'dziko lake. Idatuma akapitao kuti azikatsatsitsa anthu onsewo malamulowo. Idalamulanso anthu a m'mizinda ya ku Yuda kuti azipereka nsembe ku mafano mu mzinda uliwonse.
52Choncho Ayuda ambiri adasiya Malamulo aja nayamba kugwirizana ndi anthu otsata zachilendowo, nkumachita zoipa m'dziko.
53Makhalidwe oipawo adaumiriza Aisraele oona kuti athaŵe ndi kukabisala ku malo osiyanasiyana.
54 Dan. 9.27; 11.31; 12.11; 1Am. 6.7; Mt. 24.15; Mk. 13.14 Tsiku la 15 la mwezi wa Kisilevi, chaka cha 145, mfumu idamanga chosakaza chonyansa pa guwa la nsembe zopsereza. Anthu aja adamanganso maguwa a mafano m'mizinda ya ku Yuda ndi m'midzi yake.
55Ankafukiza lubani m'makomo a nyumba ndi m'miseu.
56Mabuku onse a Malamulo amene adaaŵapeza, adaŵang'amba nkuŵatentha.
57Potsata chilamulo cha mfumu, aliyense amene wapezeka ali ndi Buku la Chipangano, kapena akutsata Malamulo, ankamupha.
58Mwezi ndi mwezi ankazunza Aisraele amene ankaŵagwira m'mizinda.
59Tsiku la 25 la mwezi, ankapereka nsembe pa guwa la nsembe zopsereza lija.
602Am. 6.10Potsata chilamulo cha mfumu, akazi onse amene ankaumbalitsa ana ao ankaŵapha,
61ataŵakoleka ana aowo m'khosi, kenaka nkupha anthu a m'banja mwao ndi amene adaŵaumbala.
62Komabe Aisraele ambiri ankalimba mtima, nkumakana kudya chakudya chonyansa pa chipembedzo.
63Ankavomera kufa, osafuna kudziipitsa ndi chakudya chonyansa kapena kuphwanya chipangano choyera. Motero ankaphedwadi.
64Unalidi waukulu mkwiyo wa Mulungu umene udaaŵagwera Aisraele.
Kukhulupirika kwa MatatiasiWho We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.