Lun. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Mphu. 16.3 Ndibwino koposa kukhala wosabereka

koma uli wachilungamo,

chifukwa kulungamako anthu amakukumbukira mpaka muyaya,

kumavomerezedwa ndi Mulungu ndi anthu omwe.

2Mkhalidwe wotere ukakhalapo, timautsanzira,

koma ukakhala palibe, timaulakalaka.

Mpaka muyaya udzayenda patsogolo,

utavala chisoti chaulemerero,

chifukwa udapambana pa nkhondo

ya kulimbana ndi zoipa.

3Koma ana ochuluka a anthu osamvera

adzakhala opandapake.

Poti adabadwira m'chigololo,

sadzazika mizu mozama,

sadzakhala ndi maziko olimba.

4Ngakhale aphuke nthambi pa kanthaŵi,

masinde ao osalimba adzagwedezeka ndi mphepo,

mphepo yamkuntho idzaŵazula.

5Nthambi zao zidzathyoka zisanakhwime,

zipatso zao zidzakhala zosadyeka,

chifukwa ndi zosapsa bwino

ndipo ndi zopandapake.

6Ana obadwira m'chigololo

amakhala mboni zotsutsa makolo ao

pamene Mulungu aweruza mlandu wao.

Kufa msanga kwa anthu olungama

7Koma munthu wolungama,

ngakhale afe msanga,

adzapeza chiwuso.

8Timalemekeza nkhalamba

osati chifukwa cha kutalika kwa moyo

kapena kuchuluka kwa zaka,

9koma nzeru ndiye imvi za munthu,

moyo wosalakwa ndiye ukalamba wake.

10 Gen. 5.21-24; Mphu. 44.16; Ahe. 11.5 Panali munthu wina amene adaakomera Mulungu,

ndipo Mulungu adaamukonda.

Tsono pamene ankakhala pakati pa anthu ochimwa,

Mulungu adamtenga.

11Adamtengako kuti nsanje ingaipitse luntha lake,

chinyengo chingachimwitse mtima wake.

12Chifukwa kukopeka ndi zoipa kumadetsa m'maso,

zilakolako zamitundumitundu zimaipitsa

ngakhale mtima wolungama.

13Koma iyeyo pa nthaŵi yochepa

adasanduka wangwiro,

nakwaniritsa moyo wa zaka zambiri.

14Mtima wake udakomera Ambuye,

nchifukwa chake Ambuyewo adamuchotsa msanga

pakati pa zoipa.

15Anthu ankapenya zimenezi,

komabe sadazimvetse,

ndipo sadazisamale.

Sadazindikire kuti Mulungu amakomera mtima

osankhidwa ake,

ndi kuŵachitira chifundo,

ndikutinso amatchinjiriza anthu ake oyera mtima.

16Koma olungama amene afa

amatsutsa amene akali moyo

koma ali osamvera.

Ndipo anyamata oyera mtima otsirizika msanga

amatsutsa okalamba a zaka zambiri

pamene iwo ali osalungama.

17Anthu amaona kutha kwa munthu wolungama,

koma osamvetsa cholinga cha Chauta

chakuti imeneyi ndiye njira

yomutchinjirizira ku zoopsa.

18Anthu amamuwona nkumamunyoza,

koma Ambuye adzaŵanyodola iwowo.

Iwowo akadzafa, maliro ao adzakhala osalemekezeka,

adzanyozeka nthaŵi zonse

ngakhale pakati pa anthu akufa omwe.

19Ndithudi Ambuye adzaŵakantha

nkuŵagwetsa chadodolido,

iwowo pansi thi osanena kanthu.

Maziko ao adzagwedezeka,

anthu onsewo adzakhala ngati nthaka youma

yosabereka kanthu.

Adzamva mazunzo,

ndipo maina ao sadzakumbukikanso.

Za olungama ndi osalungama pa tsiku la chiweruzo

20Pamene azidzaŵerengera machimo ao,

anthu ochimwawo adzabwera ali ndi nkhaŵa,

ndipo zoipa zaozo zidzaŵaukira nkuŵatsutsa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help