Chiv. 14 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za nyimbo ya anthu oomboledwa

1 Ezek. 9.4; Chiv. 7.3 Pambuyo pake nditayang'ana, ndidaona Mwanawankhosa ataimirira pa Phiri la Ziyoni. Pamodzi ndi Iye panali anthu zikwi 144, olembedwa dzina lake ndiponso dzina la Atate ake pamphumi pao.

22Es. 6.17Tsono ndidamva liwu lochokera kumwamba longa ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Liwu limene ndidaamvalo linkamveka ngati anthu akuimba azeze ao.

3Anthu aja ankaimba nyimbo yatsopano pamaso pa mpando wachifumu uja ndi pamaso pa Zamoyo zinai zija, ndi Akuluakulu aja. Panalibe ndi mmodzi yemwe wotha kuiphunzira nyimboyo, kupatula anthu zikwi 144 aja amene anali ataomboledwa mu ukapolo wa dziko lapansi.

4Ndi ameneŵa amene ankadzisunga angwiro osadziipitsa ndi akazi. Ndi ameneŵa amene amatsata Mwanawankhosa uja kulikonse kumene akupita. Ndiwo amene adaomboledwa pakati pa anthu ena onse, kuti akhale oyambirira kuperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa uja.

5Zef. 3.13Sadanenepo bodza konse. Alibe cholakwa.

Za angelo atatu

6Pambuyo pake ndidaona mngelo wina akuuluka mu mlengalenga. Anali ndi Uthenga Wabwino wamuyaya woti akalalike kwa anthu okhala pa dziko lapansi, kwa anthu a mtundu uliwonse, a fuko lililonse, ndi a chilankhulo chilichonse.

7Mngeloyo adanena mokweza mau kuti, “Opani Mulungu ndi kumtamanda, pakuti yafika nthaŵi yoti aweruze anthu. Mumpembedze Iye amene adalenga thambo, dziko lapansi, nyanja, ndi akasupe a madzi.”

8 Yes. 21.9; Yer. 51.8; Chiv. 18.2 Padafika mngelo wina wachiŵiri wotsatana ndi woyamba uja. Adati, “Wagwa, wagwa Babiloni wotchuka uja, amene ankamwetsa anthu a mitundu yonse vinyo wa zilakolako zake zadama.”

9Kenaka padafikanso mngelo wina wachitatu, wotsatana ndi aŵiri ena aja. Mokweza mau adati, “Aliyense wopembedza chilombo chija ndi fano lake, ndi kulembedwa chizindikiro pa mphumi kapena pa dzanja,

10Yes. 51.17; Gen. 19.24; Ezek. 38.22nayenso adzamwako vinyo wa ukali wa Mulungu. Vinyo wake adzathiridwa, popanda kanthu kochepetsa mphamvu yake, m'chikho cha mkwiyo wa Mulungu. Munthuyo adzazunzidwa ndi moto ndi miyala yasulufure yoyaka. Zimenezi zidzachitikira pamaso pa angelo a Mulungu, ndi Mwanawankhosa uja.

11Yes. 34.10Utsi wa moto woŵazunzawo umakwera kumwamba mpaka muyaya. Anthu amene adapembedza chilombo chija ndi fano lake, ndiponso amene adalembedwa chizindikiro cha dzina lake chija, sapeza mpumulo usana kapena usiku.

12“Pamenepa mpofunika kuti anthu a Mulungu akhale opirira, amene amatsata malamulo ake ndipo ali ndi chikhulupiriro mwa Yesu.”

13Pambuyo pake ndidamva mau ochokera Kumwamba. Adati, “Lemba kuti, Ngodala anthu akufa amene kuyambira tsopano mpaka m'tsogolo muno afa ali otumikira Ambuye.” Mzimu Woyera akuti, “Inde, ngodaladi. Akapumule ntchito zao zolemetsa, pakuti ntchito zaozo zimaŵatsata.”

“Nyengo ya masika yafika”

14 Dan. 7.13 Pambuyo pake nditayang'ana ndidaona mtambo woyera. Pamtambopo padaakhala wina ngati Mwana wa Munthu, kumutu atavala chisoti chaufumu chagolide, m'manjamu ali ndi chikwakwa chakuthwa.

15Yow. 3.13Mngelo wina adatuluka m'Nyumba ya Mulungu nafuula ndi mau amphamvu kwa Uja wokhala pamtamboyu. Adati, “Gwiritsa ntchito chikwakwa chako, yambapo kudula dzinthu. Tsopano nyengo yamasika yafika, ndipo dzinthu dza pa dziko lapansi dzidacha kale.”

16Pamenepo wokhala pamtambo uja adakayambadi ntchitoyo ndi chikwakwa chake, nadula dzinthu dzonse dza pa dziko lapansi.

17Pambuyo pake mngelo wina adatuluka m'Nyumba ya Mulungu Kumwamba. Nayenso anali ndi chikwakwa chakuthwa.

18Kenaka mngelo winanso, amene amalamulira moto, adatulukira kuchokera ku guwa lansembe. Adafuula ndi mau amphamvu kwa Uja wokhala ndi chikwakwa chakuthwa. Adati, “Gwiritsa ntchito chikwakwa chakocho, yambapo kudula mphesa za m'munda wamphesa wa pa dziko lapansi, pakuti mphesazo zidapsa kale.”

19Pamenepo mngelo uja adakayambadi ntchitoyo ndi chikwakwa chake, nadula mphesa zonse za pa dziko lapansi, nkuziponya m'chopondera mphesa cha ukali woopsa wa Mulungu.

20Yes. 63.3; Mali. 1.15; Chiv. 19.15Mphesazo zidapondedwa m'chopondera mphesa kunja kwa mzinda. Ndipo m'chopondera mphesacho mudatuluka magazi nkumayenderera ngati mtsinje, kutalika kwake makilomita 300, kuzama kwake ngati mita ndi hafu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help