1 Num. 20.2-13 Khamu lonse la Aisraele lija lidachoka ku chipululu cha Sini kuja, ndipo linkangoyenda kuchoka pa chigono china mpaka pa chigono chinanso, monga momwe Chauta ankalamulira. Tsono adakamanga mahema ku Refidimu. Kumeneko kunalibe madzi akumwa.
2Ndiye anthuwo adayamba kukangana ndi Mose, namanena kuti, “Tipatseni madzi akumwa.” Mose adaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukukangana ndi ine? Chifukwa chiyani mukuyesa Chauta?”
3Koma anthu aja anali ndi ludzu loopsa, ndipo ankangoŵiringulira Mose, kuti “Chifukwa chiyani mudatitulutsa ku Ejipito kuti mutiphe ndi ludzu, ife pamodzi ndi ana athu ndi zoŵeta zathu?”
4Apo Mose adapemphera mokweza mau kwa Chauta, adati, “Kodi anthu ameneŵa ndichite nawo chiyani? Iwowo ngokonzeka kundiponya miyala.”
5Pamenepo Chauta adauza Mose kuti, “Tengako atsogoleri ena a Aisraele, mukakhale patsogolo pa anthuwo. Tsono utenge ndodo udamenya nayo madzi a mu mtsinje wa Nailo ija, ndipo upite.
6Ine ndidzakhala patsogolo pako kumeneko pafupi ndi thanthwelo, pa phiri la Horebu. Ukamenye thanthwe, tsono mudzatuluka madzi m'thanthwemo, kuti anthuwo amwe.” Mose adachitadi zimenezo pamaso pa atsogoleri a Aisraele aja.
7Malowo adaŵatcha Mayeso ndiponso Makangano, chifukwa Aisraele adakangana ndi Mose, ndipo adayesa Chauta pofunsa kuti, “Kodi Chauta ali nafe, kapena ai?”
Aisraele amenyana ndi Aamaleke8Tsono kudabwera Aamaleke ku Refidimu kudzamenyana ndi Aisraele.
9Mose adauza Yoswa kuti, “Tisankhulireko amuna ena, maŵa mupite kukamenyana nawo nkhondo Aamaleke. Ine ndidzaimirira pamwamba pa phiri, nditagwira ndodo adandipatsa Mulungu ija.”
10Yoswa adachitadi monga momwe Mose adalamulira, adatuluka kukamenyana ndi Aamalekewo. Nthaŵi yomweyo Mose, Aroni ndi Huri adakwera pamwamba pa phiri.
11Mose ankati akakweza manja ake, Aisraele ankapambana pa nkhondoyo, koma akatsitsa pansi manja, Aamaleke ankapambana.
12Tsono manja a Mose atatopa, Aroni pamodzi ndi Huri uja adatenga mwala namkhazikira Mose kuti akhalepo. Aŵiriwo adakhala wina uku wina uku, atagwirira manja a Mose aja. Adaŵagwirira ndithu mpaka dzuŵa kuloŵa.
13Ndipo Yoswa adagonjetseratu kwathunthu Aamalekewo.
14 Deut. 25.17-19; 1Sam. 15.2-9 Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Zimenezi muzilembe m'buku kuti zidzakumbukike, ndipo munene pamaso pa Yoswa kuti Aamalekewo adzafafanizika kwathunthu.”
15Ndipo Mose adamanga guwa nalitcha kuti, “Chauta ndiye mbendera yanga.”
16Adati, “Kwezetsani mbendera ya Chauta! Chauta adzapitirirabe kumenya nkhondo ndi Aamaleke mpaka muyaya.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.