1 Deut. 11.13-17 Mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata mosamala malamulo onse amene ndikukupatsani leroŵa, Chauta, Mulungu wanu, adzakukwezani kopambana mitundu yonse ya pa dziko lapansi.
2Mverani Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzalandira madalitso onse aŵa:
3Chauta adzadalitsa mizinda yanu ndi minda yanu.
4Chauta adzadalitsa ana anu ndi zokolola zanu, ndi ana a zoŵeta zanu, ndipo adzakupatsani ng'ombe ndi zoŵeta zina zambiri.
5Chauta adzadalitsa mbeu zanu ndi chakudya chimene muchikonza kuchokera ku mbeuzo, kuti zichuluke.
6Chauta adzadalitsa zochita zanu zonse.
7Chauta adzakuthandizani kuti mugonjetse adani anu pamene akuukirani. Pokuukirani adzatulukira njira imodzi, koma pothaŵa adzathaŵira m'zikuŵa zisanu ndi ziŵiri.
8Chauta adzadalitsa ntchito zanu, ndipo nkhokwe zanu zidzadzaza. Adzakudalitsani m'dziko limene akukupatsanilo.
9Chauta adzakusandutsani anthu opatulikira Iye monga adalonjezera, malinga mukachita zonse zimene akukulamulani ndi kuyenda m'njira yake.
10Tsono anthu onse a pa dziko lonse lapansi adzaona kuti Chauta, Mulungu wanu, wakusankhani inu kuti mukhale anthu akeake, ndipo azidzakuwopani.
11Chauta adzakudalitsani pokupatsani ana ambiri, zoŵeta zambiri ndiponso zokolola zambiri. Zonsezi adzakupatsani m'dziko limene Iye adalonjeza kwa makolo anu kuti adzakupatsani.
12Pa nyengo yake, adzakutumizirani mvula kuchokera kumene amaisunga mu mlengalenga, ndipo adzadalitsa ntchito zanu zonse, kotero kuti inuyo muzidzakongoza mitundu ina zinthu, koma inuyo osakongola kwa aliyense.
13Mulungu wanu adzakusandutsani atsogoleri pakati pa mitundu ya anthu, osati otsata pambuyo. Mukamamvera malamulo ake amene ndikukupatsani lero ndi kuŵatsatadi mosamala, mudzakhala okwera nthaŵi zonse, osati otsika.
14Choncho pa mau ndikukuuzani leroŵa, musapatuke kumanja kapena kumanzere, pakutsata milungu ina ndi kumaitumikira.
Zotsatira za kusamvera(Lev. 26.14-46)15Komatu mukapanda kumvera bwino mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero lino, adzakugwerani matemberero aŵa:
16Chauta adzatemberera mizinda yanu ndi minda yanu.
17Chauta adzatemberera zokolola zanu ndiponso zokandiramo ufa wanu.
18Chauta adzakutembererani pokupatsani ana oŵerengeka, zokolola zochepa, ndiponso ng'ombe ndi zoŵeta zina pang'ono chabe.
19Chauta adzatemberera ntchito zanu zonse.
20Mukamachita zoipa ndi kumkana Mulungu, Iye adzakutumizirani matemberero, chisokonezo ndiponso zokuvutani pa ntchito zanu zonse, mpaka mutaonongeka ndi kufa nonsenu pa kamphindi kochepa.
21Adzakutumizirani matenda otsatanatsatana, mpaka mutatha nonse kuti psiti m'dziko limene muli kukakhalamolo.
22Chauta adzakukanthani ndi nthenda zopatsana, zotupatupa ndi zamalungo. Adzakutumiziraninso kutentha koopsa ndi chilala ndiponso chinsikwi ndi chinoni zoononga mbeu zanu. Masoka amenewo adzakhala pa inu mpaka kukufetsani.
23Mvula sidzakugwerani ndipo nthaka yanu idzauma kuti gwa ngati chitsulo.
24M'malo mwa mvula, Chauta adzakugwetserani fumbi ndi mchenga, mpaka mutaonongeka nonse.
25Chauta adzalola kuti adani anu akugonjetseni. Pokalimbana nawo mudzadzera njira imodzi, koma poŵathaŵa mudzapanga zikuŵa zisanu ndi ziŵiri. Ndipo mafumu onse a pa dziko lapansi adzaopsedwa poona zokuchitikiranizo.
26Mutafa, mbalame pamodzi ndi nyama zakuthengo zidzadya mitembo yanu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzazipirikitse.
27Chauta adzakulangani ndi zithupsa zonga za ku Ejipito zija. Mudzakhala ndi zilonda, mphere, ndi kunyerenyesa, zonsezo zosamva mankhwala. Thupi lanu lidzakhala la mphere zokhazokha, ndipo muzidzangokandakanda, koma osachira.
28Chauta adzakuchititsani misala, ndipo adzakusandutsani akhungu ndi osokonezeka.
29Ngakhale dzuŵa lili nye, muzidzachita kufufuza njira ngati anthu akhungu. Kalikonse kamene mudzachite simudzalemera nako. Kaŵirikaŵiri azidzakupsinjani ndi kumakuberani, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzakuthandizeni.
30Mudzafunsira mbeta mtsikana, koma ndi wina amene adzakwatirane naye. Kumanga nyumba mudzamanga ndithu, koma simudzagonamo. Munda wamphesa mudzabzala, koma mphesa zake simudzadyako.
31Ng'ombe zanu azidzakupherani mukupenya, koma nyama yake simudzadyako. Abulu anu azikaŵalanda mwamphamvu ndi kupita nawo kwina, inu mukupenya, ndipo sadzakubwezerani. Nkhosa zanu adzazipereka kwa adani anu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzakuthandizeni.
32Ana anu aamuna ndi aakazi adzatengedwa ukapolo ndi alendo, inu mukupenya. Tsiku ndi tsiku maso anu adzakhala ali psuu kuyang'anira ngati ana anuwo abwere, koma simudzaphulapo kanthu.
33Mtundu wachilendo udzakulandani zakumunda zanu zonse zimene mudathyoka nazo msana polima, ndipo mudzapsinjidwa ndi kuzunzika mosalekeza.
34Zimene mudzaziwona ndi maso zidzakupengetsani.
35Chauta adzabweretsa zilonda zoŵaŵa ndi zosachizika pa maondo ndi pamisongolo panu, ndipo anamkalimbwi azidzakutulukani thupi lonse, kuyambira kuphazi mpaka kumutu.
36Chauta adzaipirikitsira ku dziko lachilendo mfumu yanu, pamodzi ndi inu nomwe, kumene inuyo ndi makolo anu simudakhaleko nkale lonse. Kumeneko muzikatumikira milungu ina yopanga ndi mitengo ndi miyala.
37Ku mitundu yonse kumene Chauta adzakumwazireniko, anthu adzadabwa nanu, adzakusekani, adzakupekani nthano yokunyodolani.
38Mudzabzala zambiri, koma mudzakolola pang'ono chabe, chifukwa dzombe lidzadya zolima zanuzo.
39Minda yamphesa mudzalimadi, mpaka kuisamala bwino, koma mphesa zake simudzathyola kapena kumwako vinyo wake, chifukwa tizilombo ndito tidzadye mphesazo.
40Mitengo ya olivi izidzamera paliponse m'dziko mwanumo, koma mafuta a olivi simudzakhala nawo, chifukwa zipatso za olivizo zidzayoyoka.
41Mudzabereka ana aamuna ndi aakazi ndithu, koma sadzakhala anu, chifukwa adzatengedwa ukapolo.
42Mitengo yanu yonse ndi dzinthu dzanu dzam'munda zidzatha ndi tizilombo.
43Alendo okhala m'dziko mwanu ndiwo amene azidzakwererakwerera, koma inu muzidzatsikiratsikira.
44Iwowo azidzakukongozani ndalama, koma inu simudzakhala nazo ndi pang'ono pomwe zoŵakongoza, ndipo potsiriza adzakulamulirani.
45Masoka onseŵa adzakugwerani. Adzakhala pa inu mpaka mutaonongeka, chifukwa choti simudamvere Chauta, Mulungu wanu, ndipo simudatsate malamulo ndi malangizo onse amene Iye adakupatsani.
46Masoka onseŵa adzakhala mboni yapadera ya chilango cha Mulungu pa inu ndi pa zidzukulu zanu mpaka muyaya.
47Paja Chauta adakudalitsani pa zonse, komabe inu simudamtumikire mokondwa ndi mitima yachimwemwe.
48Motero mudzatumikira adani odzalimbana nanu amene Chauta adzakutumizireni. Mudzamva njala ndi ludzu. Zinthu zonse zidzakusoŵani pamodzi ndi zovala zomwe. Chauta adzakuzunzani mwankhanza, mpaka mutaonongeka.
49Chauta adzaitanitsa mtundu wa anthu ochokera ku malekezero a dziko lapansi, kuti adzamenyane nanu. Anthu a mtundu umenewo amene inu simudziŵa chilankhulo chao, adzakuterani ngati mphungu.
50Anthuwo adzakhala aukali, ndipo sadzachita chifundo ndi aliyense, ngakhale akhale mwana kapena nkhalamba.
51Adzakudyerani ng'ombe zanu pamodzi ndi zakumunda zanu zomwe, mpaka mudzafa ndi njala. Sadzakusiyiraniko mpang'ono pomwe tirigu, vinyo, mafuta aolivi, ng'ombe kapena nkhosa, ndipo mudzafadi.
52Adzathira nkhondo mzinda uliwonse, m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo. Ndipo malinga ataliatali amene mukuŵakhulupirirawo adzagwa ponseponse. Adzakuzingani m'mizinda yonse ya m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsanilo.
53Nthaŵi imene adani anu adzazinga mizinda yanu ndi kukusautsani koopsa, mudzasoŵa chakudya kotheratu, kotero kuti muzidzadya ana anu omwe aamuna ndi aakazi, amene Chauta adakupatsani.
54Ngakhale munthu amene ali woleredwa bwino ndi wofatsa mtima kwambiri mwa inu, adzamana chakudya mbale wake, mkazi wake wapamtima ndi ana ake omutsalira,
55mwakuti sadzapatsako ndi mmodzi yemwe nyama ya ana ake amene akuŵadya, chifukwa adzakhala alibiretu chakudya pa nthaŵi imene adani anu azidzakuzingani ndi kukusautsani koopsa.
562Maf. 6.28, 29; Mali. 4.10Ngakhale mkazi woleredwa bwino ndi wolobodoka kotero kuti sangayese nkomwe kupondetsa pansi phazi lake, adzamana mwamuna wake wapamtima ndi ana ake onse
57nyama ya ana ake ongobadwa kumene, pamodzi ndi za matenda ake zomwe zochokera m'mimba mwake, popeza kuti azidzadya zimenezi yekha mobisa, chifukwa cha kusoŵeratu chakudya, nthaŵi imene adani anu adzazinga mizinda yanu ndi kukusautsani kwambiri.
58Muzimvera mau onse a malamulo aŵa a m'buku muno, ndipo dzina ili lodabwitsa ndi lochititsa mantha la Chauta, Mulungu wanu, muzilitamanda.
59Mukapanda kutero, inuyo ndi zidzukulu zanu, Chauta adzakugwetserani masautso apadera, mavuto aakulu okhalitsa ndiponso nthenda zoopsa zosamva mankhwala.
60Nthenda zonse zoopsa zimene mudaopsedwa nazo muli ku Ejipito kuja, Chauta adzakugwetserani zimenezo, ndipo simudzachira.
61Adzakugwetseraninso nthenda zonse zamitundumitundu pamodzi ndi miliri yomwe, zimene sizidatchulidwepo m'buku la malamulo a Mulungu, ndipo mudzaonongeka.
62Ngakhale mudaachuluka ngati nyenyezi zakuthambo, koma amoyo mudzakhala ochepa, chifukwa choti simudamvere Chauta, Mulungu wanu.
63Monga momwe kudakomera Chauta kukudalitsani ndi kukuchulukitsani kuti mukhale ambiri, momwemo kudzamkomeranso kuti akuwonongeni kotheratu. Adzakuchotsani m'dziko limene mukuliloŵa kukakhalamolo.
64Ndipo Chauta adzakumwazani pakati pa mitundu yonse, kuyambira ku malekezero ena a dziko mpaka ku malekezero ake enanso. Kumeneko muzidzapembedza milungu yamitengo ndi yamiyala, imene inu ndi makolo anu simudaidziŵe nkale lonse.
65Simudzapeza mtendere kwina kulikonse ndipo malo anuanu simudzaŵapeza. Mudzakhala ankhaŵa, osoŵa thandizo ndi otaya mtima, ndipo Chauta ndiye adzagwetse zimenezi pa inu.
66Nthaŵi zonse, moyo wanu udzakhala wopenekapeneka. Muzidzakhala amantha, usiku ndi masana womwe, ndipo muzidzangokhalira kuwopa imfa.
67Mitima yanu idzakhala yamantha poona kalikonse. M'maŵa mulimonse muzidzangofuna kuti kude. Madzulo aliwonse muzidzafuna kuti kuche.
68Ndipo Chauta adzakutumizaninso ku Ejipito m'zombo zapanyanja, ngakhale kuti ndidaalonjeza kuti simudzapitakonso. Kumeneko mudzayesayesa kudzigulitsa ngati akapolo kwa adani anu, koma palibe ndi mmodzi yemwe amene adzafune kukugulani.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.