1Inu Chauta nditati nditsutsane nanu,
wokhoza ndinu ndithu.
Komabe ndifuna kudandaulako kwa Inu
za mlandu wanga.
Chifukwa chiyani anthu oipa
zinthu zimaŵayendera bwino?
Chifukwa chiyani anthu osakhulupirika
amakhala pabwino?
2Inu mudaŵabzala, ndipo adamera mizu.
Amakula, namabala zipatso.
Amakonda kulankhula za Inu,
koma mitima yao ili kutali ndi Inu.
3Koma Inu Chauta ine mumandidziŵa.
Mumandiyang'ana, ndipo mumayesa mtima wanga,
nkuwona kuti ndimakukondani.
Muŵakoke anthu oipa ngati nkhosa zokaphedwa.
Muŵaike padera mpaka tsiku loti akaphedwe.
4Kodi dziko lidzakhala likulirabe mpaka liti?
Ndipo udzu wake udzakhalabe wouma mpaka liti?
Palibe mbalame kapena nyama zimene zatsala
chifukwa anthu okhalamo ndi oipa kwambiri.
Amati, “Mulungu sadzaona zimene
zidzatiwonekere masiku athu otsiriza.”
5Chauta adayankha kuti,
“Ngati kukutopetsa kuthamanga ndi anthu,
nanga udzapikisana bwanji ndi akavalo?
Ngati mtima wako ulefuka m'dziko lokoma,
nanga udzatani m'nkhalango ya ku Yordani?
6Ngakhale abale ako ndi anansi ako
nawonso amakuchita chiwembu,
onsewo amvana pa zokuimba mlandu,
usaŵakhulupirire,
ngakhale alankhule nawe mau okoma.
Chauta aŵamvera chisoni anthu ake7“Banja la Israele ndalisiya,
ndaŵataya anthu amene ndidaŵasankha.
Okondeka anga ndaŵapereka kwa adani ao.
8Anthu anga osankhidwa
asanduka ngati mikango yakuthengo,
amandidzumira mwaukali.
Nchifukwa chake ndimadana nawo.
9Anthu anga osankhidwa
ali ngati mbalame yamaŵangamaŵanga
imene akabaŵi aizinga kuchokera konsekonse.
Kasonkhanitseni nyama zakuthengo,
mubwere nazo ku phwando.
10Abusa ambiri adaononga munda wanga
wamphesa, adapondereza munda wanga.
Munda wokoma uja adausandutsa chipululu.
11Ndithu adausandutsa chipululu,
ukundilirira Ine uli wokhawokha.
Dziko lonse lasanduka chipululu,
ndipo palibe amene akusamalako.
12Anthu oononga abalalikira
ku zitunda zonse zam'chipululu.
Ndipo Ine Chauta ndatuma ankhondo kuti
akanthe dziko lonse,
kuyambira ku malire ena
mpaka ku malire enanso.
Palibe aliyense amene angapeze mtendere.
13Anthu adafesa tirigu,
koma adakolola minga.
Adadzitopetsa pogwira ntchito,
koma osapindula nkanthu komwe.
Zokolola zao nzochititsa manyazi,
chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Chauta.”
Za Chilango cha maiko ena14Chauta akuti, “Anthu oipa onse oyandikana ndi Aisraele, akulanda Aisraelowo dziko, choloŵa chimene ndidapatsa anthu angawo. Nchifukwa chake ndidzaŵachotsa m'dziko limenelo, ndipo ndidzachotsa banja la Yuda pakati pao.
15Komabe nditaŵachotsa, ndidzaŵamveranso chifundo, ndipo ndidzabwezanso mtundu uliwonse ku dziko la choloŵa chake.
16Tsono iwo akadzaphunzira bwino njira za mayendedwe a anthu anga, ndi kumalumbira m'dzina langa kuti, ‘Pali Chauta Wamoyo,’ monga momwe iwo adaphunzitsira anthu anga kumalumbira m'dzina la Baala, ndiye kuti iwowo ndidzaŵakhazikitsa pakati pa anthu anga.
17Komatu ngati mtundu wina uliwonse sudzamvera Ine, ndidzauwononga kotheratu.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.