1Solomoni adapalana chibwenzi ndi Farao mfumu ya ku Ejipito pokwatira mwana wa Faraoyo. Adabwera naye mkaziyo ku mzinda wa Davide ku Yerusalemu, nakhala naye komweko mpaka atamaliza kumanga nyumba yake yatsopano ndi Nyumba ya Chauta ndiponso linga lozungulira mzindawo.
2Anthu nsembe ankatsirirabe ku akachisi osiyanasiyana, chifukwa choti nthaŵi imeneyo anali asanammangire nyumba Chauta.
3Solomoni ankakonda Chauta, namasunga malamulo a Davide bambo wake. Komabe ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani ku akachisi aja.
4 Lun. 9.1-18 Nthaŵi ina mfumu idapita ku Gibiyoni kukapereka nsembe, popeza kuti kumeneko ndiko kunali kachisi woposa ena. Solomoni ankapereka nsembe zopsereza pa guwa limenelo zokwanira 1,000.
5Ku Gibiyoniko Chauta adamuwonekera Solomoni m'maloto usiku, namuuza kuti, “Upemphe chilichonse chimene ufuna kuti ndikupatse.”
6Solomoni adati, “Inu Mulungu, mudaonetsa chikondi chanu chachikulu ndi chosasinthika kwa mtumiki wanu Davide, bambo wanga, chifukwa choti ankachita zokhulupirika ndi zolungama, ndipo ankayenda moongoka mtima pamaso panu. Ndipo mudamuwonetsabe chikondi chachikulu ndi chosasinthikacho, pakumpatsa mwana amene wakhala pa mpando waufumu wake masiku ano.
7“Tsopano, Inu Chauta Mulungu wanga, mwaika mtumiki wanune pa malo a Davide bambo wanga, ngakhale ndine mwana wamng'ono chabe, ndipo sindidziŵa kagwiridwe kake ka ntchito yanga.
8Tsono ine mtumiki wanu ndikukhala pakati pa anthu amene mudaŵasankha, mtundu waukulu, anthu ake ochuluka, oti nkosatheka kuŵaŵerenga.
9Nchifukwa chake mundipatse mtumiki wanune nzeru zolamulira anthu anu, kuti ndizidziŵa kusiyanitsa zabwino ndi zoipa. Nanga popanda nzeruzo ndani angathe kulamulira mtundu waukulu chotere wa anthu anu?”
10Zidaŵakomera Ambuye kuti Solomoni adapempha zimenezi.
11Tsono Mulungu adauza Solomoni kuti, “Chifukwa chakuti wapempha zimenezi, osapempha moyo wautali kapena chuma kapena imfa ya adani ako, koma nzeru zolamulira anthu bwino,
12ndiye Ine ndikuchitira zimene wapempha. Zoona, ndikupatsa mtima wanzeru ndi waluntha, kotero kuti sadaonekepo nkale lonse wina wofanafana nawe, ndipo sadzaonekanso wina wolingana nawe, iweyo utafa.
13Kuwonjezera pamenepo, ndikukupatsanso zimene sudapemphe: chuma ndi ulemu, kotero kuti palibe mfumu imene idzalingane nawe pa masiku onse a moyo wako.
14Ndipo ukamadzandimvera ndi kumasunga malamulo anga, monga momwe ankachitira bambo wako Davide, udzakhala ndi moyo wautali kwabasi.”
15Solomoni adadzuka nazindikira kuti anali maloto. Adabwerera ku Yerusalemu, nakaimirira patsogolo pa Bokosi lachipangano la Chauta. Kumeneko adapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, kenaka adakonzera nduna zake zonse phwando.
Solomoni aweruza mlandu wovuta16Tsiku lina akazi aŵiri adama adadza kwa Solomoni naimirira pamaso pake.
17Mkazi woyamba adati, “Inu mbuyanga, ine ndi mnzangayu timakhala nyumba imodzi. Tsono ine ndidaona mwana, mnzangayu ali m'nyumba momwemo.
18Tsiku lachitatu lake, ine nditachira kale, mnzangayu nayenso adaona mwana. Ndipo ifeyo tinali tokha, panalibe munthu wina aliyense m'nyumbamo, koma aŵiri tokhafe.
19Koma mwana wa mnzangayu adafa usiku, chifukwa adaamugonera.
20Tsono iyeyu adadzuka pakati pa usiku, natenga mwana wanga kumimba kwanga namgoneka kumimba kwake, ndipo adagoneka mwana wake wakufayo kumimba kwanga. Nthaŵiyo nkuti mdzakazi wanune ndili m'tulo.
21M'maŵa nditadzuka kuti ndiyamwitse mwana wanga, ndidaona kuti ngwakufa. Koma nditayang'anitsitsa, ndidaona kuti si mwana wanga ai.”
22Koma mkazi wina uja adamdula pakamwa nati, “Iyai, mwana wamoyoyu ndiye wanga, wako ndi wakufayu.” Mkazi woyamba uja adati, “Iyai, mwana wakufayu ngwako, koma wamoyoyu ngwanga.” Adaatero kulankhula kwake azimaiwo pamaso pa mfumu.
23Tsono mfumu idati, “Wina akuti, ‘Mwana wamoyoyu ngwanga,’ winanso akuti, ‘Iyai, mwana wako ngwakufayu, wanga ngwamoyoyu.’ ”
24Ndiye mfumuyo idati, “Patseni lupanga.” Adabwera nalo lupanga kwa mfumu.
25Tsono mfumu idagamula kuti, “Mduleni pakati mwana wamoyoyu, aliyense mwa azimai aŵiriŵa mumpatse chigawo chimodzi.”
26Pomwepo mai amene anali mwini wake wa mwana wamoyoyo adagwidwa ndi chisoni chachikulu mu mtima chifukwa cha mwanayo. Choncho adauza mfumuyo kuti, “Pepani, mbuyanga, ingompatsani iyeyu mwana wamoyoyu, musamuphe, ndakupembani.” Koma mai wina uja adati, “Iyai asapatse ine kapena iwe, amdule pakati basi!”
27Tsono mfumu idayankha kuti, “Perekani mwana wamoyoyu kwa mai woyamba uja, musamuphe ai. Ameneyu ndiye mai wake wa mwanayu.”
28Ndipo Aisraele onse adamva za m'mene mfumu idagamulira mlanduwo. Motero anthu adayamba kulemekeza Solomoni, chifukwa adaona kuti anali ndi nzeru za Mulungu zoweruza mwachilungamo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.