Num. 13 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Azondi(Deut. 1.19-33)

1Chauta adauza Mose kuti,

2“Tuma anthu kuti akazonde dziko la Kanani limene ndikupatsa Aisraele. Pa fuko lililonse utume munthu mmodzi, amene ali mtsogoleri m'fukolo.”

3Choncho Mose adaŵatuma kuchokera ku chipululu cha Parani, monga momwe Chauta adaalamulira, ndipo onsewo anali atsogoleri a Aisraele.

4Maina ao ndi aŵa: m'fuko la Rubeni, adatuma Samuwa mwana wa Zakuri.

5M'fuko la Simeoni, adatuma Safati mwana wa Hori.

6M'fuko la Yuda, adatuma Kalebe mwana wa Yefune.

7M'fuko la Isakara, adatuma Igala mwana wa Yosefe.

8M'fuko la Efuremu, adatuma Hoseya mwana wa Nuni.

9M'fuko la Benjamini, adatuma Paliti mwana wa Rafu.

10M'fuko la Zebuloni, adatuma Gadiele mwana wa Sodi.

11M'fuko la Yosefe (ndiye kuti m'fuko la Manase) adatuma Gadi mwana wa Susi.

12M'fuko la Dani, adatuma Amiyele mwana wa Gemali.

13M'fuko la Asere, adatuma Seturi mwana wa Mikaele.

14M'fuko la Nafutali, adatuma Nabi mwana wa Vofusi.

15M'fuko la Gadi, adatuma Geuwele mwana wa Maki.

16Ameneŵa ndiwo maina a anthu amene Mose adaŵatuma kukazonda dziko. Ndipo Hoseya mwana wa Nuni, Mose adamutcha dzina loti Yoswa.

17Mose adaŵatuma kukazonda dziko la Kanani, naŵauza kuti, “Pitani cha ku Negebu, ndipo mukakwere dziko lamapirilo.

18Mukaone dzikolo kuti ndi lotani, ndipo ngati anthu am'dzikomo ngamphamvu kapena opanda mphamvu, ngati ngoŵerengeka kapena ambiri.

19Mukaone ngati dziko limene akukhalamolo ndi labwino kapena loipa, ngati mizinda imene amakhalamo ndi yamahema kapena yamalinga.

20Mukaonenso ngati dzikolo ndi lolemera kapena losauka, ndipo ngati nkhalango zilimo kapena ai. Mulimbe mtima, ndipo mukabwere ndi zipatso zina zam'dzikomo.” Imeneyo inali nyengo yopsa mphesa zoyamba.

21Choncho adapita kukazonda dzikolo kuyambira ku chipululu cha Zini mpaka ku Rehobu pafupi ndi chipata cha Hamati.

22Adadzera njira ya ku Negebu nakafika ku Hebroni, kumene kunkakhala Ahimani, Sesai ndi Talimai, zidzukulu za Aanaki. (Adamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziŵiri asanamange Zowani ku Ejipito.)

23Ndipo adafika ku chigwa cha Esikolo, nathyolako nthambi yokhala ndi tsango limodzi la mphesa, ndipo aŵiri mwa iwowo adainyamula mopika. Adatengakonso makangaza ndi nkhuyu.

24Malowo adaŵatcha chigwa cha Esikolo, chifukwa cha tsango lamphesa limene anthu aja adathyola kumeneko.

25Patapita masiku makumi anai, anthu aja adabwerako kumene adakazonda dziko kuja.

26Adabwera kwa Mose ndi Aroni ndi kwa mpingo wa Aisraele m'chipululu cha Parani ku Kadesi. Adasimbira Mose ndi Aroni ndi mpingo wonse za ulendo wao naŵaonetsa zipatso za ku dzikolo.

27Adaŵauza kuti, “Tidakafika kudziko kumene inu mudatituma. Dzikolo ndi lamwanaalirenji, zipatso zake ndi izi.

28Komatu anthu am'dzikomo ngamphamvu, mizinda yao ndi yozingidwa ndi malinga, ndiponso ndi yaikulu kwambiri. Kuwonjezera pamenepo, tidaonanso zidzukulu za Aanaki kumeneko.

29Aamaleke amakhala m'dziko lakumwera. Ahiti, Ayebusi ndi Aamori amakhala m'dziko lamapiri. Akanani amakhala m'mphepete mwa nyanja ndi m'mphepete mwa mtsinje wa Yordani.”

30Koma Kalebe adaŵakhalitsa chete anthu pamaso pa Mose, nati, “Tiyeni tipite nthaŵi yomwe ino, tikalande dzikolo, chifukwa tingathe kuligonjetsa.”

31Tsono anthu aja amene adaapita naye limodziŵa adati, “Sitingathe kukalimbana nawo anthuwo, poti ngamphamvu kopambana ife.”

32Choncho adasimbira Aisraelewo zoipa za dzikolo zimene adakaziwona, adati, “Dziko limene tidakalizondalo ndi dziko limene limaononga anthu ake. Ndipo anthu onse amene tidaŵaona kumeneko ngaataliatali.

33Gen. 6.4 Tidaonanso ziphona, (zidzukulu za Aanaki). Ifeyo tinkaoneka ngati ziwala, ndipo iwonso ankatiwona ngati ziwala.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help