Mphu. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Mwana wanga, munthu wosauka usamumane

zofunikira moyo wake,

kapena kumugwiritsa fuwa lamoto

munthu waumphaŵi.

2Usavute munthu wanjala,

kapena kumupsetsa mtima

munthu waumphaŵi.

3Munthu woŵaŵa mtima

usamuonjezere mavuto,

kapena kuchedwa kumuthandiza

pa zimene akupempha.

4Usamkanize munthu wovutika akakupempha,

kapena kufulatira munthu waumphaŵi.

5Usamapenya kumbali ukaona wosauka,

kapena kumpatsa zifukwa zoti akutemberere.

6Pakuti akakutemberera ali wovutika mu mtima,

Mlengi wake adzamva pemphero lakelo.

7Uzichita zoti anthu onse azikukonda,

ndipo uzilemekeza akuluakulu.

8Munthu wosauka akakulankhula,

umumvere,

akakupatsa moni,

uvomere mwamtendere ndi mofatsa.

9Ovutitsidwa uziŵapulumutsa kwa amene

akuŵavutitsa,

ndipo ukhale wolimba mtima pa kaweruzidwe kako.

10Kwa ana amasiye ukhale ngati bambo wao,

kwa mai wa anawo ukhale ngati mwamuna wake.

Pamenepo udzakhala ngati mwana wa Mulungu

Wopambanazonse,

ndipo Iye adzakukonda

koposa m'mene amakukondera mai wako.

Nzeru zili ngati mphunzitsi

11Nzeru zimakweza ana ake

kuti akhale omveka,

zimasamala amene amazifunafuna.

12Amene amakonda nzeru,

amakonda moyo,

amene amazidzukirira m'mamaŵa

amapata chimwemwe.

13Munthu amene amakhala nazo,

anthu adzamlemekeza,

ndipo Ambuye adzamdalitsa

kulikonse kumene adzapite.

14Amene amatumikira nzeruzo,

amatumikiranso Woyera uja.

Ambuye amaŵakonda

amene amakonda nzeruzo.

15Munthu amene amatsata nzeru,

adzaweruza anthu a mitundu ina.

Amene amazimvera,

adzakhala ndi mtendere.

16Akazikhulupirira, adzakhala nazo,

ndipo zidzukulu zake zidzakhala nazonso.

17Poyamba zidzamuperekeza pa njira zokhotakhota,

ndi kumchititsa mantha ndi nthumanzi.

Zidzamuzunza pakumutsatitsa mwambo,

mpaka zidzamukhulupirire;

ndipo zidzamuyesa ndi malamulo ake.

18Pambuyo pake zidzabweranso kwa iye

ndi kumusangalatsa,

ndipo zidzamuululira zinsinsi zake.

19Koma akasokera, zidzamusiya,

zidzalola kuti aonongeke.

Za kuchita manyazi ndi kuwopa anthu

20Uziyang'anira bwino

m'mene ziliri zonse,

ndipo uleke zoipa,

usati uzichita zokumvetsa manyazi.

21Pali manyazi ena ochimwitsa munthu,

pali manyazi enanso obweretsa ulemerero

ndi kuyanja.

22Usadzipweteke pakuchita zokondera,

usadzilakwitse pakuwopa anthu udyo.

23Usakhale chete pamene kulankhula

kukadakuthandiza,

usabise nzeru zako.

24Nzeru za munthu zimadziŵika nkulankhula kwake,

kuphunzira kwa munthu kumadziŵika ndi mau ake.

25Usamatsutsane ndi zoona,

uzikumbukira kuti ndiwe wosadziŵa zambiri.

26Usamachite manyazi kuvomera machimo ako,

usayese kukankhira m'mbuyo madzi a mtsinje.

27Usamagonjere chitsiru,

kapena kukondera anthu amphamvu.

28Uzilimbikira mpaka kufera zoona,

Ambuye adzakumenyera nkhondo.

29Usamalankhule mosaganizira bwino,

usamagwira mwamphwai ntchito zako.

30Usakhale woopsa ngati mkango m'nyumba mwako,

kapena kumazondazonda antchito ako.

31 Ntc. 20.35 Usatambalitse dzanja

kuti ulandire kanthu,

kapena kuliwumitsa

pa nthaŵi yobwezera zinthu.

Za kusadalira chuma
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help