2 Mbi. 32 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Senakeribu athira nkhondo Ayuda(2 Maf. 18.13-37; 19.14-19, 35-37; Yes. 36.1-22; 37.8-38)

1Pambuyo pake, zitatha ntchito zachikhulupirirozi, Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya, adabwera kudzathira nkhondo dziko la Yuda, ndipo adamanga zithando zankhondo kuzinga mizinda yamalinga. Ankati aŵagumule malinga akewo.

2Hezekiya ataona kuti Senakeribu wabwera, ndipo akufuna kuthira nkhondo Yerusalemu,

3adapangana ndi nduna zake pamodzi ndi atsogoleri a gulu lankhondo, kuti akatseke madzi a ku akasupe kunja kwa mzindawo. Anthuwo adamthandiza,

4ndipo anthu ambiri adasonkhana kuti atseke akasupe onse pamodzi ndi mfuleni womwe umene unkayenda m'kati mwa nthakamo. Iwo ankati, “Akafika kuno mafumu a ku Asiriya, adzapezerenji madzi ambiri?”

5Hezekiya adalimba mtima, nayamba kumanganso khoma limene linali litagamuka. Tsono adamanganso nsanja pakhomapo, ndiponso ina kunja kwake. Adalimbitsanso linga lotchedwa Milo ku mzinda wa Davide. Adapanga zida zankhondo ndi zishango zambirimbiri.

6Tsono adaika atsogoleri ankhondo kuti azilamula anthu, naŵasonkhanitsa anthuwo pa bwalo ku chipata cha mzindawo. Tsono adaŵalankhula moŵalimbitsa mtima kuti,

7“Khalani amphamvu, limbani mtima. Musati muwope kapena kutaya mtima pamaso pa mfumu ya ku Asiriya ndi chigulu chankhondo chimene ali nachochi.

8Iyeyo ali ndi gulu lankhondo la anthu, koma ife tili ndi Chauta, Mulungu wathu, wotithandiza ndi wotimenyera nkhondo zathu.” Apo anthuwo adakhulupirira mau a Hezekiya mfumu ya ku Yuda.

Mthenga wochokera kwa Senakeribu

9Pambuyo pa zimenezi Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya, amene anali atazinga mzinda wa Lakisi pamodzi ndi ankhondo ake onse, adatuma akazembe ake ku Yerusalemu kwa Hezekiya mfumu ya ku Yuda ndi kwa anthu onse a ku Yuda amene anali mu Yerusalemu. Adaŵatuma ndi mau akuti,

10“Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya, akufunsa kuti, ‘Kodi mukukhulupirira chiyani, kuti muzikanirira mu Yerusalemu ndi kumatsekedwa?

11Kodi Hezekiya sakukulakwitsani, kuti akuphetseni ndi njala ndi ludzu, pamene akukuuzani kuti, “Chauta, Mulungu wathu, adzatipulumutsa kwa mfumu ya ku Asiriya?”

12Kodi si Hezekiya yemweyu amene adachotsa akachisi ndi maguwa ku mapiri, nalamula anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu kuti, “Muzipembedza ku guwa limodzi lokha ndipo muzipereka nsembe zanu zopsereza pa guwa limodzi lokhalo?”

13Kodi inu simukudziŵa zimene ine ndi makolo anga takhala tikuichita mitundu yonse ya anthu a maiko ena? Kodi milungu ya mitundu ina ya anthu a m'maikowo idatha kupulumutsa maiko ao m'manja mwanga?

14Kodi pakati pa milungu ya mitundu ina ya anthuyo, imene makolo anga adaiwononga kotheratu, ndi uti amene adatha kupulumutsa anthu ake m'manja mwanga, kuti inuyo muziti Mulungu wanu adzakupulumutsani m'manja mwanga?

15Ndiye inutu tsono, musalole kuti Hezekiya akunyengeni kapena kukusokezani motero ai, ndipo musamkhulupirire. Chifukwa palibe mulungu wa mtundu kapena ufumu wina uliwonse amene adatha kuŵapulumutsa anthu ake m'manja mwanga kapena m'manja mwa makolo anga. Mulungu wanuyo sadzatha kukupulumutsani m'manja mwanga ai.’ ”

16Akazembe akewo ankalankhula zambiri zonyoza Ambuye Chauta ndi mtumiki wake Hezekiya.

17Kenaka Senakeribu adalemba makalata achipongwe oputa Chauta, Mulungu wa Aisraele, adati, “Monga milungu ya mitundu ina ya anthu a m'maiko ena sidathe kuŵapulumutsa anthu ao m'manja mwanga, momwemonso Mulungu wa Hezekiya sadzatha kupulumutsa anthu ake m'manja mwanga.”

18Ndipo anthuwo mofuula adalengeza zimenezi m'chilankhulo cha Chiyuda kwa anthu a mu Yerusalemu amene anali pa khoma, kuti aŵachititse mantha ndi kuŵaopsa, ndi cholinga choti alande mzindawo.

19Ankalankhula za Mulungu wa ku Yerusalemu monga momwe ankalankhulira za milungu ya mitundu ina ya anthu a pa dziko lapansi, imene ili milungu yopangidwa ndi manja a anthu.

20Pamenepo mfumu Hezekiya pamodzi ndi mneneri Yesaya mwana wa Amozi, adayamba kupemphera, nafuulira kumwamba.

21Tsono Chauta adatuma mngelo, ndipo iye adadzapha ankhondo onse amphamvu, atsogoleri ndi akulu a ku zithando za mfumu ya ku Asiriya. Choncho Senakeribu adabwerera kumapita ku dziko la kwao ali ndi nkhope yamanyazi. Ndipo atakaloŵa m'nyumba ya Chauta wake, ana ake ena adamupha momwemo ndi lupanga.

22Choncho Chauta adapulumutsa Hezekiya, pamodzi ndi anthu onse amene ankakhala mu Yerusalemu, kwa Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya, ndiponso kwa adani ao onse. Motero Chautayo ankaŵatchinjiriza anthuwo konsekonse.

23Tsono anthu ambiri adabwera ndi zopereka kwa Chauta ku Yerusalemu, nadzaperekanso mphatso kwa Hezekiya mfumu ya ku Yuda. Zitachitika zimenezo, Hezekiyayo adakhala wolemekezeka kwambiri pamaso pa mitundu yonse ya anthu, kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka m'tsogolo.

Kudwala kwa Hezekiya ndi ntchito zake(2 Maf. 20.1-3, 12-19; Yes. 38.1-3; 39.1-8)

24Pa nthaŵi imeneyo Hezekiya adadwala, ndipo anali pafupi kufa, tsono adapemphera kwa Chauta, ndipo Chautayo adamuyankha, nampatsa chizindikiro chakuti adzachira.

25Koma Hezekiya sadachite molingana ndi zabwino zimene Chauta adaamchitira, poti mtima wake unali wodzitama. Nchifukwa chake mkwiyo wa Chauta udamugwera iyeyo, ndiponso anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu.

26Koma kenaka Hezekiya adadzichepetsa naleka kudzikuza, iyeyo ndi anthu amene ankakhala mu Yerusalemu. Motero mkwiyo wa Chauta sudagwe pa anthuwo pa masiku a Hezekiya.

Chuma chake ndi ulemerero wake wa Hezekiya

27Hezekiya anali wolemera kwambiri ndiponso waulemu zedi. Tsono adadzimangira nyumba zomasungiramo chuma cha siliva, golide, miyala yamtengowapatali, zonunkhira, zishango ndiponso mitundu yonse ya ziŵiya zamtengowapatali.

28Adamanganso nyumba zosungiramo tirigu, vinyo ndi mafuta. Adamanga makola a mitundu yonse ya ziŵeto zosiyanasiyana ndi makola a nkhosa.

29Komanso adamanga mizinda yake, ndipo anali ndi nkhosa ndi ng'ombe zambirimbiri, pakuti Mulungu adaamlemeza kwambiri.

30Hezekiyayu ndiye amene adaatseka ngalande yakumtunda ya madzi a ku Gihoni, nkuŵaongolera kuti atsikire kuzambwe kwa mzinda wa Davide. Ankakhoza pa ntchito zonse zimene ankachita.

31Choncho pamene amithenga a nduna za ku Babiloni adatumidwa kwa Hezekiya kuti akafunse za chizindikiro chija chimene chidachitika m'dzikomo, Mulungu adamsiya yekha, kuti amuyese ndipo kuti adziŵe zonse za mumtima mwake.

Kutha kwa ufumu wa Hezekiya(2 Maf. 20.20-21)

32Tsono ntchito zonse za Hezekiya, pamodzi ndi zabwino zimene ankachita, zidalembedwa m'nkhani yosimba za zimene Yesaya mneneri mwana wa Amozi adaziwona m'masomphenya. Nkhani imeneyi idalembedwa m'buku la mafumu a ku Yuda ndi a ku Israele.

33Hezekiya adamwalira, naikidwa ku chikwera ku manda a ana a Davide. Anthu onse a ku Yuda pamodzi ndi a mu Yerusalemu adamchitira ulemu pa maliro ake. Tsono Manase mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help