Eks. 25 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zopereka zomangira chihema choyera(Eks. 35.4-9)

1Chauta adauza Mose kuti,

2“Uza Aisraele apereke zopereka zao kwa Ine. Tsono iwe ulandire zoperekazo kwa munthu aliyense wa mtima wofuna kupereka.

3Zopereka zimene ulandirezo ndi izi: golide, siliva, mkuŵa,

4nsalu zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira, nsalu zokoma zathonje, nsalu zopangidwa ndi ubweya wambuzi,

5zikopa zankhosa zonyika mu utoto wofiira, zikopa zofeŵa, matabwa a mtengo wa kasiya,

6mafuta a nyale, zonunkhira za mafuta odzozera, ndiponso lubani wa fungo lokoma.

7Ulandirenso miyala yokoma ya onikisi, ndiponso miyala ina yoti uike pa chovala chaunsembe cha efodi, ndi pa chovala chapachifuwa.

8Ndipo andipangire chihema chopatulika kuti Ine ndidzakhale pakati pao.

9Umange chihemacho monga m'mene ndidzakulangizire mapangidwe ake ndiponso mapangidwe a katundu yense wam'menemo.

Za bokosi lachipangano(Eks. 7.1-9)

10“Ndipo apange bokosi la matabwa a mtengo wa kasiya. Kutalika kwake kukhale masentimita 114, muufupi mwake masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69.

11Ulikute ndi golide wabwino kwambiri m'kati mwake ndi kunja komwe. Upange mkombero wagolide kuzungulira bokosi lonselo.

12Upange mphete zinai zagolide zonyamulira bokosilo, ndi kumangirira mphetezo ku miyendo yake inai, uku ziŵiri uku ziŵiri.

13Upangenso mphiko zakasiya, ndipo mphikozo uzikute ndi golide.

14Mphiko zimenezo udzazilonge m'mphetezo pa mbali ziŵiri za bokosilo, kuti azinyamulira.

15Mphikozo zidzangokhala m'mphetezo osazitulutsanso.

16M'bokosimo udzaikemo miyala iŵiri yolembedwapo Malamulo imene ndidzakupatse.

17 Ahe. 9.5 “Upange ndi golide wabwino kwambiri chivundikiro cha bokosi, kutalika kwake masentimita 114, kupingasa kwake masentimita 69.

18Pa mbali ziŵiri za chivundikirocho, m'mphepete mwake, upange akerubi aŵiri, agolide, osula ndi nyundo,

19wina uku wina uku. Akerubiwo uŵalumikize ndi chivundikiro.

20Mapiko a akerubiwo adzatambasukire pamwamba pa chivundikirocho, kuti adzachiphimbe. Akerubi adzakhale choyang'anana, aliyense kumayang'ana chivundikirocho.

21Chivundikiro cha bokosicho udzachiike pamwamba pa bokosilo, ndipo m'bokosimo udzaikemo miyala iŵiri ija ya Malamulo imene ndidzakupatse.

22Ndizidzakumana nawe kumeneko, ndipo kuchokera pamwamba pa chivundikirocho, pakati pa akerubi ali pamwamba pa bokosiwo, ndidzakuuza malamulo okhudza anthu anga Aisraele.

Tebulo la buledi woperekedwa kwa Mulungu(Eks. 37.10-16)

23“Upange tebulo la matabwa a mtengo wa kasiya, kutalika kwake masentimita 91, muufupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69.

24Tsono ulikute ndi golide wabwino kwambiri ndipo pozungulira pake ponse upange mkombero wagolide.

25Upange fulemu lozungulira tebulo, muufupi mwake kuyesa chikhatho, ndipo upange mkombero wagolide wozungulira fulemulo.

26Upange mphete zinai zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya zinai za ku miyendo yake inai.

27Mphete zopisamo mphiko zonyamulira tebulolo ziikidwe pafupi ndi fulemu lija.

28Upange mphiko zonyamulira za mtengo wa kasiya, ndipo uzikute ndi golide.

29Upange mbale ndi zipande zofunika popereka lubani, ndiponso mitsuko ndi mabeseni ofunika pa zopereka za chakumwa. Zonsezi zikhale za golide wabwino kwambiri.

30Lev. 24.5-8 Patebulopo uziikapo buledi woperekedwa kosalekeza, kuti azikhala pamaso panga nthaŵi zonse.

Choikaponyale(Eks. 37.17-24)

31“Upange choikaponyale cha golide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi thunthu lake zikhale zagolide, ndipo uchisule ndi nyundo. Zikho zake, ndiye kuti nkhunje ndi maluŵa ake, zonsezo zipangidwire kumodzi.

32Pa mbali zake pakhale mphanda zisanu ndi imodzi, zitatu pa mbali iliyonse.

33Mphanda yoyamba ikhale ndi zikho zitatu zopangidwa ngati maluŵa amtowo, nkhunje ndi duŵa. Ku mphanda ina kukhalenso zikho zitatu zonga maluŵa amtowo, nkhunje ndi duŵa. Zikhale momwemo mphanda zonse zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikaponyalecho.

34Pa choikaponyalecho padzakhale maluŵa anai a maonekedwe onga maluŵa amtowo, okhala ndi nkhunje ndi maluŵa ake.

35Padzakhale nkhunje imodzi m'munsi mwake mwa magulu atatu a mphanda zija, utazipatula ziŵiriziŵiri.

36Nkhunjezo pamodzi ndi mphandazo zidzapangidwire kumodzi ndi choikaponyalecho. Chonsecho chidzangokhala chimodzi, chopangidwa ndi golide, chosula ndi nyundo.

37Upange nyale zisanu ndi ziŵiri, ndipo uziike pa choikaponyale chija, kuti ziziwunikira kutsogolo.

38Mbano zogwirira, pamodzi ndi timbale take tomwe, zikhale za golide wabwino kwambiri.

39Choikaponyalecho ndi zipangizo zonse uzipange ndi golide wolemera makilogaramu 34.

40Ntc. 7.44; Ahe. 8.5 Usamale kuti upange zimenezi monga momwe ndikukuwonetsera paphiri pano.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help