1Ndikupereka m'manja mwanu Febe, mlongo wathu, amene ali mtumiki wa mpingo wa ku Kenkrea.
2Mlandireni m'dzina la Ambuye, monga momwe anthu a Mulungu ayenera kulandirirana. Mumthandize monga momwe angasoŵere chithandizo chanu, pakuti iyeyo adathandiza anthu ambiri, ine ndemwenso adandithandizako.
3 anzanga otumikira Khristu Yesu.
4Iwoŵa anali okonzeka kuphedwa kuti apulumutse moyo wanga. Si ndine ndekhatu ndikuŵathokoza, komanso mipingo yonse ya ku maiko a anthu a mitundu ina.
5Mundiperekerenso moni kwa anthu amene amasonkhana ngati ampingo m'nyumba mwao.
Moni kwa Epeneto, bwenzi langa lapamtima, amene ndi woyamba mu Asiya kukhulupirira Khristu.
6Moni kwa Maria, amene wakhala akukugwirirani ntchito kolimba.
7Moni kwa Androniko ndi Yunia, Ayuda anzanga amene anali nane m'ndende. Iwoŵa ndi otchuka pakati pa atumwi, ndipo ndi ine ndi iwowo adayambira ndiwo kukhala akhristu.
8Moni kwa Ampiliato, bwenzi langa lokondedwa mwa Ambuye.
9Moni kwa Urbano, mtumiki mnzathu pa ntchito ya Khristu, ndiponso kwa Stakisi, amene ndimamkonda.
10Moni kwa Apelesi, mkhristu wolimba uja. Moni kwa a m'banja la Aristobulo.
11Moni kwa Herodiono, Myuda mnzanga. Moni kwa akhristu a m'banja la Narkiso.
12Moni kwa Trifena ndi Trifosa, amene amagwira mwamphamvu ntchito ya Ambuye. Moni kwa Perisi, wokondedwa uja, amene wachita zambiri pogwirira Ambuye ntchito.
13 wotchuka pa ntchito ya Ambuye. Moninso kwa mai wake amene ali ngati mai wanganso.
14Moni kwa Asinkrito, Filegoni, Heremesi, Patrobasi, Herimasi ndi abale onse amene ali nawo pamodzi.
15Moni kwa Filologo ndi Juliya, kwa Nereo ndi mlongo wake, kwa Olimpasi ndi kwa anthu onse a Mulungu amene ali nawo pamodzi.
16Mupatsane moni mwa chikondi choona. Mipingo yonse yachikhristu ikukupatsani moni.
Malangizo otsiriza17Ndikukupemphani abale, chenjera nawoni anthu amene amapatutsa anzao naŵachimwitsa. Iwo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene inu mudaphunzira. Muziŵalewa,
18pakuti anthu otere satumikira Khristu Ambuye athu, koma amangotumikira zilakolako zao basi. Ndi mau okoma ndi oshashalika amanyenga anthu a mitima yoona.
19Anthu onse adaimva mbiri ya kumvera kwanu. Tsono ine ndikunyadira inuyo, koma ndifuna kuti mukhale anzeru pa zabwino, ndi othaŵa zoipa.
20Ndipo Mulungu amene amapatsa mtendere, posachedwa adzatswanya Satana pansi pa mapazi anu.
Ambuye athu Yesu Khristu akudalitseni.
21 mnzanga wogwira naye ntchito, akukupatsani moni. Lusio, Yasoni ndi Sosipatere, Ayuda anzanga, nawonso akuti moni.
22Ine Tersio, mlembi chabe wa kalatayi, ndikuti moni, inu abale mwa Ambuye.
23Ntc. 19.29; 1Ako. 1.14; 2Tim. 4.20Akukupatsani moni Gayo, amene akundisamala ine pamodzi ndi mpingo wonse kunyumba kwake. Akukupatsani moni Erasito, msungachuma wa mzinda wonse, ndiponso Kwarto, mbale wathu.
[
24Ambuye athu Yesu Khristu akudalitseni nonse. Amen.]
Mulungu alemekezeke25Tiyeni tilemekeze Mulungu! Iye ali ndi mphamvu za kukulimbitsani potsata Uthenga Wabwino umene ndimaulalika, umene ndi mau olengeza za Yesu Khristu. Zimenezi zinali zachinsinsi, ndipo zidaabisika pa zaka zonse kuyambira kalekale.
26Koma tsopano zatulukira poyera kudzera m'zimene aneneri adalemba, ndiponso kudzera m'lamulo la Mulungu wachikhalire zadziŵika kwa anthu a mitundu yonse, kuti azizikhulupirira ndi kuzimvera.
27Kwa Mulungu, amene ndiye yekha wanzeru, kukhale ulemerero mwa Yesu Khristu mpaka muyaya. Amen.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.