1Patapita kanthaŵi, pa nyengo yodula tirigu, Samisoni adapita kukacheza kwa mkazi wake, atatenga mwanawambuzi. Ndipo adati, “Ndikufuna kukaloŵa m'chipinda cha mkazi wanga.” Koma bambo wake wa mkaziyo adamkaniza kuloŵa.
2Bamboyo adamuuza kuti, “Ine ndidaatsimikiza kuti mukudana naye kwambiri mkaziyu. Choncho ndidamkwatitsa kwa mnzanu uja. Kodi mng'ono wake si wokongola kupambana iyeyu? Pepani ndithu, ingotengani ameneyu m'malo mwake.”
3Samisoni adaŵauza kuti, “Ulendo uno aliyense asandinene, ndikaŵachita choipa chachikulu Afilistiŵa.”
4Motero Samisoni adakagwira nkhandwe mazana atatu nazimangirira michira ziŵiriziŵiri. Kenaka pa mfundo iliyonse ya michirayo adamangirirapo nsakali naziyatsa.
5Atayatsa nsakalizo, adazitaya nkhandwezo kuti zipite m'minda yatirigu ya Afilisti. Popitapo zidakatentha milu ya tirigu ndi tirigu wosadula yemwe, pamodzi ndi mitengo ya olivi.
6Tsono Afilisti adayamba kufunsana kuti, “Ndani wachita zimenezi?” Ena adayankha kuti, “Ndi Samisoni, mkamwini wa Mtimuna uja, amene wachita zimenezi, chifukwa chakuti Mtimunayo watenga mkazi wa Samisoni kumkwatitsa kwa mnzake.” Tsono Afilisti adabwera namtentha mkaziyo pamodzi ndi bambo wake yemwe.
7Atamva zimenezi Samisoni adati, “Ngati zimenezi nzimene mumachita, ndikulumbira kuti sindileka mpaka nditakulipsirani.”
8Tsono adamenyana nawo koopsa napha anthu ambiri. Kenaka adakaloŵa ku phanga la ku Etamu, nakhala komweko.
Samisoni agonjetsa Afilisti.9Pambuyo pake Afilisti adadzamanga zithando zao zankhondo m'dziko la Yuda, ndipo adathira nkhondo pa Lehi.
10Anthu a ku Yuda adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwadzamenyana nafe?” Iwowo adayankha kuti, “Tabwera kudzamanga Samisoni kuti timchite zomwe iye adatichita ife.”
11Tsono anthu 3,000 a ku Yuda adapita ku phanga la ku Etamu, namufunsa Samisoni kuti, “Kodi sukudziŵa kuti Afilisti ndiwo amene amatilamulira? Nanga izi watichitazi nzotani?” Iye adaŵayankha kuti, “Ndaŵachita zomwe iwowo adandichita ine.”
12Tsono iwowo adamuuza kuti, “Tabwera kudzakumanga kuti tikakupereke kwa Afilisti.” Samisoni adaŵauza kuti, “Lonjezeni molumbira kuti simundipha ndi inuyo.”
13Iwo adamuuza kuti, “Iyai. Ife tingokumanga chabe nkukakupereka kwa iwowo. Sitikupha ai.” Choncho adammanga ndi zingwe ziŵiri zatsopano, namtulutsa m'phanga muja.
14Samisoni atafika ku Lehi, Afilisti adabwera akufuula kudzamchingamira. Pompo Mzimu wa Chauta udamtsikira mwamphamvu, ndipo zingwe zimene adammanga nazo zija zidasanduka ngati thonje logwira moto, zidachita ngati kusungunuka nkuchoka m'manja mwake.
15Tsono adapeza chibwano cha bulu amene anali atafa chatsopano. Adachitola, naphera nacho anthu chikwi chimodzi.
16Apo Samisoni adayamba kuimba nyimbo yakuti,
“Ndi chibwano cha bulu, milu ndi milu ya anthu!
Ndi chibwano cha bulu, ndapha anthu chikwi chimodzi!”
17Pambuyo pake, adachitaya pansi chibwano chija, ndipo malowo adatchedwa Ramatilehi.
18Tsono Samisoni adamva ludzu kwambiri ndipo adatana Chauta mopemba nati, “Inu mwapereka chipulumutso chachikulu choterechi kudzera mwa ine mtumiki wanu. Kodi tsopano ndife ndi ludzu ndi kugwidwa ndi anthu osaumbalidwaŵa?”
19Pamenepo Mulungu adang'amba nthaka ku Lehi, ndipo madzi adatuluka m'dzenjemo. Samisoni atamwa madziwo, mphamvu zake zidabwereramo, ndipo adatsitsimuka. Nchifukwa chake malowo adatchedwa Enihakore. Malowo ali ku Lehi mpaka pano.
20Samisoni adatsogolera Aisraele pa nthaŵi ya Afilisti zaka makumi aŵiri.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.