Ntc. 22 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1“Inu abale anga ndi inu akuluakulu, mvereni ndiyankhe tsopano zimene akundinenezazi.”

2Pamene iwo adamumva akulankhula nawo pa Chiyuda, adakhala chete kopambana. Tsono Paulo anati,

3, ndipo umve mau ake olankhula nawe.

15Pakuti udzamchitira umboni kwa anthu onse pa zimene waziwona ndi kuzimva.

16Nanga tsono ukuchedweranji? Dzuka ndi kutama dzina lake mopemba, ubatizidwe ndi kusambitsidwa kuti machimo ako achoke.’ ”

Ambuye atuma Paulo kwa anthu a mitundu ina

17“Tsono ndidabwerera ku Yerusalemu, ndipo pamene ndinkapemphera m'Nyumba ya Mulungu, ndidachita ngati ndakomoka.

18Ndidaona Ambuye akundiwuza kuti, ‘Fulumira, tuluka msangamsanga m'Yerusalemu muno, chifukwa anthuŵa sadzauvomera umboni wako wonena za Ine.’

19Ine ndidati, ‘Zoonadi Ambuye, chifukwa iwo omwe akudziŵa kuti ine ndinkapita ku nyumba iliyonse yamapemphero kukaŵagwira ndi kuŵaponya m'ndende, nkumaŵakwapula onse okhulupirira Inu.

20Ntc. 7.58Pamene ankapha Stefano, mboni yanu, inenso ndinali pomwepo. Ndinkavomerezana nawo, ndipo ndinkasunga ndine zovala za amene ankamuphawo.’

21Apo Ambuye adandiwuza kuti, ‘Nyamuka, chifukwa Ine ndidzakutuma kutali kwa anthu a mitundu ina.’ ”

Mkulu wa asilikali auzidwa kuti Paulo ndi mfulu yachiroma

22Mpaka apa anthu aja ankamvetsera bwinobwino mau a Paulo. Koma pamene adadzatchula mau otsirizaŵa, iwo adayamba kufuula kuti, “Munthu wotere koma kungokonzeratu. Sayeneranso kukhala moyo.”

23Iwowo ankafuula nkumazunguza malaya ao, namawaza fumbi kumwamba.

24Nthaŵi yomweyo mkulu wa asilikali uja adalamula kuti aloŵe naye Paulo m'linga la asilikali lija. Adaŵauza kuti amkwapule, kuti iyeyo aulule chifukwa chimene anthu aja ankamukuwizira chotere.

25Pamenepo padaaimirira mtsogoleri wa gulu la asilikali 100. Tsono asilikali ake atamanga Paulo kuti amkwapule, Pauloyo adafunsa kuti, “Kodi malamulo anu amalola kukwapula mfulu yachiroma musanazenge nkomwe mlandu wake?”

26Pamene mtsogoleriyo adamva zimenezi, adapita kwa mkulu wa asilikali uja namufunsa kuti, “Kodi inu mukuti mutani? Munthu ujatu ndi mfulu yachiroma.”

27Apo mkuloyo adadzafunsa Paulo kuti, “Kodi ati iwe ndiwe mfulu yachiroma?” Iye adati, “Inde.”

28Tsono mkulu uja adamuuza kuti, “Ine ndidachita chogula ufulu wangawu ndi ndalama zambiri.” Paulo adati, “Koma ine wangawu ndidachita chobadwa nawo.”

29Pompo asilikali aja amene adaati afunse Paulo mafunso, adamleka. Mkulu ujanso adachita mantha atazindikira kuti adaamanga munthu amene ali mfulu yachiroma.

Paulo ku Bwalo Lalikulu lamilandu la Ayuda

30Mkulu wa asilikali uja adaafuna kudziŵa kwenikweni chifukwa chimene Ayuda adaadzanenezera Paulo. Choncho m'maŵa mwake adammasula, nalamula kuti akulu a ansembe ndi onse a pa Bwalo Lalikulu lamilandu la Ayuda asonkhane. Kenaka adabwera ndi Paulo namuimika pakati pao.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help