1 2Maf. 22.1—23.30; 2Mbi. 34.1—35.27 Pa nthaŵi ya Yosiya, mwana wa Amoni, mfumu ya ku Yuda, Chauta adamupatsa uthenga Zefaniya, mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya.
Za tsiku limene Chauta adzalange anthu2Chauta adati,
“Ndidzafafaniziratu
zonse za pa dziko lapansi.”
3“Ndidzafafaniziratu anthu ndi nyama zomwe.
Ndidzaononga mbalame zamumlengalenga
ndi nsomba zam'nyanja.
Ndidzagwetsa anthu ochimwa.
Ndidzafafaniziratu mtundu wa anthu
kuti usaonekenso pa dziko lapansi,”
akuterotu Chauta.
4“Ndidzasamula dzanja langa
kuti ndilange anthu a m'dera la Yuda
ndi onse okhala ku Yerusalemu.
Ndidzafafaniziratu zotsalira zonse za
Baala pa malo ano.
Palibe aliyense
amene adzakumbukirenso ansembe a fanolo.
5Ndidzafafanizanso amene amaŵerama pa
madenga ao nkumapembedza dzuŵa, mwezi ndi nyenyezi.
Ndidzaononganso amene amati kwinaku
akulambira Chauta ndi kulumbira m'dzina lake,
kwinaku nkumalumbira m'dzina la Milikomu.
6Iwowo adafulatira Chauta osamtsatanso,
safuna kupembedza Chauta,
kapena kumpempha nzeru.”
7Khalani chete pamaso pa Ambuye Chauta!
Tsikutu la Chauta layandikira.
Chauta wakonza kuti
anthu ake adzaperekedwe ngati nsembe,
ndipo wapatuliratu oitanidwa odzapereka nsembeyo.
8Chauta akuti,
“Pa tsiku limenelo la nsembe yanga
ndidzalanga ana a mfumu ndi akalonga ake,
ndi onse otengera zachilendo.
9Pa tsiku limenelo ndidzalanga onse
olumpha pa chiwundo,
ndiponso amene amachita zankhanza ndi
zonyenga zambiri.”
10Chauta akunena kuti,
“Pa tsiku limenelo kulira kwakukulu
kudzamveka ku Chipata cha Msika wa Nsomba;
kulira kwakukuluko kudzamveka ku chigawo
cham'kati cha mzinda wa Yerusalemu;
kudzamvekanso kugunda kuchokera ku mapiri.
11Inu okhala ku chigwa cha mzinda
lirani komvetsa chisoni,
chifukwa amalonda onse atha,
onse ogulitsa siliva aonongeka.
12Pa nthaŵi imeneyo ndidzafufuzafufuza
mu Yerusalemu ndi nyale,
ndipo ndidzaŵalanga anthu
ongokhala khale ngati vinyo wosakhutchumula,
amene mumtima mwao amati,
‘Chauta sadzachitapo chabwino,
kapena kuchitapo choipa.’
13Anthu otereŵa chuma chao adani adzachifunkha,
nyumba zao adzaziphwasula.
Adzamanga nyumba, koma sadzakhalamo.
Adzabzala mphesa, koma sadzamwa vinyo wake.”
14Tsiku lalikulu la Chauta lili pafupi,
layandikira ndipo likudza mofulumira.
Tsikulo kubwera kwake nkopweteka,
ngakhale ankhondo amphamvu omwe akulira pamenepo.
15Tsikulo lidzakhala tsiku la mkwiyo wa Chauta,
tsiku la mavuto ndi mazunzo,
tsiku la kuwonongeka ndi kupasuka kwa zinthu,
tsiku la mdima ndi chisoni,
tsiku la mitambo ndi labii kuda.
16Tsiku limenelo kudzamveka lipenga
ndi kufuula kwankhondo,
kwa asilikali othira nkhondo mizinda ya malinga
ndiponso nsanja zankhondo za Yerusalemu.
17Chauta akuti,
“Chifukwa anthuwo adandichimwira,
ndidzaŵasautsa koopsa,
kotero kuti azidzayenda ngati akhungu.
Magazi ao adzachita kuti mwaa ngati fumbi,
matupi adzangoti vuu, nkumaola ngati ndoŵe.
18Ngakhale siliva wao kapena golide wao
sadzatha kuŵaombola,
tsiku la mkwiyo wa Chautalo.
Ukali wake wotentha ngati moto,
udzapsereza dziko lonse,
ndipo mwadzidzidzi adzathetsa onse okhala m'menemo.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.