1 Ntc. 11.30; 15.2 Pambuyo pake, patapita zaka khumi ndi zinai, ndidapitanso ku Yerusalemu pamodzi ndi Barnabasi. Ndidatenganso Tito kuti apite nafe.
2Ndidapita kumeneko chifukwa Mulungu adaachita kundiwululira kuti ndipite. Mu msonkhano wa atsogoleri okhaokha ndidaŵafotokozera Uthenga Wabwino umene ndimalalika pakati pa anthu osakhala Ayuda. Ndidachita zimenezi kuwopa kuti ntchito imene ndikuchitayi, ndiponso imene ndidachita kale, ingakhale yachabe.
3Koma mnzanga uja, Tito, ngakhale ndi Mgriki, sadamkakamize kuti aumbalidwe,
4ngakhale kuti anthu ena adaafuna kuti iyeyu aumbalidwe ndithu. Anthu ameneŵa adaabwera modzizimbayitsa ngati abale athu. Iwowo adangodzaloŵa ngati azondi kuti adzaone ufulu wathu umene tili nawo mwa Khristu Yesu. Ankafuna kutisandutsa akapolo.
5Sitidaŵagonjere mpang'ono pomwe, popeza kuti tinkafuna kukusungirani kwathunthu zoona za Uthenga Wabwino.
6 Deut. 10.17 Koma kunena za aja ankaŵayesa atsogoleriŵa, (kaya analidi atsogoleri kaya, ndilibe nazo kanthu. Mulungu sakondera paja), iwowo sadaonjeze kanthu kena koti ndilalike.
7Makamaka adaaona kuti Mulungu adandipatsa ine ntchito ya kulalika Uthenga Wabwino kwa anthu osakhala Ayuda, monga momwe adapatsira Petro ntchito ya kuulalika kwa Ayuda.
8Pakuti Mulungu yemweyo amene adagwira ntchito mwa Petro pomutuma ngati mtumwi kwa Ayuda, adagwiranso ntchito mwa ine, pondituma ngati mtumwi kwa anthu a mitundu ina.
9Yakobe, Petro ndi Yohane, amene anthu ankaŵaona kuti ndi mizati mu Mpingo, adazindikira kuti ineyo Mulungu adandipatsadi ntchito imeneyi. Motero adagwirana chanza ndi ine ndiponso ndi Barnabasi, kutsimikiza chiyanjano chathu. Ndipo tidavomerezana kuti ine ndi Barnabasi tipite kwa anthu a mitundu ina, iwowo apite kwa Ayuda.
10Adangopempha chokhachi kuti tisaleke kukumbukira anthu ao aumphaŵi. Ndipotu chimenechi ndicho ndakhala ndikuchita moikapo mtima.
Paulo adzudzula Petro ku Antiokeya11Koma pamene Petro adafika ku Antiokeya, ndidamtsutsa poyera, chifukwa adaapezeka wolakwadi.
12Pakuti asanafike anthu ena amene Yakobe adaaŵatuma, iye ankadya pamodzi ndi abale osakhala Ayuda. Koma atafika iwowo, iye adayamba kudzipatula, osafuna kudya nawonso, chifukwa choopa anthu amene ankafuna kuti omwe sali Ayuda aumbalidwe.
13Abale ena onse ochokera ku Chiyuda nawonso adayamba kuchita chiphamaso, kotero kuti ngakhale Barnabasi yemwe adaatengeka nacho chiphamaso chaocho.
14Ine ndidaaona kuti iwo sakuyenda molunjika, sakutsata choona cha Uthenga Wabwino. Tsono ndidauza Petro pamaso pa onse kuti, “Iwe ndiwe Myuda, komabe ukukhala ngati munthu wa mtundu wina, osati Myuda. Nanga ungakakamize bwanji anthu a mitundu ina kukhala ngati Ayuda?”
Ayuda ndi akunja amapulumuka ndi chikhulupiriro15Ife ndife a mtundu wa Ayuda, osati anthu aja amati akunja ochimwa.
16Mas. 143.2; Aro. 3.20; Aro. 3.22Komabe tikudziŵa kuti munthu sangapezeke kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakuchita ntchito zolamulidwa ndi Malamulo, koma pakukhulupirira Yesu Khristu. Ifenso tidakhulupirira Khristu Yesu kuti tisanduke olungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira Khristu, osati chifukwa cha ntchito zolamulidwa ndi Malamulo. Pakuti palibe munthu amene angapezeke kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu chifukwa cha ntchito zolamulidwa ndi Malamulo.
17Tsono ngati ifeyo, poyesetsa kusanduka olungama mwa Khristu, tikupezeka kuti ndifenso ochimwa, kodi pamenepo ndiye kuti Khristu ndi wotumikira uchimo? Mpang'ono pomwe.
18Ngati ndimanganso zomwezo zimene ndidaagamula, pamenepo kukuwonekeratu kuti ndine wopalamula.
19Malamulo ndiwo adandizindikiritsa kuti ndiyenera kulekeratu kuŵadalira Malamulowo, ndipo kuti moyo wanga wonse uyenera kukhala wodalira Mulungu mwini.
20Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
21Sindiisandutsa yopandapake mphatso yaulere ya Mulungu. Pakuti ngati munthu atha kusanduka wolungama pamaso pa Mulungu pakutsata Malamulo, ndiye kuti Khristu adafa pachabe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.