1Miriyamu ndi Aroni adayamba kumnena Mose chifukwa cha mkazi wachikusi amene Moseyo adamkwatira, poti adakwatiradi mkazi wa ku Kusi.
2Iwowo adafunsa kuti, “Kodi nzoona kuti Chauta adalankhula kudzera mwa Mose yekha? Kodi sadalankhulenso kudzera mwa ife?” Chauta adazimva zimenezo.
3Mphu. 45.4Koma Mose anali munthu wofatsa kupambana anthu onse a pa dziko lapansi.
4Tsono Chauta adauza Mose, Aroni ndi Miriyamu kuti, “Atatu nonsenu mubwere ku chihema chamsonkhano.” Ndipo onse atatuwo adapitadi.
5Chauta adatsika mu mtambo, naima pakhomo pa hema, ndipo adaitana Aroni ndi Miriyamu, tsono aŵiri onsewo adabweradi.
6Chauta adati, “Imvani mau anga. Pakakhala mneneri pakati panupa, Ine Chauta ndimadziwonetsa kwa munthuyo m'masomphenya, ndimalankhula naye m'maloto.
7Ahe. 3.2 Koma sinditero ndi mtumiki wanga Mose, amene wakhala woyang'anira anthu anga onse a Israeli.
8Ndimalankhula naye pakamwampakamwa, momveka osati mophiphiritsa, ndipo amaona ulemerero wanga. Chifukwa chiyani tsono simudaope kumnena Mose, mtumiki wanga?”
9Pamenepo Chauta adaŵakwiyira, nachokapo.
10Mtambo utachoka pamwamba pa chihema, Miriyamu adapezeka ali ndi khate lambuu ngati ufa, ndipo Aroni atacheuka, adangoona Miriyamu ali ndi khate.
11Apo Aroni adauza Mose kuti, “Mbuyanga, musatilange chifukwa choti tachimwa, ndipo tachita zopusa.
12Musalole kuti Miriyamu akhale ngati mwana wobadwa wakufa, amene thupi lake lili loonongeka kumodzi.”
13Tsono mokweza mau Mose adauza Chauta kuti, “Mulungu ndikukupemphani kuti mumchiritse Miriyamu.”
14Num. 5.2, 3 Koma Chauta adauza Mose kuti, “Bambo wake akadamthira malovu kumaso, kodi Miriyamu sakadachita manyazi masiku asanu ndi aŵiri? Basi, amtsekere kunja kwa mahema masiku asanu ndi aŵiri, ndipo pambuyo pake angathe kumloŵetsanso.”
15Choncho adamtsekera Miriyamu kunja kwa mahema masiku asanu ndi aŵiri. Ndipo anthu sadathe kunyamuka ulendo wao mpaka Miriyamu atamloŵetsanso.
16Pambuyo pake anthu aja adanyamuka ku Hazeroti nakamanga mahema ao ku chipululu cha Parani.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.