Ezek. 7 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chimalizo chili pafupi

1Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,

2“Iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Chauta ndikuuza dziko la Israele kuti chimalizo chili pafupi. Chimalizo chafika ku mbali zonse zinai za dziko.

3Tsopano chimalizo chili pa iwe Israele. Mkwiyo wanga ndidzauthira pa iwe. Ndidzagamula mlandu wako potsata mayendedwe ako, ndipo ndidzakulanga chifukwa cha zonyansa zako.

4Sindidzakumvera chifundo kapena kukuleka. Ndidzakulanga chifukwa cha machitidwe ako ndiponso chifukwa cha zonyansa zimene zili pakati pako. Pamenepo udzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.

5“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Chiwonongeko chikubwera, chiwonongeko chotsatana nchinzake.

6Chimalizo chafika, chimalizo chija chafika! Chakugwera, ndithu chabwera.

7Inu anthu okhala m'dziko, chiwonongeko chanu chafika. Nthaŵi yafika, tsiku lili pafupi, tsiku lachisokonezo, osati lachimwemwe, ku mapiri.

8Posachedwapa ndidzakukwiyirani, ndipo ukali wanga udzathera pa inu. Ndidzagamula mlandu wanu potsata makhalidwe anu, ndipo ndidzakulangani chifukwa cha zonyansa zanu zochuluka.

9Sindidzakumverani chifundo kapena kukulekani ai. Ndidzakulangani potsata makhalidwe anu ndiponso chifukwa cha zonyansa zimene mumachita. Pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, amene ndakulangani.”

10“Onanitu tsiku latsoka! Onanitu chikubwera! Chilango chanu chafika. Kunyada kwanu kwakakata, kudzitama kwanu kwaonekera poyera.

11Ndeu zasanduka chilango cha kuipa kwao. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene adzatsale. Zinthu zao zidzatha, chuma chao chidzathanso, ndipo ulemerero wao womwe udzatha.”

12“Nthaŵi yafika, tsiku layandikira. Wogula asakondwe, ndipo wogulitsa asamve chisoni, pakuti ukali wanga waŵagwera onse chimodzimodzi.

13Wogulitsa sadzazipezanso pa moyo wake wonse zimene adagulitsa kwa wina, pakuti chilango chidzagwera onsewo, sichingasinthike. Chifukwa cha machimo ake, palibe aliyense amene adzapulumutsa moyo wake.

14Lipenga lalira, ndipo onse akonzeka. Koma palibe ndi mmodzi yemwe amene akupita ku nkhondo, pakuti mkwiyo wanga wagwera onse pamodzi.

Mulungu adzalanga Aisraele chifukwa cha machimo ao

15“M'miseu akumenyana, m'nyumba muli mliri ndi njala. Anthu okhala ku midzi adzafa ndi nkhondo. Okhala m'mizinda adzafa ndi mliri ndi njala.

16Ngati otsala adzapulumukepo, azikakhala ku mapiri, nkumalira ngati nkhunda. Aliyense azidzabuula chifukwa cha tchimo lake.

17Manja onse adzalefuka, maondo adzangoti zii, kulobodoka ngati madzi.

18Adzavala ziguduli, ndipo adzagwidwa ndi mantha. Adzakhala ndi nkhope zamanyazi, kumutu adzameta mpala.

19Adzataya siliva wao m'miseu, ndipo golide wao adzamuwona ngati wonyansa. Siliva wao ndi golide wao sadzatha kuŵapulumutsa pa tsiku limene Chauta adzaonetse ukali wake. Chuma chaochi sichingaŵathandize kuthetsa njala, kapena kukhala okhuta, pakuti ndicho chidaŵagwetsa m'machimo.”

20“Kale ankanyada chifukwa cha zodzikongoletsera zao zamakaka. Koma ankazigwiritsa ntchito popanga mafano onyansa. Nchifukwa chake zodzikongoletsera zaozo ndidzazisandutsa zoŵanyansa.

21Ndidzazipereka kwa anthu akudza kuti azifunkhe. Anthu oipa kwambiri a pa dziko lapansi adzazilanda ndi kuziipitsa.

22Ine ndidzaŵalekerera anthuwo, kuti adzaipitse malo anga okondedwa. Adzaloŵamo ngati mbala nkuipitsamo.

23“Konzani maunyolo, popeza kuti anthu opha anzao achuluka m'dziko, mzinda wadzaza ndi ndeu.

24Ndidzatuma mitundu ya anthu yoipa kwambiri kuti ilande nyumba zao. Amphamvu pakati panu kunyada kwao kudzaŵathera, pamene ndidzalole mitundu yachilendoyo kuti iwononge malo amene amapembedzerapo.

25Pamene nkhaŵa idzaŵafikira, adzafunafuna mtendere, koma osaupeza.

26Tsoka lidzatsatana ndi tsoka linzake, padzakhala mphekesera zosatha. Anthu adzafunafuna mneneri kuti aŵalosere zakutsogolo, adzasoŵa ansembe oŵaphunzitsa malamulo, ndipo akuluakulu sadzakhalanso ndi uphungu.

27Mfumu idzalira, akalonga ake adzachita mantha. Manja a anthu am'dzikomo adzauma ndi mantha. Ndidzaŵalanga moyenerera machimo ao, ndidzaŵaweruza monga momwe iwowo adaŵeruzira anzao. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”

EZEKIELE APITIRIZA KUWONA ZINTHU M'MASOMPHENYA(Ezek. 8.1—10.22)
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help