1 Eks. 13.17-22 Koma kuyera kwakukulu kudaŵalira oyera anu.
Aejipito adamvadi mau ao,
ngakhale sadaone nkhope zao,
ndipo adaŵatcha odala,
popeza kuti analibe kanthu koŵavuta.
2Ndiye popeza kuti ana anuwo
sadalipsire pa mavuto ao,
Aejipito ankaŵathokoza
naŵapempha kuti aŵakhululukire
zolakwa zao zija.
3Tsono pamalo pa mdima,
Inu mudapatsa ana anu mtambo wamoto,
kuti uŵatsogolere pa njira yosaidziŵa iwowo.
Unali ngati dzuŵa losaŵavuta
pa ulendo wao wotchuka uja.
4Adani ao adayeneradi kuŵachotsera kuŵala
ndi kuŵatsekera mu mdima,
chifukwa adaaponya ana anu m'ndende.
Ana anuwo ndiwo amene anali odzapereka
kuŵala kwamuyaya kwa malamulo anu
kwa anthu a dziko lapansi.
Ana oyamba a ku Ejipito afa onse5Iwo aja adafuna kupha ana a anthu anu oyera.
Koma mwana mmodzi uja ataikidwa
pa madzi a mtsinje nkupulumuka,
Inu mudaŵalanga anthuwo
pakupha ana ao ambirimbiri.
Ndipo mudaŵamiza onse pamodzi
m'mafunde aukali.
6Usiku umenewo makolo athu anali ataudziŵiratu,
kuti azilimba mtima ndi kukondwa
podziŵa kuti apherezera malumbiro
aja ankaŵakhulupiriraŵa.
7Choncho anthu anu
ankayembekeza chipulumutso cha olungama
ndiponso chiwonongeko cha adani ao.
8Njira yomwe mudalangira adani athu,
idakhala njira yoti mutichitire ife zaulemu
potiitana kwa Inu.
9Adzukulu oyera mtima a olungama aja
ankapereka nsembe mobisala.
Ankavomerezana kuti adzasunga malamulo a Mulungu
ndi kugaŵana molingana zinthu zimodzimodzi,
kaya zikhale madalitso, kaya zoopsa.
Motero adaayambiziratu kuimba nyimbo zotamanda
za makolo ao.
10Koma nthaŵi yomweyo konsekonse kudamveka mfuu
wosokonezeka wa adani ao akulira ana ao.
11Kapolo ndi mbuye wake adalandira chilango chimodzi,
munthu wamba adavutika chimodzimodzi monga mfumu.
12Onsewo anali ndi maliro osaŵerengeka
a amene adafa imfa imodzimodzi.
Sipadatsale amoyo okwanira oti nkuika maliro onsewo,
chifukwa ana ao amene iwo ankanyadira kwambiri
adafa kamodzinkamodzi.
13Adakana kukhulupirira chilichonse
chifukwa cha masenga ao,
koma pamene adafa ana ao oyamba,
anthuwo adazindikira
kuti mtundu wa anthu anu
unalidi wa ana a Mulungu.
14Pamene zinthu zonse zinali chete,
ndipo usiku utafika pakati pake,
15mau anu amphamvu adalumpha
kuchokera kumwamba ku mpando wachifumu,
kudzagwa m'dziko lotembereredwa
ngati wankhondo wopanda chisoni.
16Wokhala ndi lupanga lakuthwa
la lamulo lanu losasinthika,
adaima ndi kudzaza dziko ndi imfa,
mapazi ake ataponda pansi,
mutu wake utakhudza ku thambo.
17Pompo maloto oopsa adaŵachititsa mantha,
zinthu zozilota ndi zoziwona m'masomphenya zidaŵaopsa.
18Atagwa pansi, wina uku, wina uku,
nkukhala ngati akufa,
aliyense adaulula zifukwa zake zimene ankafera.
19Maloto aja amene adaŵavuta
anali ataŵadziŵitsiratu zimenezo,
kuwopa kuti angafe osazindikira chifukwa chake
cha mazunzo ao.
Pemphero la Aroni lipulumutsa Aisraele ku imfa20 Num. 16.41-50 Ngakhalenso anthu olungama omwe, imfayo idaŵakhudza,
ndipo m'chipululu muja mliri udagwetsa ambiri.
Koma mkwiyo wanu sudakhalitse nthaŵi yaitali.
21Munthu wina wosapalamula adafulumira
kuŵatchinjiriza,
ndipo atatenga zida za utumiki wake,
adapemphera ndi kufukiza lubani wopepesera machimo.
Motero adaletsa ukali wanu, nathetsa mliri uja,
kuwonetsa kuti analidi mtumiki wanu.
22Adaletsa ukali wanuwo,
osati chifukwa cha nyonga za thupi,
kapena chifukwa cha mphamvu za zida,
koma adafeŵetsa mtima wa wolangayo ndi mau ake,
pomukumbutsa malumbiro ake
ndiponso zimene adaapangana ndi makolo athu.
23Akufa aja atagwa ndi kuunjikika pa mulu umodzi,
iye adanenera anthu naletsa ukali wanu,
ndipo adautsekera njira kuti amoyo usaŵagwere.
24Pamkanjo pake panali chithunzi
cha dziko lonse lapansi,
maina olemekezeka a makolo athu anali olembedwa
pa mizere inai ya miyala ya mtengo wapatali.
Tsono ulemerero wanu unkaoneka
pa chisoti cha pamutu pake.
25Poona zimenezo, woononga uja adaima,
ankachita nazo mantha,
chifukwa kunkakwanira kuwonetsa
chitsanzo cha ukali wanu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.