1Tsono mneneri wa Mulungu adachokera ku Yuda napita ku Betele monga momwe Chauta adaamlamulira. Nthaŵi imeneyo nkuti Yerobowamu ataimirira pambali pa guwa akufukiza lubani.
22Maf. 23.15, 16 Ndipo mneneriyo adatemberera guwalo potsata mau a Chauta nati, “Guwa iwe, guwa iwe, imva mau a Chauta, akunena kuti, ‘Mwana wamwamuna adzabadwa pa banja la Davide, dzina lake Yosiya. Pa iwe iyeyo adzaperekapo ngati nsembe ansembe otumikira ku malo achipembedzo amene amafukiza lubani pa iwe, ndipo pa iwe adzatenthapo mafupa a anthu.’ ”
3Tsono mneneri uja adapereka chizindikiro pa tsiku lomwelo nati, “Chizindikiro chimene Chauta wanena ndi ichi, ‘Guwali lidzang'ambika ndipo phulusa limene lili pamenepo lidzamwazika.’ ”
4Mfumu Yerobowamu atamva zimene ankanena mneneri wa Mulungu zija za guwa la ku Betele, adatambalitsa dzanja lake ali kuguwako nati, “Mgwireni.” Pomwepo dzanja lake lomwe adaatambalitsira mneneri wa Mulungu lija lidauma kuti gwa, ndipo sadathenso kulibweza.
5Nthaŵi yomweyo guwa lija nalonso lidang'ambika, ndipo phulusa lapaguwapo lidamwazika potsata chizindikiro chimene adaapereka mneneri wa Mulunguyo, malinga ndi m'mene adaanenera Chauta.
6Apo mfumu idauza mneneri wa Mulungu uja kuti, “Mupemphere kwa Chauta Mulungu wanu kuti andikomere mtima, dzanja langali lichire.” Mneneri wa Mulungu adapemphera kwa Chauta, ndipo dzanja la mfumu lidachiradi.
7Tsono mfumuyo idauza mneneri wa Mulungu uja kuti, “Tiyeni kunyumba mukadye chakudya, ndipo ndikakupatsani mphotho.”
8Koma mneneri wa Mulungu uja adauza mfumu kuti, “Ngakhale mundipatse theka la chuma chanu, sindikadya chakudya chilichonse kapena kumwa madzi kuno.
9Pakuti Chauta adandilamula kuti, ‘Usakadye chakudya chilichonse, kapena kumwa madzi, kapenanso kudzera njira yomwe udaadzera kale pobwera.’ ”
10Motero mneneriyo adadzera njira ina, osatsata njira imene adaadzera popita ku Betele.
11Tsono ku Betele kunkakhala mneneri wina wokalamba. Ana ake adadza kudzamuuza zonse zimene mneneri wa Mulungu adaachita ku Betele tsiku lija. Adauzanso atate ao mau onse amene mneneri wa Mulungu uja adaauza mfumu.
12Ndipo bambo wao uja adaŵafunsa kuti, “Kodi adadzera njira iti?” Ana akewo adamlangiza njira imene adadzera mneneri wa Mulungu wochokera ku Yuda uja.
13Bambo uja adauza ana akewo kuti, “Mangireni chishalo pa bulu.” Anawo adamanga chishalocho pa bulu, ndipo nkhalamba ija idakwerapo.
14Idalondola mneneri wa Mulungu uja, nikampeza atakhala pansi patsinde pa mtengo wa thundu. Tsono idamufunsa kuti, “Kodi inu ndiye mneneri wa Mulungu amene mudachoka ku Yuda?” Munthu uja adayankha kuti, “Ndine amene.”
15Nkhalambayo idati, “Tiyeni kwathu tikadye.”
16Koma mneneriyo adati, “Ine sindingabwerere nanu kapena kukaloŵa m'nyumba mwanu. Sindikadya chakudya kapena kumwa nanu madzi kuno.
17Pakuti Chauta adandiwuza kuti, ‘Usakadye chakudya kapena kumwa madzi kumeneko, kapenanso kubwerera podzera njira imene udaadzera popita.’ ”
18Nkhalambayo idamuuza kuti, “Inenso ndine mneneri monga inu nomwe, ndipo mngelo adalankhula nane nandiwuza kuti, ‘Ubwerere naye limodzi kunyumba kwako, kuti akadye chakudya ndiponso akamweko madzi.’ ” Nkhalambayo inkamuuza zabodza.
19Motero idabwerera naye limodzi kunyumba kwake, ndipo adakadya namwa madzi.
20Nthaŵi imene analikudya, Chauta adalankhula ndi mneneri wokalamba uja amene adaabweza mnzakeyo,
21ndipo iyeyo adafuulira mneneri wa Mulungu, wochokera ku Yuda uja kuti, “Imvani mau a Chauta, akuti chifukwa choti simudamvere mau a Chauta, ndipo simudatsate lamulo lake limene adakulamulani,
22koma mwabwerera, ndipo mwadya ndi kumwa madzi pa malo amene Chauta adakuuzani kuti musakadye chakudya kapena kumwako madzi, mtembo wanu sadzauika m'manda a makolo anu.”
23Choncho atatha kudya ndi kumwa, adamangirira chishalo pa bulu wa mneneri wa ku Yuda uja.
24Iyeyo popita, adakumana ndi mkango pa mseu, ndipo udamupha. Tsono mtembo udagwera mu mseu, ndipo bulu uja adaima pambali pa mtembowo. Mkango uja nawonso udaima pambali pa mtembowo.
25Anthu ena amene ankapita mumseumo, adaona mtembo uli gone, mkango utaima pambali pake. Ndipo adapita namakasimbira anzao mu mzinda za zimene adaaona pamseu paja.
26Mneneri amene adaabweza mnzake kunjira uja, atamva zimenezo, adati, “Ameneyo ndi mneneri wa Mulungu uja amene sadamvere mau a Chauta. Nchifukwa chake Chauta wampereka kwa mkango, umene wamkadzula ndi kumupha, monga momwe Chauta adaanenera.”
27Pompo mneneri wokalamba uja adauza ana ake kuti, “Mundimangire chishalo pa bulu.” Anawo adamangirira chishalocho.
28Tsono adapita, nakapeza mtembo wa munthu uja uli gone pa mseu, bulu ataima pambali pake pamodzi ndi mkango womwe. Mkangowo sudadye mtembowo kapena kukadzula bulu uja ai.
29Mneneri wokalambayo adatenga mtembo wa mneneri wa Mulungu uja, nauika pa buluyo, ndipo adabwera nawo ku mzinda kuti alire maliro ndi kuika mtembowo m'manda.
30Tsono adaika mtembowo m'manda ake. Pomulira ankati, “Mbale wanga ine! Mbale wanga ine!”
31Ndipo atamuika m'manda adauza ana ake kuti, “Ine ndikafa mudzandiike m'manda m'mene mneneri wa Mulunguyu waikidwa. Mudzaike mtembo wanga pambali pa mtembo wake.
32Zoonadi, zimene Chauta adalankhulitsa mneneriyo zotemberera guwa la ku Betele ndi nyumba za pa malo achipembedzo zimene zili m'mizinda ya ku Samariya, zidzachitikadi.”
Tchimo la Yerobowamu33Ngakhale zidaatero, Yerobowamu sadasiye njira zake zoipa, koma adaikanso anthu wamba kukhala ansembe pa malo akeake achipembedzo. Aliyense amene ankafuna, adampatula kuti akhale wansembe wa pa malowo.
34Limeneli linali tchimo lalikulu pa banja la Yerobowamu. Nchifukwa chake banjalo lidaonongeka ndi kufafanizika pa dziko lapansi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.