1Imvani mau anga, Inu Chauta,
mverani kusisima kwanga.
2Imvani kulira kwanga,
Inu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga,
pakuti ndikupempha chithandizo kwa Inu.
3M'maŵa, Inu Chauta, mumamva mau anga.
M'maŵa ndimapemphera kwa Inu,
ndi kudikira kuti mundiyankhe.
4Inu sindinu Mulungu wokondwerera machimo.
Simufuna zoipa pamaso panu.
5Anthu onyada sangathe kuwonekera pamaso panu.
Inu mumadana ndi anthu onse ochita zoipa.
6Inu mumaŵaononga anthu olankhula zonama.
Inu Chauta mumanyansidwa nawo
anthu onyenga ndi opha anzao.
7Koma ine ndidzatha kuloŵa m'Nyumba mwanu
chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu.
Ndidzaŵeramitsa mutu pansi,
kupembedza Inu m'Nyumba yanu yoyera.
8Inu Chauta, ndinu olungama,
munditsogolere pakati pa adani ondizonda.
Mundikonzere njira yoongoka kuti ndidzeremo.
9 Aro. 3.13 Adani anga amalankhula mabodza okhaokha.
Mtima wao umangofuna kuwononga.
Mummero mwao muli ngati manda apululu,
ndipo lilime lao limalankhula zonyenga.
10Asenzetseni tchimo lao, Inu Mulungu.
Upo wao woipa uŵagwetse iwo omwe,
muŵachotse pamaso panu
chifukwa cha zochimwa zao zambirimbiri,
chifukwa akuukirani Inu.
11Koma onse othaŵira kwa Inu akondwere,
aziimba ndi chimwemwe nthaŵi zonse.
Inu muŵatchinjirize,
kuti okukondani akondwere
chifukwa cha chitetezo chanu.
12Inu Chauta, mumadalitsa munthu wochita chilungamo.
Kukoma mtima kwanu kuli ngati chishango chomuteteza.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.