1Abale, ndinu oyera ake a Mulungu, inuyo adakuitanani kuti nanunso mukhale ndi moyo wakumwamba. Nchifukwa chake muzisinkhasinkha za Yesu, mtumwi wa Mulungu, ndiponso Mkulu wa ansembe onse wa chikhulupiriro chimene timavomereza.
2Num. 12.7 Paja Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu amene adampatsa udindowo, monga momwe Mosenso anali wokhulupirika m'nyumba yonse ya Mulungu.
3Munthu womanga nyumba amalandira ulemu woposa ulemerero wa nyumbayo. Momwemonso Yesu ngwoyenera kulandira ulemerero woposa ulemerero wa Mose.
4Nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu wakutiwakuti, koma amene adapanga zonse, ndi Mulungu.
5Mose anali wokhulupirika m'nyumba yonse ya Mulungu ngati wantchito chabe, kuti achitire umboni zimene Mulungu analikudzanena m'tsogolo mwake.
6Koma Khristu anali wokhulupirika m'nyumba ya Mulungu ngati mwana wolamulira pa zonse za m'nyumba mwakemo. Ndipo nyumba yakeyo ndife, ngati tiika mphamvu pa kulimba mtima ndi kunyadira zimene tikuziyembekeza.
Za mpumulo wa anthu a Mulungu7 Mas. 95.7-11 Nchifukwa chake tsono,
monga Mzimu Woyera akunenera,
“Lero lino mukamva mau a Mulungu,
8musaumitse mitima yanu
monga muja zidaachitikira pomuukira Mulungu,
tsiku la kumuyesa m'chipululu muja.
9Mulungu akuti,
Pamene paja, makolo anu adaandiputa pakundiyesa,
ndipo adaona zimene ndidaŵachita pa zaka makumi anai.
10Tsono ndidaukwiyira mbadwowo,
ndipo ndidati,
‘Nthaŵi zonse amasokera mumtima mwao,
sanaphunzirebe njira zanga.’
11Motero ndili wokwiya ndidalumbira kuti,
‘Sadzaloŵa konse mu mpumulo
umene ndidaŵakonzera.’ ”
12Abale, mchenjere, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woipa ndi wosakhulupirira, womlekanitsa ndi Mulungu wamoyo.
13Kwenikweni muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku ikadalipo nthaŵi, imene m'mau a Mulungu imatchedwa kuti, “Lero”. Muzichita zimenezi, kuwopa kuti wina aliyense mwa inu angaumitsidwe mtima ndi chinyengo cha uchimo.
14Paja timasanduka anzake a Khristu, malinga tikasunga kwenikweni mpaka potsiriza kulimba mtima kumene tinali nako poyamba.
15Mas. 95.7, 8 Paja Malembo akuti,
“Lero lino mukamva mau a Mulungu,
musaumitse mitima yanu
monga muja zidaachitikira poukira Mulungu.”
16 Num. 14.1-35 Nanga amene adaamva mau ake a Mulungu namuukira, ndani? Ndi onse aja amene Mose adaaŵatsogolera nkuŵatulutsa m'dziko la Ejipito.
17Nanga amene Mulungu adaaŵakwiyira zaka makumi anai, ndani? Ndi anthu amene adaachimwa aja, mitembo yao nkutsalira m'chipululu.
18Nanga Mulungu ankanena za yani pamene adaati, “Ndikulumbira kuti ameneŵa sadzaloŵa konse mu mpumulo umene ndidaŵakonzera?” Pajatu ankanena za anthu amene adaamuukira.
19Motero tikuwona kuti anthuwo sadathe kuloŵa, chifukwa cha kusakhulupirira.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.