Mas. 135 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nyimbo yotamandaSalmo la Davide.

1Tamandani Chauta.

Tamandani dzina la Chauta,

Perekani matamando, inu atumiki a Chauta,

2inu amene mumatumikira m'Nyumba ya Chauta,

m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu!

3Tamandani Chauta, pakuti ngwabwino.

Muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake,

pakuti nlokoma kwambiri.

4Wadzisankhulira Yakobe kuti akhale wake,

Israele kuti akhale chuma chake.

5Pakuti ndimadziŵa kuti Chauta ndi wamkulu,

kuti Chauta, Mulungu wathu, ndi wamphamvu

kupambana milungu yonse.

6Chilichonse chimene Chauta amafuna kuchita

amachitadi kumwamba ndi pa dziko lapansi,

m'nyanja ndi monse mozama.

7Ndiye amene amatulutsa mitambo

ku mathero a dziko lapansi,

amene amachititsa zing'aning'ani za mvula,

amene amaombetsa mphepo kuchokera m'nkhokwe zake.

8Ndiye amene adapha ana achisamba a ku Ejipito,

ana a anthu ndi a nyama omwe,

9amene adaonetsa Farao ndi atumiki ake onse

zizindikiro zamphamvu ndi zodabwitsa m'dziko la Ejipito.

10Ndiye amene adaononga mitundu yambiri ya anthu,

ndi kupha mafumu amphamvu aja,

11Sihoni, mfumu ya Aamori, ndi Ogi, mfumu ya ku Basani,

pamodzi ndi maufumu onse a ku Kanani.

12Adapereka dziko lao kuti likhale choloŵa,

choloŵa cha Aisraele, anthu ake.

13Dzina lanu, Inu Chauta, nlamuyaya,

kutchuka kwanu ndi kwa pa mibadwo yonse.

14Pakuti Chauta adzaweruza anthu ake kuti alibe mlandu,

adzachitira chifundo atumiki ake.

15 Mas. 115.4-8; Chiv. 9.20 Mafano a mitundu ina ya anthu

ndi asiliva ndi agolide chabe,

ndi opangidwa ndi manja a anthu.

16Pakamwa ali napo, koma salankhula,

maso ali nawo, koma sapenya.

17Makutu ali nawo, koma saamva,

ndipo alibe mpweya m'kamwa mwao.

18Anthu amene amapanga mafanowo afanefane nawo,

chimodzimodzi onse amene amaŵakhulupirira.

19Inu a m'banja la Israele, tamandani Chauta!

Inu a m'banja la Aroni, tamandani Chauta!

20Inu a banja la Levi, tamandani Chauta!

Inu amene mumaopa Chauta, tamandani Chauta!

21Atamandike ku Ziyoni Chauta,

amene amakhala ku Yerusalemu!

Tamandani Chauta!

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help