1“Za Ufumu wakumwamba tingazifanizire motere: Munthu wina adaalaŵirira m'mamaŵa kukalemba anthu okagwira ntchito m'munda wake wamphesa.
2Adaapangana nawo kuti adzaŵalipira ndalama imodzi yasiliva pa tsiku, naŵatuma kumunda kwake.
3Pa nthaŵi ya 9 koloko adapitanso, nakapeza ena atangokhala khale pa msika, osagwira ntchito.
4Adaŵauza kuti, ‘Inunso pitani ku munda wanga wamphesa, ndidzakulipirani moyenerera.’
5Iwowo adapitadi. Munthu uja adapitanso pa 12 koloko masana ndi pa 3 koloko, nakachita chimodzimodzi.
6Pafupi 5 koloko madzulo adapitanso nakapeza enanso akungokhala. Adaŵafunsa kuti, ‘Bwanji mwangokhala khale pano tsiku lonse osagwira ntchito?’
7Iwowo adayankha kuti, ‘Chifukwa palibe amene watilemba.’ Iye uja adaŵauza kuti, ‘Inunso pitani ku munda wanga wamphesa.’
8 kwa Yesu, namgwadira kuti ampemphe kanthu.
21Yesu adamufunsa kuti, “Amai, kodi muli ndi mau?” Iye adayankha kuti, “Ndimati mulonjeze kuti mu Ufumu wanu ana anga aŵiriŵa adzakhale wina ku dzanja lanu lamanja, wina ku dzanja lanu lamanzere.”
22Koma Yesu adayankha kuti, “Simukudziŵa zimene mukupempha. Kodi inu mungathe kumwa nao chikho chamasautso chimene ndikudzamwera Ine?” Iwo aja adayankha kuti, “Inde, tingathe.”
23Apo Yesu adati, “Chabwino, mudzamwa nao chikho changacho. Koma Ineyo si udindo wanga kusankha munthu kuti akhale ku dzanja langa lamanja, kapena ku dzanja langa lamanzere. Atate ndiwo adzapereke malo ameneŵa kwa amene Atatewo adaŵakonzera.”
24Pamene khumi ena aja adamva zimenezi, adapsera mtima abale aŵiri aja.
25Lk. 22.25, 26Koma Yesu adaŵaitana ophunzira akewo naŵauza kuti, “Mukudziŵa kuti olamulira amadyera anthu ao masuku pa mutu. Akuluakulu aonso amaonetsadi mphamvu zao pa anthu ao.
26Mt. 23.11; Mk. 9.35; Lk. 22.26Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, akhale mtumiki wanu.
27Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, akhale kapolo wanu.
28Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”
Yesu achiritsa anthu aŵiri akhungu(Mk. 10.46-52; Lk. 18.35-43)29Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankatuluka mu mzinda wa Yeriko, anthu ambirimbiri ankamutsatira.
30Panali anthu aŵiri akhungu amene adaakhala pansi pamphepete pa mseu. Iwo aja atamva kuti Yesu akupita mumseumo, adayamba kufuula kuti, “Inu Ambuye, Mwana wa Davide, mutichitire chifundo.”
31Anthu aja adaŵazazira akhunguwo kuti akhale chete. Koma iwo nkumafuulirafuulira kuti, “Inu Ambuye, Mwana wa Davide, mutichitire chifundo.”
32Yesu adaima, naŵaitana, nkuŵafunsa kuti, “Kodi mukufuna kuti ndikuchitireni chiyani?”
33Iwo aja adati, “Ambuye, tikufuna kuti tizipenya.”
34Yesu adaŵamvera chifundo nakhudza maso ao. Pompo iwo adayamba kupenya, kenaka nkumamutsata.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.