Yob. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Tsiku lina pamene angelo a Mulungu ankabwera kudzadziwonetsa pamaso pa Chauta, nayenso Satana adafika nawo limodzi.

2Pamenepo Chauta adafunsa Satanayo kuti, “Nanganso iwe Satana, kutereku ukuchokera kuti?” Iye adayankha kuti, “Ndakhala ndikuyendayenda ndi kumangozungulira dzikoli.”

3Chauta adamufunsanso kuti, “Kodi wazindikirapo mtumiki wanga Yobe, kuti safanafana ndi wina aliyense pa dziko lapansi? Iye uja ndi munthu wosalakwa ndi wolungama. Amandimvera Ine Mulungu, ndipo amapewa zoipa. Iyeyo akali ndithu wokhulupirikabe kwambiri, ngakhale kuti iwe paja udaandiwumiriza kuti ndikulole kuti umuvutitse popanda chifukwa.”

4Apo Satana adayankha kuti, “Koma ayesedwe m'thupi mwake. Zinthu zonse zimene munthu ali nazo angathe kuzipereka, chikulu iyeyo ali moyo.

5Koma tsopano taonongani thupi lake, muwona, adzakutukwanirani pamaso.”

6Chauta adauza Satana uja kuti, “Chabwino, iyeyo uchite naye zonse zimene ukufuna, koma moyo wake wokha usauchotse.”

7Choncho Satana adachoka kumsiya Chauta napita kukazunza Yobe ndi zilonda zoopsa pa thupi lonse.

8Pamenepo Yobe adatenga phale kuti azidzikandira, nakakhala pa dzala.

9Tsono mkazi wake adamuuza kuti, “Ha! Mukukhalabe okhulupirika motere! Ingomtukwanani Mulunguyo, mufe basi!”

10Koma Yobe adauza mkazi wakeyo kuti, “Ukulankhula ngati mkazi wopusa. Ngati tilandira zokondweretsa kwa Mulungu, tilekerenji kulandiranso zoŵaŵa?” Motero pa zonsezi Yobe sadachimwe polankhula pake.

Abwenzi a Yobe abwera kudzacheza naye

11Tsono abwenzi ake a Yobe, Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Suki, ndi Zofari wa ku Naama, adazimva za masoka onseŵa amene adamgwera. Ndiye tsiku lina anthu atatuwo adabwera, aliyense kuchokera kwao. Onsewo anali atapangana za nthaŵi yoti adzampepese ndi kudzamsangulutsa.

12Ataona Yobeyo chakutali, sadamzindikire, ndipo adayamba kulira mofuula. Adang'amba zovala zao, nadzithira fumbi kumutu.

13Adakhala ndi Yobeyo masiku asanu ndi aŵiri, usana ndi usiku womwe. Koma panalibe ndi mmodzi yemwe amene ankalankhula naye, chifukwa chozindikira kuti Yobeyo akuvutika kwambiri.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help