1 Mbi. 26 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Alonda a ku Nyumba ya Chauta

1Magulu a alonda odikira pa khomo naŵa: m'gulu la Akora munali Meselemiya, mwana wa Kore, mmodzi mwa ana a Asafu.

2Meselemiya anali ndi ana aŵa: wachisamba anali Zekariya, wachiŵiri Yediyale, wachitatu Zebadiya, wachinai Yatiniele,

3wachisanu Elamu, wachisanu ndi chimodzi Yehohanani ndipo wachisanu ndi chiŵiri Elihunai.

42Sam. 6.11; 1Mbi. 13.14 Obededomu Mulungu anali ndi ana aŵa: wachisamba anali Semaya, wachiŵiri Yehozabadi, wachitatu Yowa, wachinai Sakara, wachisanu Netanele,

5wachisanu ndi chimodzi Amiyele, wachisanu ndi chiŵiri Isakara ndipo wachisanu ndi chitatu Peuletai, (pakuti paja Mulungu adaamdalitsa Obededomuyo.)

6Semaya mwana wake nayenso anali ndi ana amene anali otchuka m'mabanja a makolo ao, makamaka aŵiri omariza.

7Ana a Semaya naŵa: Otini, Refaele, Obede ndi Elizabadi amene anali ndi abale ao amphamvu, Elihu ndi Semakiya.

8Kuchokera ku banja la Obededomu kudasankhidwa anthu 62, onsewo okhoza ntchito.

9Kuchokera ku banja la Meselemiya kudasankhidwa anthu aluso 18.

10Kuchokera ku banja la Merari kudasankhidwa Hosa amene anali ndi ana aŵa: Simiri mtsogoleri (iyeyu ngakhale sanali mwana wachisamba, atate ake adaamsankhula kuti akhale mtsogoleri.)

11Wachiŵiri Hilikiya, wachitatu Tebaliya, wachinai anali Zekariya. Onse a m'banja la Hosa amene anali alonda analipo 13.

12Alonda a pa khomo la Nyumba ya Chauta adaŵaika m'magulu, potsata mabanja ao, ndipo adaŵapatsa ntchito zao zotumikira, monga momwe adachitira Alevi anzao.

13Iwonso adachita maere pa mabanja onse ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe, kuti apeze okalonda pa makomo.

14Selemiya adamsankha kuti azilonda pa khomo lakuvuma. Mwana wake Zekariya, phungu wanzeru, adamsankha kuti azilonda khomo lakumpoto.

15Obededomu adamsankha kuti azilonda khomo lakumwera, ndipo ana ake adaŵaika kuti azilonda nyumba ya katundu.

16Supimu ndi Hosa adaŵasankha kuti azilonda kuzambwe ku khomo la Saleketi, pa mseu wokwera. Maulonda ankakhala otsatanatsatana.

17Kuvuma kunkakhala alonda asanu ndi mmodzi tsiku lililonse. Kumpoto kunkakhala alonda anai tsiku lililonse, kumwera alonda anai tsiku lililonse, ndiponso alonda aŵiriaŵiri ku nyumba ya katundu.

18Ku bwalo lakuzambwe kunali alonda anai ku mseu ndiponso alonda aŵiri ku bwalo lenilenilo.

19Ameneŵa ndiwo amene anali magulu a alonda apamakomo, ochokera ku mabanja a Akora ndi a Merari.

Ntchito zina za ku Nyumba ya Chauta

20Mwa Alevi, Ahiya ankayang'anira chuma cha ku Nyumba ya Chauta ndiponso zipinda zosungiramo zinthu zopatsidwa kwa Mulungu.

21Ladani, mmodzi mwa ana a Geresoni, adabereka ana ake amene ankakhala atsogoleri a mabanja, makamaka Ayehiyeli.

22Ana ena a Ladani, Zetamu ndi Yowele mbale wake, nawonso ankayang'anira chuma cha ku Nyumba ya Chauta.

23Ena mwa Aamuramu, Aizari, Ahebroni ndi Auziyele adalandira maudindo osiyanasiyana:

24Sebuele mwana wa Geresomo, mwana wa Mose anali mkulu woyang'anira chuma.

25Abale ake obadwa mwa Eliyezere anali Rehabiya mwana wake, Yesaiya, Yoramu, Zakiri ndiponso Selomoti.

26Selomotiyu pamodzi ndi abale ake, ankasunga chuma cha mphatso zopatulika zimene mfumu Davide adazipereka, pamodzi ndi atsogoleri a mabanja, atsogoleri a anthu zikwi, atsogoleri a anthu mazana, ndiponso atsogoleri a magulu a ankhondo.

27Pa zofunkha zotenga ku nkhondo, adapatulapo mphatso zina kuti zikhale zothandiza kusunga Nyumba ya Chauta.

28Selomoti pamodzi ndi abale ake, ndiwo amene ankasamalira mphatso zonse zopatulika zoperekedwa ndi mneneri Samuele, ndi Saulo mwana wa Kisi, ndi Abinere mwana wa Nere, ndiponso ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndipo zinthu zina zonse zoperekedwa ndi munthu wina aliyense zinali m'manja mwa Selemoti ndi abale ake.

Ntchito za Alevi ena

29Mwa zidzukulu za Izara, Kenaniya ndi ana ake ndiwo adaŵaika kuti azigwirira Aisraele ntchito zoyang'anira zinthu, monga zolembalemba ndiponso kuweruza milandu.

30Mwa Ahebroni, Hasabiya pamodzi ndi abale ake 1,700, anthu anzeru, ankayang'anira Aisraele chakuzambwe kwa Yordani, pa ntchito zonse za chipembedzo ndiponso za boma.

31Yeriya ndiye anali mtsogoleri wa Ahebroni potsata mndandanda wa mabanja a makolo. Pa chaka cha 40 cha ufumu wa Davide padachitika kafukufuku ndipo padapezeka kuti ena otchuka a m'banja la Yeriya ankakhala ku Yazere ku Giliyadi.

32Mfumu Davide adasankha atsogoleri okwanira 2,700 a m'banja la Yeriyayo kuti aziyang'anira Arubeni, Agadi ndiponso fuko lahafu la Amanase pa zonse zokhudza chipembedzo ndiponso za boma.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help