Mas. 90 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za Mulungu ndi munthuPemphero la Mose, munthu wa Mulungu.

1Inu Ambuye, ndinu kothaŵira kwathu

pa mibadwo yonse.

2Mapiri asanabadwe,

ndipo musanalenge dziko lapansi ndi pokhala anthu,

ndinu Mulungu kuyambira muyaya mpaka muyaya.

3Inu mumabwezera anthu ku fumbi,

ndipo mumati,

“Bwererani inu ana a anthu.”

4 2Pet. 3.8 Pakuti zaka chikwi chimodzi pamaso panu

zili ngati dzulo chabe,

kapena ngati kamphindi chabe kausiku.

5Inu mumachotsa moyo wa anthu mwadzidzidzi.

Ali ngati maloto,

ali ngati udzu wongotsitsimuka m'maŵa.

6M'mamaŵamo umatsitsimuka ndipo umakondwa.

Madzulo umafota ndi kuuma.

7Ife tapseratu ndi mkwiyo wanu woyaka,

tikufa ndi mantha chifukwa cha ukali wanu.

8Inu mwaika machimo athu pamaso panu,

ngakhale machimo obisika mwaŵaonetsa poyera.

9Pajatu masiku athu amachepa chifukwa cha mkwiyo wanu,

zaka zathu zimatha ngati kuusa moyo chabe.

10 Mphu. 18.8, 9 Zaka za moyo wathu nzokwanira makumi asanu ndi aŵiri,

tikakhala amphamvu, ndiye makumi asanu ndi atatu.

Koma zaka zonsezo ndi za nkhaŵa ndi mavuto.

Zakazo zimatha msanga, ife nkumapita.

11Kodi ndani amadziŵa kukula kwa mkwiyo wanu

ndi ukali wanu,

kupambana anthu okuwopani?

12Tsono tiphunzitseni kuŵerenga masiku athu,

kuti tikhale ndi mtima wanzeru.

13Lezani mtima, Inu Chauta.

Nanga mudzatikwiyira mpaka liti?

Achitireni chifundo atumiki anu.

14Tidzazeni m'maŵa mulimonse

ndi chikondi chanu chosasinthika,

kuti tizikondwa ndi kusangalala masiku athu onse.

15Tisangalatseni masiku ambiri

monga masiku amene mudatisautsira,

zaka zambiri monga zaka zimene tidaona mavuto.

16Mulole kuti ntchito zanu ziwoneke kwa atumiki anu,

mphamvu zanu zaulemerero ziwoneke kwa ana ao.

17Inu Ambuye, Mulungu wathu, mutikomere mtima,

ndi kudalitsa zonse zimene timachita,

ndithu mudalitse ntchito zonse za manja athu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help