1Pa nthaŵi imeneyo Herode, mfumu ya ku Galileya, adaamva zimene anthu ankanena za Yesu.
2Tsono adauza nduna zake kuti, “Ameneyu ndi Yohane Mbatizi uja, adauka kwa akufa, nkuwona akuchita zamphamvu zonsezi.”
3Lk. 3.19, 20Pajatu Herode kale adaatuma asilikali ake kuti akagwire Yohane, akammange ndi kumponya m'ndende. Adaachita zimenezi chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo, mbale wake.
4Lev. 18.16; 20.21Pakuti Yohane adaauza Herode kuti, “Nkulakwira Malamulo kumukwatira mkaziyo.”
5Kwenikweni Herode ankafuna kupha Yohane, koma ankaopa anthu, chifukwa iwo ankati ndi mneneri.
6Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiasi adaavina pamaso pa anthu oitanidwa ku phwando, mwakuti adaakondwetsa Herode kwambiri.
7Motero Herode adaalonjeza molumbira kuti, “Ndithudi, ndidzakupatsa chilichonse chimene ungapemphe.”
8Tsono mai wake atamuuza choti apemphe, mwana wamkazi uja adati, “Mundipatse pompano mutu wa Yohane Mbatizi m'mbale.”
9Pamenepo mfumu Herode adamva chisoni. Koma chifukwa cha malumbiro ake ndiponso chifukwa cha anthu oitanidwa ku phwando aja, adalamula kuti ampatse mutu adaapemphawo.
10Tsono adatuma munthu kuti akamdule mutu Yohaneyo m'ndende.
11Mutuwo adautengera m'mbale nakaupereka kwa mtsikana uja, mtsikanayo nkukaupereka kwa mai wake.
12Pambuyo pake ophunzira a Yohane adabwera nadzatenga mtembo wake nkukauika m'manda. Kenaka adapita kukauza Yesu.
Yesu adyetsa anthu oposa zikwi zisanu(Mk. 6.30-44; Lk. 9.10-17; Yoh. 6.1-14)13Yesu atazimva zimenezi, adachokako kumeneko m'chombo, kuti apite kwayekha kwazii. Koma anthu atamva, adayenda pa mtunda namlondola kuchokera ku mizinda yao.
14Yesu adatuluka m'chombomo, ndipo pamene adaŵaona anthu ambirimbiriwo, adaŵamvera chifundo, nayamba kuchiritsa amene ankadwala.
15Nthaŵi yamadzulo ophunzira ake adadzamuuza kuti, “Kunotu nkuthengo, ndipo ano ndi madzulo. Auzeni anthuŵa azinyamuka, apite ku midzi kuti azikagula chakudya.”
16Koma Yesu adaŵauza kuti, “Palibe chifukwa choti achokere. Inuyo apatseni chakudya.”
17Iwo adati, “Pano tili ndi buledi msanu yekha ndi nsomba ziŵiri, basi.”
18Yesu adati, “Bwera nazoni kuno.”
19Atatero, adalamula kuti anthu aja akhale pansi pa udzu. Tsono adatenga buledi msanu uja ndi nsomba ziŵiri zija, nayang'ana kumwamba, nkuthokoza Mulungu. Kenaka atanyemanyema bulediyo, adazipereka kwa ophunzira ake, ophunzira aja nkukagaŵira anthuwo.
20Anthu onsewo adadya mpaka kukhuta. Pambuyo pake ophunzira aja adatola zotsala nkudzaza madengu khumi ndi aŵiri.
21Koma tsono anthu amene adaadyawo analipo ngati zikwi zisanu amuna okha, osaŵerenga akazi ndi ana.
Yesu ayenda pa madzi(Mk. 6.45-52; Yoh. 6.15-21)22Madzulo omwewo Yesu adalamula ophunzira ake kuti aloŵe m'chombo, atsogole kupita ku tsidya, pamene Iye akuuza anthu kuti azipita kwao.
23Tsono atatsazikana nawo anthu aja, Iye adakwera ku phiri yekha kukapemphera. M'mene kunkayamba kuda, nkuti ali komweko yekhayekha.
24Pamenepo nkuti chombo chija chili kutalitali ndi mtunda, chikuvutika ndi mafunde, chifukwa chinali chitayang'anana ndi mphepo.
25M'mamaŵa kukali mbuu, Yesu adadza kwa iwo Iye akuyenda pa madzi.
26Pamene ophunzira aja adamuwona akuyenda pa madzi, adaopsedwa nati, “Ndi mzukwa!” Ndipo adayamba kukuwa chifukwa cha mantha.
27Koma nthaŵi yomweyo Yesu adaŵauza kuti, “Khazikani mtima pansi, ndine; musaope.”
28Apo Petro adati, “Ambuye, ngati ndinudi, tandiwuzani kuti ndibwere kwa Inu pamadzipo.”
29Yesu adati, “Chabwino, bwera.” Tsono Petro adatuluka m'chombo nayamba kuyenda pa madzi kupita kwa Yesu.
30Koma ataona m'mene ikuwombera mphepo, adachita mantha, nkuyamba kumira. Tsono adafuula kuti, “Ambuye, pulumutseni!”
31Pompo Yesu adatambalitsa dzanja nkumugwira nati, “Iwe wa chikhulupiriro chochepawe, unakayikiranji?”
32Pambuyo pake aŵiriwo adaloŵa m'chombo muja, mphepo nkuleka.
33Apo amene anali m'chombo aja adamgwadira Yesu nati, “Ndithudi, ndinu Mwana wa Mulungu.”
Yesu achiritsa odwala ku Genesarete(Mk. 6.53-56)34Tsono onse adaoloka nyanja nakafika ku Genesarete.
35Anthu akumeneko adamzindikira Yesu, nakadziŵitsa anzao a ku dera lonse lozungulira pamenepo. Motero adadza kwa Yesu ndi anthu onse odwala.
36Adampempha kuti aŵalole odwalawo kungokhudza ngakhale mphonje ya chovala chake. Mwakuti onse amene ankaikhudza, ankachira.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.