1Afilisti adasonkhanitsa magulu ao ankhondo ku Soko, m'dziko la Yuda. Adamanga zithando zao pakati pa Soko ndi Azeka ku Efesi-Damimu.
2Saulo adasonkhanitsa Aisraele, namanga zithando zao zankhondo m'chigwa cha Ela, nandanditsa gulu lankhondo kuti amenyane ndi Afilistiwo.
3Afilisti ndi Aisraele adaika ankhondo ao moyang'anana, ena mbali ina paphiri, ena mbali ina paphirinso, pakatipa chigwa.
4Tsono ku zithando za Afilisti kudatuluka munthu wina wamphamvu wa ku Gati, dzina lake Goliyati. Msinkhu wake unali pafupi mamita atatu.
5Ankavala chisoti chamkuŵa ndi malaya achitsulo, amene kulemera kwake kunali ngati makilogramu 57.
6Ankavalanso zokuta miyendo yake zamkuŵa, ndipo ankanyamula nthungo yamkuŵa pa phewa.
7Thunthu la mkondo wake linali ngati mtanda wa choombera nsalu. Mutu wa nkhondowo unkalemera ngati makilogramu asanu ndi aŵiri. Patsogolo pake pankapita munthu womunyamulira chishango.
8Goliyatiyo adaimirira ndi kufuula kwa ankhondo a Aisraele kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita kukonzekera nkhondo chotere? Ineyo ndine Mfilisti, inuyo ndinu akapolo a Saulo. Bwanji osati mungosankhula munthu pakati panupo, adze kwa ine.
9Ngati angathe kulimbana nane ndi kundipha, ndiye kuti Afilisti tonse tidzakhala akapolo anu. Koma ndikampambana ndi kumupha, inuyo mudzakhala akapolo athu ndi kumatigwirira ntchito.
10Tiwonane lero lino basi! Patseni munthu kuti ndimenyane naye.”
11Atamva mau a Mfilistiyo, Saulo ndi Aisraele onse adachita mantha nathyoka m'nkhongono.
Davide afika ku zithando za Saulo.12Davide anali mwana wa Mwefurati wa ku Betelehemu dzina lake Yese, amene anali ndi ana aamuna asanu ndi atatu. Pa nthaŵi ya ufumu wa Saulo, Yese anali atakalamba kale kwambiri.
13Ana ake aamuna anali aŵa: Eliyabu mwana wake wachisamba, wachiŵiri Abinadabu, ndipo wachitatu anali Sama.
14Davide anali mzime. Ana akuluakulu atatuwo ndiwo anali ku nkhondo ndi Saulo.
15Koma Davide ankapita ku zithando za Saulo, namabwerako nthaŵi zina kukaŵeta nkhosa za bambo wake ku Betelehemu.
16Pa masiku makumi anai Goliyati uja adakhala akutuluka, namadziwonetsa m'maŵa ndi madzulo.
17Tsiku lina Yese adauza mwana wake Davide kuti, “Abale ako uŵatengere makilogramu khumi a tirigu wokazinga, ndi mitanda khumi yabulediyi, ndipo upite nazo mofulumira ku zithando zao.
18Utengenso mphumphu khumizi za tchizi, upite nazo kwa mkulu wolamulira ankhondo. Ukaone m'mene abale ako akukhalira, ndipo ubwereko ndi chizindikiro china chosonyeza kuti ali bwino.
19Saulo, abale akowo ndi Aisraele ena, akumenyana nkhondo ndi Afilisti ku chigwa cha Ela.”
20Tsono Davide adanyamuka m'mamaŵa, nasiyira nkhosa munthu wina wozisunga. Adatenga zakudyazo napita, monga momwe bambo wake adaamlamulira. Adafika ku zithando pamene ankhondo ankandanda pa mzere wankhondo, nkufuula mfuu wankhondo.
21Aisraele ndi Afilisti adaandanda pa mzere wankhondo moyang'anana.
22Tsono zakudya zija Davide atasiyira munthu wosunga katundu, adathamangira kumene kunali ankhondo, nakalonjera abale ake.
23Pamene ankalankhula ndi abale akewo, adangoona Goliyati uja akutuluka ku magulu ankhondo a Afilisti, akulankhula zonyoza zomwe zija. Davide nkumva zimenezo.
24Aisraele onse atamuwona munthuyo, adathaŵa chifukwa ankamuwopa kwambiri.
25Ankati, “Muwonenitu munthu uja! Amangobwera, amangodzatinyoza Aisraelefe. Tsono amene amuphe, mfumu idati idzampatsa chuma chambiri, adzampatsanso mwana wake wamkazi kuti amkwatire. Banja la bambo wake silidzalipiranso msonkho.”
26Tsono Davide adafunsa anthu amene anali pafupi naye kuti, “Adzamtani munthu amene adzaphe Mfilistiyu ndi kuŵachotsa manyazi Aisraele? Mfilisti wosaumbalidwayu ndaninso kuti angamanyoze ankhondo a Mulungu wamoyo?”
27Anthu adamuuzanso zomwe zija zimene mfumu idaati idzachitire munthu wodzapha Goliyatiyo.
28Eliyabu, mkulu wake, atamva Davideyo akulankhula ndi anthu, adamupsera mtima, namufunsa kuti, “Wadzachita chiyani kuno? Nanga nkhosa zija wasiyira yani ku chipululu? Ndikudziŵa kuti ndiwe wodzikuza ndi woipa mtima. Wadza kuno kudzangoona nkhondo chabe!”
29Davide adati, “Kodi ndachimwa chiyani? Ndiye kuti ndileke nkulankhula komwe?”
30Tsono adachoka apo napita kwa wina namufunsa zokhazokhazo. Aliyense adamuyankhanso monga poyamba paja.
Davide amenyana ndi Goliyati.31Mau amene ankalankhula Davide aja atamveka, anthu adakafotokozera Saulo, ndipo Sauloyo adamuitanitsa.
32Tsono Davide adauza Saulo kuti, “Munthu aliyense asataye mtima chifukwa cha Mfilistiyu. Ineyo mnyamata wanune ndipita kukamenyana naye.”
33Saulo adamuuza kuti, “Sungathe kukamenyana naye Mfilistiyu, pakuti iwe ndiwe mnyamata, koma iyeyu ndi munthu wozoloŵera kumenya nkhondo kuyambira ubwana wake.”
34Apo Davide adauza Saulo kuti, “Mnyamata wanune ndinkaŵeta nkhosa za bambo wanga. Ndipo mkango ukafika, kapena chimbalangondo, ndi kugwira mwanawankhosa pakati pa nkhosazo,
35ndinkalondola mpaka kuchipha chilombocho ndi kupulumutsa mwanawankhosayo kukamwa kwake. Ndipo chikati chindiwukire, ndinkachigwira tchoŵa lake ndi kuchikantha mpaka kuchipha.
36Ineineyo ndidaphapo mikango ndi zimbalangondo zomwe. Tsono Mfilisti wosaumbalidwayu, ndidzamupha monga momwe ndidaphera zilombo zija, popeza kuti akunyoza magulu ankhondo a Mulungu wamoyo.
37Chauta amene adandipulumutsa ku mkango ndi ku chimbalangondo, adzandipulumutsa kwa Mfilistiyu.” Apo Saulo adauza Davide kuti, “Pita, Chauta akhale nawe.”
38Tsono Saulo adaveka Davide zovala zake zankhondo. Adamveka chisoti chamkuŵa ndi malaya achitsulo.
39Kenaka Davide adamanga lupanga m'chiwuno mwake. Atayesera kuyenda, adaona kuti akulephera poti sadazoloŵere. Ndiye adauza Saulo kuti, “Sindingathe kuyenda nazo, poti sindidazoloŵere.” Choncho adavula zovalazo.
40Tsono adatenga ndodo yake m'manja. Adatola miyala isanu yosalala yakumtsinje, naiika m'thumba lake lakubusa. Ali ndi khwenengwe m'manja, adapita kukakumana ndi Mfilisti uja.
Davide agonjetsa Goliyati.41Tsono Mfilistiyo adayambapo kupita kumene kunali Davide, munthu wonyamula chishango ali patsogolo pake.
42Ndipo atayang'ana Davideyo, adayamba kumnyoza, poona kuti anali mnyamata chabe, wofiirira ndiponso wa maonekedwe okongola.
43Tsono adafunsa Davide kuti, “Kodi ndine galu, kuti uzibwera kwa ine ndi ndodo?” Pompo adayamba kutemberera Davide potchula milungu yake.
44Kenaka adauza Davide kuti, “Idza kuno, mnofu wako ndidyetsera mbalame zamumlengalenga ndi zilombo zakuthengo.”
45Koma Davide adauza Mfilistiyo kuti, “Wadza kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo. Koma ine ndikudza kwa iwe m'dzina la Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa magulu ankhondo a Aisraele, amene iwe wamunyoza.
46Lero lomwe lino Chauta akupereka m'manja mwanga. Ndikulasa ndi kukugwetsa pansi, ndipo ndikudula mutu. Mitembo ya magulu ankhondo a Afilisti ndiipereka lero lino kwa mbalame zamumlengalenga, ndi kwa zilombo zakuthengo, kuti dziko lonse lapansi lidziŵe kuti kuli Mulungu ku dziko la Israele.
47Anthu onse amene asonkhanaŵa adzadziŵa kuti Chauta sapulumutsa anthu ndi lupanga kapena mkondo wokha. Wopambanitsa pa nkhondo ndi Chauta, ndipo akuperekani m'manja mwathu.”
48Tsono Mfilistiyo adasendera pafupi kuti akumane ndi Davide. Pomwepo Davideyo adathamanga mofulumira ku mzere wankhondo uja, kuti nayenso akakumane naye.
49Adapisa dzanja m'thumba natulutsamo mwala, ndipo adauponya namlasa pa mphumi Mfilistiyo. Mwalawo udamuloŵa m'mutu, ndipo Mfilistiyo adagwa pansi chafufumimba.
50 2Sam. 21.19 Choncho Davide adampambana Goliyati uja pomlasa ndi mwala wam'khwenengwe, namupha Mfilistiyo. M'manja mwa Davide munalibe konse lupanga.
512Sam. 21.19 Pompo adathamanga, nakaimirira pamwamba pa Mfilisti uja. Adasolola lupanga lake lomwe m'chimake, namtsiriza pomdula mutu.
Tsono Afilisti ataona kuti ngwazi yao yamphamvu pa nkhondo yafa, adathaŵa.
52Aisraele ndi anthu a ku dziko la Yuda adanyamuka akufuula, napirikitsa Afilisti aja mpaka ku Gati ndi ku zipata za Ekeroni. Tsono Afilisti ovulala ankagwa pa njira yonse kuyambira ku Saraimu mpaka ku Gati ndi Ekeroni.
53Ndipo Aisraele adabwererako kumene ankapirikitsa Afilisti kuja, nadzafunkha m'zithando zankhondo za Afilistiwo.
54Kenaka Davide adatenga mutu wa Mfilisti uja napita nawo ku Yerusalemu. Koma zida zokha za Mfilistiyo adaziika m'hema mwake.
Abwera ndi Davide kwa Saulo.55Pamene Saulo adaaona Davide akupita kukamenyana ndi Mfilisti uja, adafunsa Abinere mkulu wa ankhondo kuti, “Kodi iwe Abinere, mnyamatayu ndi mwana wa yani?” Abinere adayankha kuti, “Pepani inu amfumu muli apa, ine sindingadziŵe.”
56Apo mfumu idati, “Kafunse kuti kodi mnyamata ameneyu ndi mwana wa yani?”
57Tsono pamene Davide ankabwererako kumene adaakapha Mfilisti kuja, Abinere adamtenga napita naye kwa Saulo, mutu wa Mfilisti uja uli m'manja mwake.
58Saulo adafunsa Davide kuti, “Kodi mnyamata iwe, paja ndiwe mwana wa yani?” Davide adayankha kuti, “Ndine mwana wa mtumiki wanu Yese, wa ku Betelehemu.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.