Amo. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Imvani mau amene Chauta adalankhula,

mau okudzudzulani inu Aisraele,

ndiye kuti banja lonse

limene Iye adalitulutsa ku dziko la Ejipito.

Adanena kuti,

2“Ine ndidasankha ndi kusamala inu nokha

pakati pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi.

Tsono ndidzakulangani koposa

chifukwa cha machimo anu onse.”

Za ntchito ya mneneri

3“Kodi anthu aŵiri nkuyendera pamodzi,

osapangana?

4Kodi mkango umabangula m'nkhalango,

usanagwire nyama?

Kodi msona wa mkango umakhuluma m'phanga mwake,

usanagwire kanthu?

5Kodi mbalame nkukatera pa msampha pansi,

popanda nyambo yake?

Nanga msamphawo kodi nkufwamphuka pansipo,

usanakole kanthu?

6Kodi lipenga lankhondo nkulira mu mzinda,

anthu osachita mantha?

Nanga tsoka likagwera mzinda,

kodi si Chauta amene amachita zimenezo?

7Zoonadi, Ambuye Chauta sachita kanthu

osadziŵitsa atumiki ao, aneneri,

zimene akonzekera.

8Mkango ukabangula,

kodi sachita mantha ndani?

Ambuye Chauta akalankhula,

kodi ndani sadzalalika?”

Chilango cha Asamariya

9“Ulengeze kwa anthu okhala m'malinga a ku Asidodi,

ndiponso kwa okhala m'malinga a ku Ejipito,

uŵauze kuti akasonkhane ku mapiri a ku Samariya,

akaone zachipwirikiti ndi zachifwamba

zimene zikuchitika pakati pa anthu ake.”

10“Sadziŵa kuchita zolungama

amene amadzaza malinga ao

ndi zinthu zozipeza mwankhondo ndi mwakuba.”

Akuterotu Chauta.

11Nchifukwa chake Ambuye Chauta mau ao ndi aŵa:

“Adani adzalizinga dzikolo,

malinga ake adzaŵagwetsa,

ndipo adzafunkha zonse zam'menemo.”

12Zimene akunena Chauta ndi izi: “Monga mbusa amangotolako miyendo iŵiri kapena nsonga ya khutu la nkhosa yake ikajiwa ndi mkango, ndimo m'mene adzapulumukire Aisraele okhala ku Samariya, ngati zidutswa chabe za bedi.

13“Mverani, muŵaimbe mlandu am'banja la Yakobe,”

akutero Ambuye Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse.

14 2Maf. 23.15 “Pa tsiku limene ndidzalange Israele

chifukwa cha zolakwa zake,

maguwa a ku Betele ndidzaŵagumula,

ndipo nyanga za guwa zidzathyoka nkugwa pansi.

15Ndidzagwetseratu nyumba za nthaŵi

yachisanu ndi za nthaŵi yamafundi.

Nyumba zaminyanga zidzaonongeka,

ndithu nyumba zazikulu zidzaphwasuka.”

Akuterotu Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help