1
[Pakuti ufumu, mphamvu ndi ulemerero
ndi zanu kwamuyaya.
Amen.]
14 Mk. 11.25, 26 Mphu. 28.1-5 “Ndithu ngati mukhululukira anthu machimo ao, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani inunso.
15Koma ngati simukhululukira anthu machimo ao, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.
Za kusala zakudya16“Pamene mukusala zakudya, musamaonetsa nkhope zachisoni monga amachitira anthu achiphamaso aja. Iwo amaipitsa nkhope kuti anthu aone kuti akusala zakudya. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao.
17Yud. 10.3Koma iwe, pamene ukusala zakudya, samba m'maso nkudzola mafuta kumutu,
18kuti anthu asadziŵe kuti ukusala zakudya. Koma Atate ako amene ali osaoneka ndiwo adziŵe. Ndipo Atate akowo amene amaona zobisika, adzakupatsa mphotho.
Za chuma chakumwamba(Lk. 12.33-34)19 Yak. 5.2, 3 “Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba.
20Mphu. 29.11Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba.
21Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.
Maso ndiwo nyale za thupi(Lk. 11.34-36)22“Maso ndiwo nyale zounikira thupi la munthu. Ngati maso ako ali bwino, m'thupi mwako monse mumakhala kuŵala.
23Koma ngati maso ako sali bwino, m'thupi mwako monse mumakhala mdima. Tsono ngati kuŵala kumene kuli mwa iwe kusanduka mdima, mdima wakewo ndi wochita kuti goo!
Za Mulungu ndi Chuma(Lk. 16.13; 12.22-31)24“Munthu sangathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkumanyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.
25“Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadyanji, kapena mudzamwanji, kapena thupi lanu, kuti mudzavalanji. Kodi suja moyo umaposa chakudya? Kodi suja thupi limaposa zovala?
26Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
27Ndani mwa inu ndi maganizo ankhaŵa angathe kuwonjezera ngakhale tsiku limodzi pa moyo wake?
28“Ndipo mumaderanji nkhaŵa ndi zovala? Onani maluŵa akuthengo m'mene amakulira. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu ai.
291Maf. 10.4-7; 2Mbi. 9.3-6 Komatu kunena zoona, ngakhale mfumu Solomoni yemwe, mu ulemerero wake wonse, sankavala zokongola kulingana ndi limodzi lomwe mwa maluŵa ameneŵa.
30Tsono ngati Mulungu amaveka motere udzu wakuthengo, umene ungokhalapo lero lokha, maŵa lino nkuponyedwa pa moto, nanji inuyo, angapande kukuvekani, inu a chikhulupiriro chochepanu?
31“Nchifukwa chake musamada nkhaŵa nkumanena kuti, ‘Tidzadyanji? Tidzamwanji? Tidzavalanji?’
32Paja zimenezi amazifunafuna ndi anthu akunja. Atate anu akumwamba amadziŵa kuti mukuzisoŵa zonsezi.
33Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
34Motero musadere nkhaŵa zamaŵa. Zamaŵa nzamaŵa. Tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.