1Inu Chauta, imvani pemphero la ine munthu wolungama,
imvani kupemba kwanga.
Tcherani khutu kuti mumve mau
ochokera kwa ine, munthu wosanyengane.
2Kusalakwa kwanga kuwonekere poyera pa chiweruzo chanu,
maso anu aone kulungama kwanga.
3Ngakhale muyese mtima wanga,
kapena kundipenyetsetsa usiku,
kaya mundiyang'anitsitse chotani,
mudzapeza kuti ndilibe mlandu.
Pakamwa panga sipalankhula zoipa.
4Kunena za ntchito za anthu,
ine posunga mau anu,
sindidatsate za anthu andeu.
5Ndayenda m'njira zanu nthaŵi zonse,
sindidapatuke konse.
6Ndikupemphera kwa Inu Mulungu,
chifukwa mudzandiyankha.
Tcherani khutu kuti mumve mau anga.
7Onetsani chifundo chanu pakuchita zodabwitsa,
Inu amene mumaŵapulumutsa ndi dzanja lanu lamanja
onse obwera kwa Inu, kuthaŵa adani ao.
8Mundisunge ngati mwana wa diso,
munditeteze pansi pa mapiko anu,
9kuti asandiwone anthu oipa ofuna kupasula,
ndiye kuti adani anga oopsaŵa amene akundizinga.
10Mitima yao ilibe chifundo,
amalankhula modzikuza.
11Amangondilondola ndi kundizinga.
Amandiyang'ana kuti apeze njira yondigwetsera pansi.
12Ali ngati mkango wofunitsitsa kuti ukadzule,
ngati chilombo cholusa cholalira.
13Dzambatukani, Inu Chauta,
mukumane nawo ndi kuŵagonjetsa.
Mundipulumutse ndi lupanga lanu kwa anthu oipawo.
14Inu Chauta, ndi dzanja lanu mundilanditse kwa adani,
kwa anthu amene moyo wao umangosamala zapansipano.
Muŵalange ndi zoŵaŵa zimene mudaŵasungira.
Nawonso ana awo akhale nazo zambiri,
ndipo iwowo asiyireko ana aonso.
15Koma ine m'kulungama kwanga
ndidzaona nkhope yanu.
Tsono ine nditadzuka,
ndidzakondwa kotheratu poonana ndi Inu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.