Mphu. 48 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Eliya

1 1Maf. 17.1-24; 18.38; 19.15, 16; 2Maf. 1.10-16; 2.11; Mal. 4.5, 6 Pambuyo pake padabwera Eliya, mneneri

wonga moto,

mau ake ankaŵala ngati nsakali.

2Adadzetsa njala pa anthu,

motero anthu ambiri adafa chifukwa cha

changu chake.

3Potsata mau a Ambuye adatseka thambo lakumwamba,

ndipo adatsitsa moto katatu.

4Iwe Eliya, ntchito zako zinali zozizwitsa kwabasi.

Ndani angathe kunyadira ntchito zotere?

5Udaukitsa munthu wakufa m'manda

ndi mau a Mulungu Wopambanazonse.

6Udagwetsa mafumu m'chiwonongeko,

ndipo anthu otchuka udaŵagwetsa pansi

kuchokera pabedi pao.

7Udamva mau odzudzula ku phiri la Sinai,

mau otsimikiza za chilango ku phiri la Horebu

8Tsono udadzoza mafumu kuti azilipsira,

ndi aneneri kuti aloŵe m'malo mwako.

9Udatengedwa kupita kumwamba ndi kamvulumvulu

wamoto m'galeta lokokedwa ndi akavalo amoto.

10Zidalembedwa kuti udzabwera pa nthaŵi yake,

kudzaziziritsa mkwiyo wa Mulungu,

ukali wake usanabuke,

kudzayanjanitsa bambo ndi mwana

ndi kukhazikitsanso mafuko a Yakobe.

11Ngodala amene adzakuwona,

ndiponso amene adafa ali ndi chikondi.

Ndithudi ifenso tidzakhala ndi moyo.

Elisa

12 2Maf. 2.9, 13 Pamene paja Eliya adatengedwa ndi kamvulumvulu,

Elisa adadzazidwa ndi nzeru zake.

Pa moyo wake wonse sadachite mantha ndi mfumu ina iliyonse,

ndipo panalibe munthu womgonjetsa.

13 2Maf. 13.20, 21 Panalibe ntchito yomukanika.

Ngakhale atafa, thupi lake lidatchula mau olosa.

14Ali moyo adachita zinthu zozizwitsa,

ndipo atafa ntchito zake zidakhalanso zodabwitsa.

Chilango cha anthu osakhulupirika

15 2Maf. 18.11, 12 Ngakhale zinthu zidatero,

anthu sadatembenuke mtima kapena kuleka machimo ao.

Mulungu adaŵachotsa m'dziko mwao

naŵabalalitsa m'dziko lonse lapansi.

Anthu oŵerengeka okha adatsalapo,

ndipo ankalamulidwa ndi mfumu ya ku banja la Davide.

16Ena mwa iwowo adachita zokomera Ambuye,

koma ena ankachimwirachimwirabe.

Hezekiya

17 2Maf. 20.20 Hezekiya adamangira mzinda wake linga

nadzetsa madzi m'kati mwa mzindawo.

Adaboola thanthwe ndi zitsulo,

napanga maiŵe osungiramo madzi.

18 2Maf. 18.13-17 Pa nthaŵi ya ufumu wa Hezekiya,

Senakeribu adadzathira nkhondo,

natuma Rabisake mtsogoleri wankhondo.

Adathira nkhondo mzinda wa Ziyoni,

nayamba kudzikuza zedi m'kunyada kwake.

19Tsono anthu adataya mtima, nkumanjenjemera,

ndipo adayamba kuda nkhaŵa ngati mkazi amene akuchira.

20 2Maf. 19.15-20, 35 Adapempha Ambuye achifundo,

kuchita kukweza manja kwa Iwo.

Kumwamba Woyera uja adamva pemphero lao msanga,

ndipo adatuma Yesaya kuti aŵapulumutse.

21Mulungu adagwetsa zithando zankhondo za Aasiriya,

ndipo mngelo wake adaŵaonongeratu.

Yesaya

22Zidatero pakuti Hezekiya adachita zokomera Ambuye,

ndi kusunga makhalidwe a kholo lake Davide,

monga adamulangizira Yesaya,

mneneri wotchuka amene ankalosa zokhulupirika.

23 2Maf. 20.10, 11 Pa nthaŵi ya Yesaya, dzuŵa lidabwerera m'mbuyo

ndipo adaonjezera masiku a moyo wa mfumu.

24Mwa mphamvu za mzimu adaona zakutsogolo

ndipo adasangalatsa anthu odandaula ku Ziyoni.

25Adaulula zinthu zakutsogolo mpaka kutha kwa nthaŵi,

nafotokoza zinsinsi zina zobisika, zisanachitike konse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help