Yos. 11 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yoswa agonjetsa Yabini pamodzi ndi ogwirizana naye.

1Mbiri ya zimene zinkachitikazi idamfika Yabini, mfumu ya ku Hazori. Motero iyeyo adatumiza uthenga kwa Yobabu mfumu ya ku Madoni, ndiponso kwa mafumu a ku Simironi ndi Akisafu.

2Adatumizanso uthenga kwa mafumu a ku dziko lamapiri kumpoto kwa chigwa cha Yordani, kumwera kwa nyanja ya Galilea, m'dziko la chigwa cha Yordani ndiponso kumbali kwa nyanja, kufupi ndi Dori.

3Adatumizanso uthenga kwa Akanani a pa mbali zonse ziŵiri za Yordani, kwa Aamori, Ahiti, Aperizi ndi Ayebusi a ku dziko lamapiri, mpakanso kwa Ahivi amene ankakhala patsinde pa phiri la Heremoni m'dziko la Mizipa.

4Mafumuwo adabwera ndi ankhondo ao onse, ndipo kuchuluka kwao kwa ankhondowo kunali ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Anali ndi akavalo ambiri, pamodzi ndi magaleta omwe.

5Mafumu onseŵa adasonkhana pamodzi, nakamanga zithando ku mtsinje wa Meromu, kuti alimbane ndi Aisraele.

6Chauta adauza Yoswa kuti, “Usaŵaope amenewo. Maŵa pa nthaŵi yonga yomwe ino, adzaphedwa onsewo. Akavalo ao muŵalumaze, ndipo mutenthe magaleta ao.”

7Motero Yoswa pamodzi ndi anthu ake adaŵathira nkhondo modzidzimutsa ku mtsinje wa Meromu.

8Chauta adapatsa Aisraelewo mphamvu zogonjetsera adaniwo, mwakuti adaŵapambana kwenikweni, naŵapirikitsa mpaka kumpoto ku Sidoni Wamkulu ndi ku Misirefoti-Maimu ndiponso kuvuma, ku chigwa cha Mizipa. Adapha onsewo, osatsala ndi mmodzi yemwe.

9Yoswa adangoŵachita zomwe Chauta adalamula. Adalumaza akavalo, natentha magaleta.

10Pambuyo pake Yoswa adabwera nagonjetsa mzinda wa Hazori ndi kupha mfumu yake. Nthaŵi imeneyo nkuti mzinda wa Hazori uli wamphamvu kupambana maufumu ena onse.

11Adapha aliyense kumeneko osasiya wamoyo ndi mmodzi yemwe, ndipo mzinda wonsewo adauthira moto.

12Yoswa adagwira mafumu onsewo pamodzi ndi mizinda yao yomwe. Adalamula kuti aphedwe onsewo, potsata lamulo la Mose mtumiki wa Mulungu.

13Komabe Aisraelewo sadatenthe mizinda yomangidwa pa magomo, kupatula mzinda wa Hazori umene Yoswa adauthira moto.

14Tsono Aisraele adafunkha zinthu zonse zabwino za m'mizinda imeneyo, pamodzi ndi zoŵeta zomwe monga ng'ombe, nazisunga kuti zikhale zao. Koma adani okha adaphedwa onse, osatsala ndi mmodzi yemwe.

15Monga momwe Chauta adaalamulira mtumiki wake Mose, momwemo Moseyo adapereka malamulowo kwa Yoswa, ndipo Yoswa adachitadi zonse zimene Chauta adalamula Mose.

Dziko limene Yoswa adalanda.

16Yoswa adagonjetsa dziko lonse, kuyambira dziko lamapiri, dziko lonse la Negebu lakumwera, dziko lonse la Goseni, chigwa chonse, dziko la Araba, dziko lonse la Israele lamapiri ndi chigwa chake chomwe,

17kuchokera ku phiri la Halaki kufupi ndi Seiri mpaka ku Baala-Gadi m'chigwa cha Lebanoni, kumwera kwa phiri la Heremoni. Adapha mafumu ao onse,

18atalimbana nawo nthaŵi yaitali.

19Palibe ndi mfumu imodzi yomwe imene idakambirana zamtendere ndi Aisraele, kupatula Ahivi okha amene ankakhala ku Gibiyoni. Koma ena onse adachita choŵagonjetsa ndi nkhondo.

20Deut. 7.16 Chauta adaŵalimbitsa mtima iwowo kuti alimbane ndi Aisraele, kuti motero aonongeke onse, ndipo aphedwe mopanda chifundo. Zimenezi ndizo zimene Chauta adaalamula Mose.

21Nthaŵi imeneyi nkuti Yoswa atapita kukaonongeratu mtundu wa Aanaki. Iwowo anali kukhala m'dziko lija lamapiri, monga ku Hebroni, ku Debiri, ku Anabu ndi ku maiko onse amapiri aja a Yuda ndi a Israele. Yoswa adaŵaononga kwathunthu onsewo ndi mizinda yao yomwe.

22Palibe ndi Mwanakimu mmodzi yemwe amene adatsalako m'dziko lonse la Aisraele, komabe ku Gaza, ku Gati ndi ku Asidodi adatsala pang'ono.

23Choncho Yoswa adagonjetsa dziko lonselo potsata mau amene Chauta adaalamula Mose. Chauta adapereka dziko kwa Aisraele kuti likhale lao, ndipo adaligaŵagaŵa kuti fuko lililonse likhale ndi gawo lake. Motero anthu onse adapumula osamenyanso nkhondo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help