Mt. 8 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yesu achiritsa munthu wakhate

1Yesu atatsika kuphiri kuja, anthu ambirimbiri adamtsatira.

2Tsono munthu wina wakhate adadzamugwadira nati, “Ambuye, mutafuna mungathe kundichiritsa.”

3Yesu adatambalitsa dzanja nkumukhudza, nati, “Chabwino, ndikufuna, chira!” Pomwepo khate lake lija lidatha, ndipo adachiradi.

4Lev. 14.1-32 Tsono Yesu adamuuza kuti, “Chenjera, usakambire wina aliyense zimenezi. Ingopita, ukadziwonetse kwa wansembe, ndipo ukapereke nsembe adalamula Mose ija. Imeneyi ikhale yotsimikizira anthu onse kuti wachiradi.”

Za mkulu wa asilikali wachiroma

5Pamene Yesu ankaloŵa m'mudzi wa Kapernao, mkulu wina wolamulira gulu la asilikali 100 achiroma adadza kwa Iye.

6Adampempha kuti, “Ambuye, wantchito wanga ali gone kunyumbaku. Sakutha kuyenda, ndipo akumva kupweteka kwambiri.”

7Yesu adamuuza kuti, “Chabwino, ndibwera kudzamchiritsa.”

8Koma mkulu uja adati, “Ambuye, sindili woyenera kuti Inu nkuloŵa m'nyumba mwanga. Mungonena mau okha, ndipo wantchito wangayo achira.

9Bar. 3.33-35Inetu ndili ndi akuluakulu ondilamulira, komanso ndili ndi asilikali amene ineyo ndimaŵalamulira. Ndimati ndikauza wina kuti, ‘Pita,’ amapitadi. Ndikauzanso wina kuti, ‘Bwera,’ amabweradi. Ndipo ndikauza kapolo wanga kuti, ‘Chita chakuti,’ amachitadi.”

10Yesu atamva zimenezi, adachita chidwi, ndipo adauza anthu amene ankamutsata aja kuti, “Kunena zoona, ngakhale pakati pa Aisraele sindidapeze chikhulupiriro chotere.

11Lk. 13.29Ndithu ndikunenetsa kuti ambiri adzabwera kuchokera kuvuma ndi kuzambwe nadzakhala nao pa phwando mu Ufumu wakumwamba pamodzi ndi Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.

12Mt. 22.13; 25.30; Lk. 13.28Koma chonsecho amene akadayenera kukhala mu Ufumuwo, adzaŵaponya kunja, ku mdima. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano chifukwa cha zoŵaŵa.”

13Kenaka pouza mkulu wa asilikali uja Yesu adati, “Inu pitani bwino, zikuchitikireni monga momwe mwakhulupiriramu.” Tsono wantchito wake uja adachira nthaŵi yomweyo.

Yesu achiritsa anthu ambiri(Mk. 1.29-34; Lk. 4.38-41)

14Pamene Yesu adakaloŵa m'nyumba ya Petro, adaona apongozi a Petro ali gone, akudwala malungo.

15Adakhudza amaiwo pa dzanja, ndipo malungowo adatha. Pomwepo amai aja adadzuka nayamba kukonzera Yesu chakudya.

16Madzulo amenewo, anthu adabwera kwa Yesu ndi anzao ambiri ogwidwa ndi mizimu yoipa. Yesu adaitulutsa mizimuyo ndi mau chabe, ndipo onse amene ankadwala adaŵachiritsa.

17Yes. 53.4Adachita zimenezi kuti zipherezere zimene mneneri Yesaya adaanena zakuti, “Iye adatenga zofooka zathu, adasenza nthenda zathu.”

Za kutsata Yesu(Lk. 9.57-62)

18Pamene Yesu adaona chinamtindi cha anthu amene adaamuzinga, adauza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tiwolokere tsidya linalo.”

19Koma nthaŵi yomweyo padafika mphunzitsi wina wa Malamulo namuuza kuti, “Aphunzitsi, ndizikutsatani kulikonse kumene muzipita.”

20Yesu adamuyankha kuti, “Nkhandwe zili ndi michembo yake, mbalame zili ndi zisa zake, koma Mwana wa Munthu alibe mpogoneka mutu pomwe.”

21 Tob. 4.3, 4 Wophunzira wake wina adauza Yesu kuti, “Ambuye, mundilole ndiyambe ndakaika maliro a atate anga.”

22Koma Yesu adamuuza kuti, “Iweyo unditsate, aleke akufa aziika akufa anzao.”

Yesu athetsa namondwe(Mk. 4.35-41; Lk. 8.22-25)

23Yesu adaloŵa m'chombo, ndipo ophunzira ake adatsagana naye.

24Tsono padauka namondwe woopsa panyanjapo, kotero kuti mafunde ankaloŵa m'chombomo. Koma Yesu anali m'tulo.

25Pamenepo ophunzira ake aja adamudzutsa, adati, “Ambuye, tipulumutseni, tikumiratu!”

26Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuchita mantha, inu anthu a chikhulupiriro chochepa?” Atatero adaimirira nkudzudzula mphepoyo ndi nyanjayo, kenaka padagwa bata lalikulu ndithu.

27Ophunzira aja adazizwa nati, “Kodi ameneyu ndi munthu wotani kuti ngakhale mphepo ndi nyanja yomwe zizimumvera?”

Yesu achiritsa anthu ogwidwa ndi mizimu yoipa(Mk. 5.1-20; Lk. 8.26-39)

28Yesu atafika ku tsidya la nyanja, ku dera la Agadara, anthu aŵiri ogwidwa ndi mizimu yoipa adadzakumana naye kuchokera ku manda. Anali aukali kwambiri, kotero kuti panalibe munthu ndi mmodzi yemwe wotha kudzera njira imeneyo.

29Mwadzidzidzi anthuwo adayamba kufuula kuti, “Kodi takuputani chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Kodi mwabwera kuno kudzatizunza nthaŵi isanakwane?”

30Pafupi pomwepo pankadya gulu lalikulu la nkhumba.

31Tsono mizimu yoipa ija idapempha Yesu kuti, “Mukatitulutsa, bwanji mutitume kuti tikaloŵe m'gulu la nkhumba zili apozo.”

32Yesu adaiwuza kuti, “Chabwino, pitani!” Iyo idatuluka nkukaloŵadi m'nkhumbazo. Pomwepo gulu lonselo lidaguduka kutsika chitunda chija mwaliŵiro, nkukadziponya m'nyanja mpaka kufera m'madzimo.

33Oŵeta nkhumbazo adathaŵa. Atakaloŵa mu mzinda, adakasimbira anthu zonse zimene zidachitika, ndiponso zimene zidaŵaonekera ogwidwa ndi mizimu yoipa aja.

34Pamenepo anthu onse amumzindamo adatuluka kuti akakumane ndi Yesu. Tsono atampeza, adamupempha kuti achoke ku dera laolo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help