1Mose adakwera phiri la Nebo kuchokera ku zigwa za Mowabu. Adakafika mpaka pamwamba pa phiri la Pisiga kuvuma kwa Yeriko. Ndipo kumeneko Chauta adamuwonetsa dziko lonse, dziko la Giliyadi mpaka ku dziko la Dani.
2Dziko lonse la Nafutali, maiko onse a Efuremu ndi Manase, ndi dziko la Yuda mpaka kukafika ku Nyanja Yaikulu.
3Adamuwonetsanso chigawo chakumwera cha Negebu, ndi chigwa chimene chimafika mpaka ku Yeriko, mzinda wa mitengo ya migwalangwa, mpaka ku Zowari.
4Gen. 12.7; Gen. 26.3; Gen. 28.13 Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Ilo ndilo dziko limene lija ndidalonjeza Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, kuti ndidzapatsa zidzukulu zao. Ndakulola kuti uliwone, koma kuloŵamo kokha sindikulola.”
5Choncho Mose, mtumiki wa Chauta, adamwalira kumeneko m'dziko la Mowabu, monga momwe Chauta adanenera.
6Chauta adamuika ku Mowabu komweko m'chigwa, moyang'anana ndi mudzi wa Betepeori. Koma palibe ndi mmodzi yemwe amene akudziŵa malo enieni a mandawo.
7Mose adamwalira ali wa zaka 120. Koma anali wamphamvube, ndipo maso ake anali akuthwabe.
8Aisraele adalira maliro ake masiku makumi atatu m'chigwa cha Mowabu. Ndipo nthaŵi yolira maliro idatha.
9Tsono Yoswa, mwana wa Nuni, adadzazidwa ndi nzeru, chifukwa Mose adaamsanjika manja kuti aloŵe m'malo mwake. Aisraele adamvera Yoswa, ndi kutsata malamulo onse amene Chauta adaŵapatsa kudzera mwa Mose.
10Eks. 33.11; Mphu. 45.1-5 Kuyambira pamenepo, sadakhaleponso mneneri wina aliyense wonga Mose. Chauta ankalankhula naye pamasompamaso.
11Palibe mneneri wina aliyense amene adachitapo zozizwitsa ndi zodabwitsa monga zimene Chauta adauza Mose kuti achite pamaso pa mfumu ya ku Ejipito, ndi pa akulu ake, ndi m'dziko lake lonse.
12Palibe mneneri wina aliyense amene adachita zinthu zazikulu ndi zoopsa zonga zimene adachita Mose pamaso pa Aisraele onse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.