1Lonjezo la Mulungu lakuti tidzaloŵa mu mpumulo umene Iye adatikonzera, lilipobe. Tsono tichenjere kuti pasakhale wina aliyense mwa inu wopezeka kuti walephera kuloŵamo.
2Paja ifenso tidaumva Uthenga Wabwino, monga iwo aja. Koma iwowo sadapindule nawo mau olalikidwawo, popeza kuti adangoŵamva, koma osaŵakhulupirira.
3Mas. 95.11 Ife okhulupirirafe tikuloŵamo mu mpumulowo. Paja Mulungu adaanena kuti,
“Ndili wokwiya ndidalumbira kuti,
‘Sadzaloŵa konse mu mpumulo
umene ndidaŵakonzera.’ ”
Adaanena zimenezi, ngakhale anali atatsiriza ntchito zake zonse za kulenga dziko lapansi.
4Gen. 2.2 Pena pake ponena za tsiku lachisanu ndi chiŵiri pali mau akuti, “Mulungu adapumula pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, kuleka ntchito zake zonse.”
5Mas. 95.11 Panonso akunena za zomwezo pamene akuti,
“Sadzaloŵa konse mu mpumulo
umene ndidaŵakonzera.”
6Mulungu adakonza kuti ena aloŵe ndithu mu mpumulowo, koma aja adaamva Uthenga Wabwino poyambaŵa sadaloŵemo chifukwa cha kusamvera.
7Mas. 95.7, 8 Nchifukwa chake Mulungu adaikanso tsiku lina, lotchedwa kuti “Lero”. Patapita nthaŵi yaitali Mulungu adalankhula za tsiku lomweli kudzera mwa Davide ponena mau aja tatchula kaleŵa, akuti,
“Lero, mukamva mau a Mulungu,
musaumitse mitima yanu.”
8 Deut. 31.7; Yos. 22.4 Chifukwatu Yoswa akadaŵaloŵetsa anthuwo mu mpumulo uja, sibwenzi pambuyo pake atanena za tsiku linanso.
9Nchifukwa chake tsono mpumulo wonga wa pa Sabata waŵatsalirabe anthu a Mulungu.
10Gen. 2.2 Paja munthu woloŵa mu mpumulo umene Mulungu adalonjeza, nayenso amapumula, kuleka ntchito zake, monga momwe Mulungu adaapumulira, kuleka ntchito zake.
11Tiyesetse tsono kuloŵa mu mpumulowo, kuwopa kuti wina aliyense angakhale wosamvera monga iwo aja, nalephera kuloŵamo.
12Paja mau a Mulungu ndi amoyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amabaya mpaka molumikizirana mwa moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana mfundo ndi mafuta a m'mafupa. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m'mitima mwao.
13Lun. 1.6Pamaso pa Mulungu palibe kanthu kobisika, zonse zili poyera ndipo nzovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.
Yesu ndiye Mkulu wa ansembe wopambana14Tiyeni tsono, tigwiritse chikhulupiriro chimene timavomereza. Pakuti tili naye Mkulu wa ansembe wopambana, amene adapita mpaka kukafika kumwamba kwenikweni kwa Mulungu. Iyeyu ndi Yesu, Mwana wa Mulungu.
15Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse.
16Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.