1 Am. 14 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Chaka cha 172, mfumu Demetriyo adasonkhanitsa ankhondo ake nanka ku Mediya, kuti akapezeko omthandiza kumenya nkhondo ndi Trifone.

2Arisake, mfumu ya ku Persiya ndi Mediya, atamva kuti Demetriyo waloŵa m'dziko lake, adatuma mmodzi mwa atsogoleri ake ankhondo kuti akamgwire wamoyo.

3Iyeyo adapita, nagonjetsa gulu la ankhondo a Demetriyo. Adamgwiradi nkubwera naye kwa Arisake, iyeyu nkumuika m'ndende.

4Dziko la Yudeya lidakhala pa mtendere

masiku onse a Simoni.

Ankafunira zabwino anthu a mtundu wake.

Ulamuliro wake unkasangalatsa anthu ake,

monga unaliri ulemu umene ankamupatsa,

pa masiku a moyo wake wonse.

5Adaonjezera pa ulemerero wake,

adalanda Yopa namangako dooko,

loti azikafikira ku zilumba zam'nyanja.

6Adakuza malire a dziko la mtundu wake,

nakhazikitsa ulamuliro wake wonse pa dzikolo.

7Adabweza Ayuda ambiri okhala ku ukapolo.

Adalanda Gazara, Betizure ndi boma

lankhondo la ku Yerusalemu.

Adachotsamo zoipa zonse,

ndipo sipadaoneke munthu ndi mmodzi yemwe

wotha kumletsa.

8Anthu ankalima minda yao mwamtendere.

Mindayo inkabereka bwino,

ndipo mitengo inkabala zipatso zake.

9Nkhalamba zinkakhala pansi m'mabwalo

zikukambirana za zinthu zokondweretsa.

Anyamata ankavala zovala zakaso ndi zankhondo.

10Simoni ankapereka zakudya ku mizinda,

ndipo ankailimbitsa ndi malinga

ndi zida zankhondo.

Motero dzina lake lidatchuka

mpaka ku malire a dziko lapansi pano.

11Adakhazikitsa mtendere m'dziko lake,

ndipo Aisraele ankakondwa kosaneneka.

12Aliyense ankakhala pansi pa mtengo

wake wa mpesa ndi wa mkuyu,

panalibe woŵaopsa.

13Sipadatsale ndi mmodzi yemwe womenyana

nawo nkhondo,

mafumu a adani anali ataŵagonjetsa

masiku amenewo.

14Mwa anthu a mtundu wake

Simoni ankathandiza anthu otsika onse,

ankatsata mosamala Malamulo,

ndipo adachotsa aliyense wokana chipembedzo

ndi woipa.

15Adakometsa ulemerero wa Nyumba ya Mulungu,

naonjezera ziŵiya za m'malo opatulika.

Simoni ayanjananso ndi Aroma ndi Asparta

16Atamva ku Roma ndi ku Sparta kuti Yonatani adafa, anthu adamva chisoni chachikulu.

17Adamvanso kuti Simoni mbale wake wakhala mkulu wa ansembe m'malo mwake, ndipo kuti akulamulira dziko lonse ndi mizinda yake.

181Am. 8.22Choncho adamlembera mau pa mabolodi amkuŵa akuti akupalana nayenso chibwenzi chomwe chija adaapalana ndi Yudasi ndi Yonatani abale ake.

19Adaŵerenga makalatawo pa msonkhano ku Yerusalemu.

20Aŵa ndiwo mau amene Asparta adatumiza: “Ife akuluakulu a ku Sparta ndi anthu ake tikupereka moni kwa Simoni mkulu wa ansembe, kwa akuluakulu, kwa ansembe ndi kwa Ayuda ena onse.

21Akazembe amene mudaŵatuma kwathu adatisimbira za ulemu ndi ulemerero wanu, ndipo tidakondwera ndi kufika kwao.

22Tsono tidalemba m'buku lathu la misonkhano mau aŵa otikumbutsa zimenezo: ‘Numeniyo mwana wa Antioko ndi Antipatere mwana wa Yasoni, akazembe a Ayuda, adabwera kwa ife kuti adzapalane nafenso chibwenzi.’

23Tsono anthu athu adakondwera pa kuŵalandira ndi ulemu, ndipo taika kalata ya mau ao m'mabuku osungiramo zam'dziko, kuti Asparta aziŵakumbukira. Talemberanso Simoni, mkulu wa ansembe, kalata yonena zokhazokhazo.”

24Pambuyo pake Simoni adatuma Numeniyo ku Roma ndi chishango chachikulu chagolide, chimene kulemera kwake kunali makilogramu 500, pofuna kutsimikizanso chiyanjano chao.

Ayuda atamanda Simoni

25Ayuda atamva zimenezo, adayamba kufunsana kuti, “Kodi tiŵachitire chiyani Simoni ndi ana ake, kuti tiŵathokoze?

26Pajatu iwoŵa ndi atetezi athu, iye uja pamodzi ndi abale ake ndi onse a pa banja la atate ake. Pomenya nkhondo, achotsa m'dziko adani a Aisraele, ndipo atikhalitsa pa mtendere.” Tsono adalemba zimenezo pa mabolodi amkuŵa amene adaŵapachika pa zipilala ku phiri la Ziyoni.

27Mau ake ndi aŵa: “Tsiku la 18 mwezi wa Eluli, chake cha 172, chaka chachitatu cha ulamuliro wa Simoni, mkulu wa ansembe, ku Asarameli,

28ku msonkhano waukulu wa ansembe, anthu, atsogoleri a fuko lathu ndi atsogoleri a dziko, adalalika izi:

29“Pa nkhondo zambiri zimene zidasautsa dziko lathu, Simoni, mwana wa Matatiasi, mmodzi mwa ana a Yowaribu, pamodzi ndi abale ake, adadzipereka ku zoopsa, namenyana nkhondo ndi adani a mtundu wao. Adatero pofuna kuti asunge Nyumba ya Mulungu ndi Malamulo. Motero adatengera mtundu wathu ulemu waukulu.

30Yonatani adalunzanitsa anthu a fuko lake, ndipo adakhala mkulu wao wa ansembe. Pambuyo pake adamwalira.

31Nthaŵi ina adani adaaganiza zothira nkhondo dziko lake kuti aliwononge ndi kulanda Nyumba ya Mulungu.

32Pamenepo Simoni adadzambatuka namenyera nkhondo mtundu wake. Adamwaza ndalama zambiri zakezake. Adaperekanso zida zankhondo kwa anthu oloŵa m'gulu la ankhondo a m'dziko lake, nkumaŵapatsa malipiro ao.

33Adalimbitsa malinga a mizinda ya ku Yudeya ndi a mzinda wa Betizure. Mzinda umenewu uli ku malire a dziko, kumene kale kunali boma lankhondo la adani. Iyeyo adaikako boma la Ayuda.

34Adalimbitsanso linga la Yopa, mzinda umene uli ku nyanja, ndiponso la Gaza, mzinda umene uli ku malire a Azoto, kumene kale kunali adani. Adakhazikako Ayuda, ndipo ankaŵapatsa zonse zofunika pa moyo wao.

35“Anthu onse adaona machitidwe okhulupirika a Simoni ndi ulemu umene iyeyo ankafuna kupatsa dziko lake. Tsono adamsankhula kuti akhale mfumu yao ndi mkulu wa ansembe, chifukwa cha ntchito zake zonse zobweretsa chilungamo ndi zoonetsa kukhulupirika kwake kwa mtundu wake. Chifukwa china nchakuti adaafunitsa mwa njira iliyonse kukweza ulemerero wa anthu ake.

36Nthaŵi yonse ya moyo wake, adapititsa zinthu m'tsogolo. Adachotsa anthu akunja ku dziko la Ayuda, adapirikitsa anthu okhala m'boma lankhondo la mu mzinda wa Davide ku Yerusalemu. Anthu ameneŵa ankangoyendayenda ndi kumaipitsa malo oyandikana ndi Nyumba ya Mulungu. Potero ankanyoza kwakukulu kuyera kwake.

37Adaikamo asilikali achiyuda, ndipo adalilimbitsa bomalo kuti athe kuteteza dziko ndi mzinda. Malinga a Yerusalemu adaŵakweza kutalika kwake.

38“Chifukwa cha zimenezi mfumu Demetriyo adatsimikiza zakuti Simoniyo akhale mkulu wa ansembe.

39Motero ankamuŵerengera ngati mmodzi mwa abwenzi ake, ndipo adamchitira zaulemu kwambiri.

40Adaatero chifukwa anali atamva kuti Aroma adaachita chibwenzi ndi chiyanjano ndi Ayuda mwa chibale chenicheni, ndipo kuti adaalandira ndi ulemu amithenga a Simoni.

41“Tsono Ayuda ndi ansembe ao adamvana kuti Simoni akhale mtsogoleri wao ndi mkulu wa ansembe nthaŵi zonse, mpaka kuti adzaoneke mneneri wokhulupirika.

42Adati akhalenso mtsogoleri wa ankhondo, ndiponso kuti adzakhale wosamalira Nyumba ya Mulungu. Iye yemweyonso azidzasankhula akapitao oyang'anira ntchito za m'dziko lonse, zida zankhondo ndi nyumba zankhondo. Adatinso azidzasamala malo opatulika.

43Aliyense ankayenera kudzamvera iye. Tsono pa zipangano zonse za boma m'dzikomo, iye adzalembepo dzina lake, ndipo mwiniwakeyo azidzavala nsalu zaulemu zofiirira ndi lamba wagolide.

44“Pasakhale munthu aliyense, ngakhale wansembe, wothetsa zinthu tazinenazi, kapena kuchita msonkhano popanda chilolezo cha iyeyo, kapena woyesera kuvala zovala zofiirira kapena kumanga lamba wagolide.

45Aliyense wosatsata lamuloli kapena wonyoza ngakhale chimodzi chokha mwa zimenezi, adzayenera kumlanga.”

46Anthu onse adavomera kupatsa Simoni mphamvu ndi ulemerero monga momwe zidaanenera zogamulazo.

47Simoni adalola, navomera kukhala mkulu wa ansembe, mtsogoleri wa Ayuda ndi wa ansembe, ndiponso mtetezi wa iwo onse.

48Anthu adapangana kuti mauwo alembedwe pa mobolodi amkuŵa ndi kuŵaika poyera m'bwalo la Nyumba ya Mulungu.

49Adapangananso kuti mabolodi ena otere alembedwe ndi kusungidwa m'chipinda mosungira chuma cha ku Nyumba ya Mulungu, kuti Simoni ndi ana ake akhale nawo.

Antioko wachisanu ndi chiŵiri
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help