1Abramu ali wa zaka 99, Chauta adamuwonekera namuuza kuti, “Ine ndine Mulungu Mphambe. Tsono uzindimvera nthaŵi zonse, ndipo uzichita zolungama.
2Ndidzachita nawe chipangano, ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri.”
3Pomwepo Abramu adagwada pansi ndipo Mulungu adati,
4“Nachi chipangano chimene ndidzachite nawe. Ndikulonjeza kuti udzakhala kholo la anthu a mitundu yambiri.
5 Limeneli ndilo dzina lako, chifukwa ndikukusandutsa kholo la anthu a mitundu yambiri.
6Ndidzakupatsa zidzukulu zambiri, ndipo zina mwa izo zidzakhala mafumu. Udzakhala ndi zidzukulu zambiri kotero kuti zidzakhala mitundu yaikulu.
7 Ndidzasunga chipangano changa ndi iyeyo ndiponso ndi zidzukulu zake, ndipo chipanganocho chidzakhala chamuyaya.
20Koma kunena za Ismaeleyu, ndidzamdalitsa, ndipo ndidzampatsa ana ambiri pamodzi ndi zidzukulu. Adzakhala bambo wa mafumu khumi ndi aŵiri, ndipo zidzukulu zake ndidzakhala mtundu waukulu.
21Koma ndidzasunga chipangano changa ndi mwana wako Isaki amene adzabadwa mwa Sara pa nyengo yonga yomwe ino chaka chamaŵachi.”
22Mulungu atatha kulankhula ndi Abrahamu, adamsiya pomwepo.
23Tsiku lomwelo Abrahamu adakumbukira zimene Mulungu adamuuza, ndipo adatenga mwana wake Ismaele ndi akapolo onse obadwira m'nyumba mwake, kapena amene Abrahamu adaŵagula, kungoti amuna onse a m'nyumba mwake, naŵaumbala monga momwe Mulungu adaamuuzira.
24Abrahamu anali wa zaka 99 pa nthaŵi imene adaumbalidwa.
25Mwana wake Ismaele anali wa zaka 13 pamene adaumbalidwa.
26Pa tsiku limeneli Abrahamu ndi mwana wake Ismaele adaumbalidwa,
27pamodzi ndi anthu aamuna onse, amuna obadwira m'banja mwake ndiponso ena amene adaŵagula ndi ndalama kwa alendo, onsewo adaumbalidwa pamodzi ndi iyeyo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.