2 Sam. 24 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kaundula wa anthu.(1 Mbi. 21.1-27)

1Nthaŵi ina Chauta adaŵakwiyiranso Aisraele, choncho adautsa mtima wa Davide kuti aŵavutitse. Adamuuza kuti, “Pita ukaŵerenge Aisraele ndi Ayuda.”

2Choncho mfumu Davide adauza Yowabu ndi atsogoleri ankhondo amene anali naye pamodzi kuti, “Pitani pakati pa mafuko onse a Aisraele kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, mukaŵerenge anthu kuti ndidziŵe chiŵerengero chao.”

3Koma Yowabu adauza mfumu kuti, “Chauta Mulungu wanu achulukitse anthu makumi khumi kupambana m'mene alirimu, ndipo alole kuti inu mbuyanga mfumu mudzaziwone zimenezo. Koma chifukwa chiyani inu mbuyanga mfumu mukufuna chinthu chotere?”

4Komabe mau a mfumu adapambana mau a Yowabu ndi a atsogoleri ankhondo aja. Choncho Yowabu ndi atsogoleri ankhondowo adachokapo kuti akaŵerenge Aisraele.

5Adaoloka mtsinje wa Yordani, nayambira ku Aroere, mzinda umene uli pakati pa chigwa cha ku Gadi, mpaka ku Yazere.

6Tsono adafika ku Giliyadi ndi ku Kadesi m'dziko la Ahiti, nakafika ku Dani, kuchokera kumeneko adayenda mozungulira ku Sidoni.

7Ndipo adakafika ku linga la Tiro ndi ku mizinda yonse ya Ahivi, ndi ya Akanani. Atatero, adachoka kumeneko nakafika kumwera kwa Yuda, ku Beereseba.

8Motero, atabzola dziko lonselo, adadzafika ku Yerusalemu itatha miyezi isanu ndi inai ndi masiku makumi aŵiri.

9Tsono Yowabu adapereka chiŵerengero cha anthu onse kwa mfumu. Ku dziko la Israele kunali anthu 800,000 otha kumenya nkhondo, ndipo ku Yuda kunali 500,000 pamodzi.

10Pambuyo pake Davide adadzitsutsa mumtima mwake, atatha kaundulayo. Ndipo adapemphera kwa Chauta kuti, “Ndachimwa kwambiri pochita zimenezi. Koma tsopano, Inu Chauta, ndikukupemphani kuti mundikhululukire tchimo langa ine mtumiki wanu, popeza kuti ndachita zopusa kwambiri.”

11Tsono Davide atadzuka m'maŵa, Chauta adalankhula ndi Gadi, mneneri wa Davide, namuuza kuti,

12“Pita ukamuuze Davide kuti, ‘Ine Chauta ndikunena kuti, “Ndikuika pamaso pako zinthu zitatu zoti ndikuchite. Tsono usankhepo chimodzi, ndipo ndidzakuchita.” ’ ”

13Choncho Gadi adadza kwa Davide, namuuza kuti, “Musankhe, kodi pabwere zaka zitatu zanjala m'dziko mwanu, kapena inu mukhale mukuthaŵa adani anu pa miyezi itatu, kapena pakhale mliri wa masiku atatu m'dziko mwanu? Ganizani bwino, ndipo mutsimikize chilichonse choti muyankhe, kuti ine ndikauze amene adanditumayo.”

14Apo Davide adauza Gadi kuti, “Iyai, ine pamenepa ndavutika kwambiri mu mtima. Makamaka tigwe m'manja mwa Chauta, popeza kuti chifundo chake nchachikulu. Koma chonde, tisagwe m'manja mwa anthu ai.”

15Choncho Chauta adagwetsa mliri pa Aisraele, kuyambira m'maŵa mpaka pa nthaŵi imene adaafuna mwini wake, mwakuti kuchokera ku Dani mpaka ku Beereseba adafa anthu okwanira 70,000 pamodzi.

16Ndipo pamene mngelo adatambalitsa dzanja lake kuloza mzinda wa Yerusalemu kuti auwononge, Chauta adasintha maganizo achilangowo, nauza mngelo wake amene ankaononga anthu uja kuti, “Iyai, basi tsopano! Kwakwanira. Bweza dzanja lakolo.” Nthaŵi imeneyo nkuti mngelo wa Chautayo ataima pa malo opunthira tirigu a Arauna Myebusi.

17Davide adaona mngelo uja, ndipo adalankhula ndi Chauta, nati, “Ndachimwa ndine, ndipo ndachita choipa. Koma nkhosa izi kodi zachita chiyani? Amangonditsatira chabe. Tsono dzanja lanu likanthe ine ndi banja la bambo wanga.”

18Tsiku limenelo Gadi adafika kwa Davide namuuza kuti, “Mupite mukamangire Chauta guwa pa malo opunthira tirigu a Arauna Myebusi uja.”

19Atamva mau a Gadiwo, Davide adapita monga momwe Chauta adaalamulira.

20Ndipo Arauna atapenya chakunsi, adaona mfumu ikudza kwa iye pamodzi ndi atumiki ake. Pomwepo Araunayo adapita kukalambira mfumu choŵerama pansi.

21Tsono adafunsa mfumu kuti, “Bwanji mbuyanga mfumu, mukudza kwa ine mtumiki wanu?” Davide adati, “Ndikufuna kuti ndigule malo opunthira tirigu aja, kuti ndimangirepo Chauta guwa, kuti mliriwu uŵachoke anthu.”

22Arauna adauza Davide kuti, “Mbuyanga mfumu, mutenge mukapereke nsembe zinthu zimene zikukomereni. Nazi ng'ombe zokaperekera nsembe yopsereza. Nazinso zipangizo zomangira ng'ombe pamodzi ndi magoli omwe a ng'ombezo, kuti zikhale nkhuni.”

23Zonsezi Arauna adazipereka kwa mfumu, ndipo adapitiriza nati, “Chauta Mulungu wanu, alandire nsembe zanuzo.”

24Koma mfumu idauza Arauna kuti, “Iyai, koma ndichita chogula ndithu kwa iwe pa mtengo wake. Sindingapereke ngati nsembe zopsereza kwa Chauta Mulungu wanga zinthu zosagula.” Choncho Davide adagula malo opunthirapo tirigu aja pamodzi ndi ng'ombe zomwe pa mtengo wa masekeli asiliva makumi asanu.

25Ndipo kumeneko adamangako guwa, kumangira Chauta, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Choncho Chauta adamva kupemba kwake kopembera dziko, ndipo mliriwo udaleka m'dziko la Israele.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help